Malembo Oyera
3 Nefi 27


Mutu 27

Yesu alamula kuti Mpingo utchedwe mu dzina Lake—Utumiki Wake ndi nsembe yochotsera machimo zimapanga uthenga wabwino Wake—Anthu akulamulidwa kuti alape ndi kubatizidwa kuti akathe kuyeretsedwa ndi Mzimu Woyera—Iwo ayenera kukhala monga momwe Yesu alili. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34–35.

1 Ndipo zidachitika kuti pamene ophunzira a Yesu adali pa ulendo ndipo adali akulalikira zinthu zimene adazimva ndi kuziona, ndipo adali kubatiza m’dzina la Yesu, zidachitika kuti ophunzirawo adasonkhana pamodzi ndipo adalumikizana mu pemphero lamphamvu ndi kusala kudya.

2 Ndipo Yesu adadzionetseranso yekha kwa iwo, pakuti adali kupemphera kwa Atate m’dzina lake; ndipo Yesu adadza ndi kuyimilira pakati pawo, ndikunena kwa iwo, Mukufuna kuti ndikupatseni inu chiyani?

3 Ndipo iwo adati kwa iye: Ambuye, ife tikufuna kuti inu mutiuze ife dzina limene ife tidzautchula mpingo uwu; pakuti pali mikangano pakati pa anthu pa nkhani imeneyi.

4 Ndipo Ambuye adati kwa iwo: Indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, n’chifukwa chiyani zili kuti anthu azing’ung’uza ndi kukangana chifukwa cha chinthu ichi?

5 Kodi iwo sadawerenge malemba oyera, amene amati inu mukuyenera kutenga pa inu dzina la Khristu, limene liri dzina langa? Pakuti mu dzina ili mudzatchedwa pa tsiku lotsiriza;

6 Ndipo amene adzatenga pa iye dzina langa, ndi kupilira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa pa tsiku lotsiriza.

7 Kotero, chilichonse mudzachita, mudzachichita m’dzina langa; kotero inu mudzatchula Mpingowo mu dzina langa; ndipo mudzaitanira pa Atate m’dzina langa, kuti adzadalitse mpingowo chifukwa cha ine.

8 Ndipo ungakhale bwanji mpingo wanga kupatula utatchulidwa m’dzina langa? Pakuti ngati mpingo ukutchedwa mu dzina la Mose ndiye ndi mpingo wa Mose; kapena ngati udzatchedwa mu dzina la munthu ndiye udzakhala mpingo wa munthu; koma ngati iwo utchedwa m’dzina langa ndiye uli mpingo wanga, ngati uwo wamangidwa pa uthenga wanga wabwino.

9 Indetu ndinena kwa inu, kuti inu mwamangidwa pa uthenga wanga wabwino; kotero mudzatchula zinthu zilizonse zomwe mudzatchula, m’dzina langa; kotero ngati inu muitanira pa Atate, pa za mpingo; ngati zitakhale m’dzina langa Atate adzamva inu;

10 Ndipo ngati zitakhale kuti mpingo wamangidwa pa uthenga wanga wabwino pamenepo Atate adzaonetsa ntchito zawo zomwe m’menemo.

11 Koma ngati sumangidwira pa uthenga wabwino wanga, ndipo wamangidwa pa ntchito za anthu, kapena pa ntchito za mdyerekezi, indetu ndinena kwa inu ali ndi chisangalalo mu ntchito zawo kwa kanthawi, ndipo posachedwa mapeto akubwera, ndipo adzadulidwa, ndikuponyedwa kumoto, kumene palibe kubwelera.

12 Pakuti ntchito zawo zimawatsata; pakuti chifukwa cha ntchito zawo iwo agwetsedwa; kotero kumbukirani zimene ndakuuzani inu.

13 Taonani ndapereka kwa inu uthenga wanga wabwino, ndipo uwu ndi uthenga wabwino umene ndapereka kwa inu—kuti ndidadza m’dziko kudzachita chifuniro cha Atate anga, chifukwa Atate anga adandituma ine.

14 Ndipo Atate adandituma ine kuti ine ndikathe kukwezedwa pa mtanda; ndipo nditakwezedwa pa mtanda, kuti ndikakokere anthu onse kwa ine, kuti monga ndakwezedwa ndi anthu kotero kuti anthu akwezedwe mmwamba ndi Atate, kuimilira pamaso panga, kuti aweruzidwe ku ntchito zawo, kaya zili zabwino kapena zoipa—

15 Ndipo pa chifukwa cha ichi ndakwezedwa; kotero, monga mwa mphamvu ya Atate ndidzakokera anthu onse kwa Ine, kuti akathe kuweruzidwa molingana ndi ntchito zawo.

16 Ndipo zidzachitika, kuti amene walapa ndi kubatizidwa m’dzina langa adzadzazidwa; ndipo ngati apilira kufikira kuchimaliziro, taonani, ndidzamuyesa wopanda mlandu pamaso pa Atate anga pa tsiku lomwe ndidzayimilira kuweruza dziko lapansi.

17 Ndipo iye amene sapilira kufikira chimaliziro, yemweyo ndiye amene amadulidwa ndi kuponyedwa m’moto, kumene sadzabweleranso, chifukwa cha chilungamo cha Atate.

18 Ndipo awa ndi mawu amene adapereka kwa ana a anthu. Ndipo chifukwa cha ichi akwaniritsa mawu amene apereka, ndipo samanama, koma amakwaniritsa mawu awo onse.

19 Ndipo palibe chinthu chodetsedwa chingalowe mu ufumu wake; kotero palibe kanthu kolowa mu mpumulo wake kupatula iwo amene atsuka zovala zawo m’mwazi wanga; chifukwa cha chikhulupiliro chawo, ndi kulapa kwa machimo awo onse, ndi kukhulupirika kwawo mpaka kumapeto.

20 Tsopano ili ndi lamulo: Lapani, inu malekezero a dziko lapansi, ndipo idzani kwa ine ndi kubatizidwa m’dzina langa, kuti muthe kuyeretsedwa ndi kulandira kwa Mzimu Woyera, kuti muthe kuyima opanda banga pamaso panga pa tsiku lotsiriza.

21 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, uwu ndi uthenga wanga wabwino; ndipo mukudziwa zinthu zimene mukuyenera kuchita mu mpingo wanga; pakuti ntchito zimene mwandiona ine ndikuzichita zimenezo inu mudzazichitanso; pakuti chimene mwandiona ine ndikuchita ngakhale ichonso mudzachichita;

22 Kotero ngati muchita zinthu izi ndinu odala, pakuti mudzakwezedwa m’tsiku lotsiriza.

23 Lemba zimene waziona ndi kuzimva, kupatula izo zimene zili zoletsedwa.

24 Lemba ntchito za anthu awa, zomwe zidzakhala, ngakhale monga kwalembedwa, za zomwe zidalipo.

25 Pakuti, taonani, kuchokera m’mabuku amene adalembedwa, ndi amene adzalembedwa, anthu awa adzaweruzidwa, pakuti mwa iwo ntchito zawo zidzadziwika kwa anthu.

26 Ndipo taonani, zinthu zonse zalembedwa ndi Atate; kotero kuchokera m’mabuku amene adzalembedwa dziko lapansi lidzaweruzidwa.

27 Ndipo dziwani inu kuti mudzakhala oweruza a anthu awa, molingana ndi chiweruzo chimene Ine ndidzapereka kwa inu, chimene chidzakhala cholungama. Kotero, kodi mukuyenera kukhala anthu otani? Indetu ndinena kwa inu, ngakhale monga ine ndilili.

28 Ndipo tsopano ndipita kwa Atate. Ndipo indetu, ndinena kwa inu, zinthu zilizonse mukapempha Atate m’dzina langa zidzapatsidwa kwa inu.

29 Kotero pemphani, ndipo mudzalandira; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti iye wopempha, amalandira; ndi kwa iye amene agogoda, chidzatsekulidwa.

30 Ndipo tsopano, taonani, chisangalalo changa chili chachikulu, ngakhale ku chidzalo, chifukwa cha inu, ndiponso m’badwo uwu; inde, ndipo ngakhale Atate akondwera, ndiponso angelo onse oyera, chifukwa cha inu ndi m’badwo uno; pakuti palibe m’modzi wa iwo wotayika.

31 Taonani, ndikufuna kuti mumvetsetse; pakuti ndikutanthauza iwo amene ali ndi moyo tsopano a m’badwo uwu; ndipo palibe m’modzi wa iwo wotayika; ndipo mwa iwo ndili nacho chidzalo cha chisangalalo.

32 Koma onani, zikundimvetsa chisoni chifukwa cha m’badwo wachinayi kuchokera mu m’badwo uwu, pakuti iwo atsogozedwa ku ukapolo ndi iye ngakhale monga adali mwana wa chitayiko; pakuti adzandigulitsa ndi siliva ndi golide, ndi chimene njenjete imawononga, ndi chimene mbala zimaboola ndi kuba. Ndipo tsiku limenelo ndidzawayendera, ngakhale kutembenuzira ntchito zawo pa mitu yawo.

33 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adatha mawu amenewa, adati kwa ophunzira ake: Lowani pa chipata chopapatiza; pakuti chipata chili chopapatiza, ndipo ndiyopapatiza njira yotsogolera kumoyo, ndipo ali owerengeka akuipeza iyo; koma chotakasuka chili chipata, ndipo yotakata njira yotsogolera ku imfa, ndipo ali ambiri akuyenda m’menemo, kufikira ukadza usiku, mumene palibe munthu angagwiremo ntchito.