Malembo Oyera
3 Nefi 23


Mutu 23

Yesu avomereza mawu a Yesaya—Alamulira anthu kuti afufuze aneneri—Mawu a Samueli Mlamani okhudza Chiukitso awonjezedwa ku zolemba zawo. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano, taonani, ndinena kwa inu, kuti mukuyenera kufufuza zinthu izi. Inde, lamulo ine ndikupereka kwa inu kuti mufufuze zinthu izi mwakhama; pakuti mawu a Yesaya ndi aakulu.

2 Pakuti ndithudi iye adayankhula zokhudza zinthu zonse zokhudzana anthu anga amene ali a nyumba ya Israeli; kotero zikuyenera kukhala kuti iye ayankhulenso kwa Amitundu.

3 Ndipo zinthu zonse zimene iye adayankhula zakhala ndipo zidzakhala, ngakhale molingana ndi mawu amene iye adayankhula.

4 Kotero mvetserani mawu anga; lembani zinthu zimene ine ndakuwuzani; ndipo molingana ndi nthawi ndi chifuniro cha Atate izo zidzapita kwa Amitundu.

5 Ndipo aliyense amene adzamvetsera mawu anga ndi kulapa ndi kubatizidwa, yemweyo adzapulumutsidwa. Fufuzani mwa aneneri, pakuti alipo ambiri amene akuchitira umboni za zinthu izi.

6 Ndipo tsopano zidachitika pamene Yesu adanena mawu awa adanenanso kwa iwo kachiwiri, atafotokoza malemba oyera onse kwa iwo amene adalandira, adati kwa iwo: Taonani, malemba oyera ena ndikufuna kuti muwalembe, amene mulibe.

7 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa Nefi: Bweretsani zolemba zimene mudasunga.

8 Ndipo pamene Nefi adabweretsa zolembedwazo, ndipo adaziyika izo pamaso pake, iye adaponya maso ake pa izo ndipo adati:

9 Indetu ndinena kwa inu, ndidalamulira kapolo wanga Samueli, Mlamani, kuti achitire umboni kwa anthu awa, kuti pa tsiku limene Atate adzalemekeza dzina lawo mwa ine kuti padali oyera mtima ambiri amene akuyenera kuwuka kwa akufa, ndipo adzawonekera kwa ambiri, ndipo akuyenera kutumikira kwa iwo. Ndipo iye adati kwa iwo, Sizinali choncho kodi?

10 Ndipo ophunzira ake adamuyankha iye nati: Inde, Ambuye, Samueli adanenera monga mwa mawu anu, ndipo onse adakwaniritsidwa.

11 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Nanga bwanji inu simudalemba chinthu chimenechi, kuti oyera mtima ambiri adauka ndikuonekera kwa ambiri ndi kutumikira kwa iwo?

12 Ndipo zidachitika kuti Nefi adakumbukira kuti chinthu ichi sichidalembedwe.

13 Ndipo zidachitika kuti Yesu adalamulira kuti chilembedwe; kotero chidalembedwa monga momwe adalamulira.

14 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adalongosola malembo oyera onse pamodzi, amene iwo adawalemba, adawalamura iwo kuti akuyenera kumaphunzitsa zinthu zimene iye adafotokoza kwa iwo.