Malembo Oyera
3 Nefi 28


Mutu 28

Asanu ndi anayi a ophunzira khumi ndi awiri akhumba ndipo alonjezedwa cholowa mu ufumu wa Khristu pamene iwo amwalira—Anefi Atatu akhumba ndipo apatsidwa mphamvu pa imfa kotero kuti akhala pa dziko lapansi mpaka Yesu abwere kachiwiri—Iwo atembenuzidwa ndi kuona zinthu zosaloledwa kunenedwa, ndipo tsopano akutumikira pakati pa anthu. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34–35

1 Ndipo zidachitika pamene Yesu adanena mawu awa, adayankhula ndi ophunzira ake, m’modzim’modzi, nanena kwa iwo: Mukufuna chiyani kwa ine, ndikapita ine kwa Atate?

2 Ndipo onse adayankhula, kupatulapo atatu, nati: Tikufuna kuti titakhala ndi moyo kufikira dzaka za anthu, kuti utumiki wathu, umene mudatiyitana ife ukhale ndi mathero, kuti ife tibwere kwa inu mwachangu mu ufumu wanu.

3 Ndipo adati kwa iwo: Odala muli inu chifukwa mwakhumba chinthu ichi kwa ine; kotero, pambuyo pake muli dzaka makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri mudzabwera kwa ine mu ufumu wanga; ndipo ndi ine mudzapeza mpumulo.

4 Ndipo pamene adayankhula kwa iwo, adatembenukira kwa atatuwo, nati kwa iwo: Mukufuna kuti ndidzakuchitireni chiyani, pamene ndipita kwa Atate?

5 Ndipo adamva chisoni m’mitima mwawo, pakuti sadayerekeze kunena kwa iye chimene adachifuna.

6 Ndipo adati kwa iwo: Taonani, ndikudziwa maganizo anu, ndipo mwakhumba chinthu chimene Yohane, wokondedwa wanga, amene adali ndi ine mu utumiki wanga, ndisadapachikidwe ndi Ayuda, adafuna kwa ine.

7 Kotero, odala kwambiri ndinu, pakuti simudzalawa konse imfa; koma mudzakhala ndi moyo kuona machitachita onse a Atate kwa ana a anthu, ngakhale kufikira zinthu zonse zidzakwaniritsidwa monga mwa chifuniro cha Atate, pamene ndidzadza mu ulemerero wanga ndi mphamvu zakumwamba.

8 Ndipo simudzapilira zowawa za imfa ku nthawi zonse; koma pamene ndidzabwera mu ulemelero wanga inu mudzasandulika mu kuthwanima kwa diso kuchoka ku chivundi kupita ku moyo wosafa; ndipo pamenepo mudzakhala odalitsika mu ufumu wa Atate anga.

9 Ndipo kachiwiri, inu simudzakhala ndi zowawa pamene inu mudzakhala mu thupi, kapena chisoni kupatula icho chili chifukwa cha machimo a dziko lapansi; ndipo zonsezi ndidzachita chifukwa cha chinthu chimene inu mwakhumba kwa ine, pakuti inu mwafuna kuti mubweretse miyoyo ya anthu kwa ine, pamene dziko lidzayima.

10 Ndipo chifukwa cha ichi mudzakhala nacho chidzalo cha chisangalalo; ndipo mudzakhala pansi mu ufumu wa Atate anga; inde, chisangalalo chanu chidzadzadza, ngakhale monga Atate adandipatsa ine chidzalo cha chisangalalo; ndipo mudzakhala monga ine ndiri, ndipo ine ndili ngakhale monga Atate; ndipo Atate ndi ine tili amodzi;

11 Ndipo Mzimu Woyera ukuchitira umboni wa Atate ndi ine; ndipo Atate amapereka Mzimu Woyera kwa ana a anthu, chifukwa cha ine.

12 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa, adakhudza aliyense wa iwo ndi chala chake, kupatula atatu amene adatsalawo, ndipo kenako iye adachoka.

13 Ndipo taonani, kumwamba kudatseguka, ndipo iwo adakwatulidwa kumwamba, ndipo adaona ndi kumva zinthu zosaneneka.

14 Ndipo kudaletsedwa kwa iwo kuti asanene; ngakhale sikudapatsidwe kwa iwo mphamvu kuti iwo akathe kunena zinthu zimene adaziona ndi kuzimva;

15 Ndipo ngati adali m’thupi kapena kunja kwa thupi, sadathe kudziwa; pakuti zidaoneka kwa iwo ngati kusandulika kwa iwo, kuti adasinthika kuchokera ku thupi ili la mnofu kulowa m’mkhalidwe wosafa, kuti akathe kuona zinthu za Mulungu.

16 Koma zidachitika kuti iwo adatumikira kachiwiri pa nkhope ya dziko lapansi; komabe iwo sadatumikire za zinthu zomwe adazimva ndi kuziona, chifukwa cha lamulo lomwe lidapatsidwa kwa iwo kumwamba.

17 Ndipo tsopano, ngati iwo adali achivundi kapena wosafa, kuyambira tsiku la kusandulika kwawo, ine sindikudziwa;

18 Koma zambiri izi ine ndikudziwa, malingana ndi zolemba zomwe zidaperekedwa—iwo adapita patsogolo pa nkhope ya dziko, ndipo adatumikira ku anthu onse, kugwirizanitsa ochuluka kwa mpingo amene akadakhulupilira mu kulalikira kwawo; ndi kuwabatiza iwo, ndipo onse amene adabatizidwa adalandira Mzimu Woyera.

19 Ndipo adaponyedwa m’ndende ndi iwo amene sadali a mpingo. Ndipo ndende sizidathe kuwasunga, pakuti zidang’ambika pawiri.

20 Ndipo adaponyedwa pansi; koma iwo adakantha pansipo ndi mawu a Mulungu, kotero kuti ndi mphamvu yake adamasulidwa kuchokera mu kuya kwa nthaka; ndipo motero iwo sakadatha kukumba mayenje okwanira kuwasunga iwo.

21 Ndipo katatu adaponyedwa m’ng’anjo ndipo sadavulale.

22 Ndipo adaponyedwa kawiri m’dzenje la zilombo; ndipo taonani iwo adasewera ndi zilombozo monga mwana ndi mwana wa nkhosa woyamwa, ndipo sadavulale.

23 Ndipo zidachitika kuti motero iwo adapita patsogolo pakati pa anthu onse a Nefi, ndipo adalalikira uthenga wabwino wa Khristu kwa anthu onse pa nkhope ya dziko; ndipo adatembenukira kwa Ambuye, ndipo adalumikizidwa kwa mpingo wa Khristu, ndipo motero anthu a m’badwo umenewo adadalitsidwa, monga mwa mawu a Yesu.

24 Ndipo tsopano ine, Mormoni, ndikumaliza kuyankhula zokhudzana ndi zinthu izi kwa kanthawi.

25 Taonani, ndimati ndilembe maina a iwo amene sadzalawa imfa, koma Ambuye adaletsa; kotero sindilemba izo, pakuti iwo abisidwa ku dziko.

26 Koma taonani, ndawaona, ndipo iwo atumikira kwa ine.

27 Ndipo taonani iwo adzakhala pakati pa Amitundu, ndipo Amitundu sadzawadziwa iwo.

28 Iwonso adzakhala pakati pa Ayuda, ndipo Ayuda sadzawadziwa.

29 Ndipo zidzachitika, pamene Ambuye aona kuti nkoyenera mu nzeru zake, kuti adzatumikire mafuko onse obalalika a Israeli, ndi maiko onse, ndi mafuko, ndi malilime, ndi anthu, ndipo adzatulutsa kuchoka kwa iwo kupita kwa Yesu miyoyo yambiri; kuti chikhumbo chawo chikwaniritsidwe, ndiponso chifukwa cha mphamvu yotsimikizira ya Mulungu yomwe ili mwa iwo.

30 Ndipo iwo ali ngati angelo a Mulungu, ndipo ngati iwo angapemphere kwa Atate m’dzina la Yesu iwo akhonza kudziwonetsa iwo eni kwa munthu aliyense amene angafune.

31 Kotero, ntchito zazikulu ndi zodabwitsa zidzachitidwa ndi iwo, lisadafike tsiku lalikulu ndi lakubwera pamene anthu onse akuyenera ndithu kuyima patsogolo pa mpando wa chiweruzo wa Khristu;

32 Inde ngakhale pakati pa Amitundu padzakhala ntchito yaikulu ndi yodabwitsa yochitidwa ndi iwo, lisadadze tsiku la chiweruzo.

33 Ndipo ngati inu mudali ndi malemba onse amene amapereka nkhani za ntchito zodabwitsa zonse za Khristu, mungafune, monga mwa mawu a Khristu, kudziwa kuti zinthu izi zikuyenera kubwera.

34 Ndipo tsoka likhale kwa iye amene sadzamvetsera mawu a Yesu, ndi kwa iwo amene adawasankha ndi kuwatumiza pakati pawo; pakuti amene salandira mawu a Yesu ndi mawu a iwo amene iye adawatuma samulandira iye; ndipo motero iye sadzawalandira iwo pa tsiku lotsiriza;

35 Ndipo zikadakhala bwino kwa iwo akadapanda kubadwa. Pakuti kodi mukuganiza kuti mutha kuchotsa chilungamo cha Mulungu wokhumudwitsidwa, amene waponderezedwa pansi pa mapazi a anthu, kuti mwa kutero chipulumutso chikabwere?

36 Ndipo tsopano taonani, monga ndidayankhula zokhudzana ndi iwo amene Ambuye adawasankha, inde, ngakhale atatu amene adakwatulidwa m’mwamba, kuti sindidadziwe ngati adayeretsedwa kuchoka ku moyo wa chivundi kupita ku moyo wosafa.

37 Koma onani, popeza ndidalemba, ndidafunsa kwa Ambuye, ndipo adandiwonetsera kuti pakuyenera kukhala kusintha kochitika pa matupi awo, kapena zikuyenera kukhala kuti iwo akuyenera kulawa imfa;

38 Kotero, kuti iwo asalawe imfa padali kusintha kudachitidwa pa matupi awo, kuti iwo asamve kuwawa kapena chisoni kupatula chifukwa cha machimo a dziko lapansi.

39 Tsopano kusinthaku sikudali kofanana ndi zomwe zidzachitike pa tsiku lotsiriza; koma padali kusintha kudachitika pa iwo, kotero kuti Satana sakadatha kukhala ndi mphamvu pa iwo, kuti iye sakadatha kuwayesa iwo; ndipo adayeretsedwa m’thupi, kuti adali oyera, ndi kuti mphamvu za dziko sizikadatha kuwagwira.

40 Ndipo mu chikhalidwe ichi iwo adayenera kukhala mpaka tsiku la chiweruzo cha Khristu; ndipo pa tsiku limenelo iwo adali woyenera kulandira kusintha kwakukulu, ndi kulandiridwa mu ufumu wa Atate kuti asapitenso kunja, koma kukakhala ndi Mulungu kwamuyaya m’mwamba.