Mutu 29
Kubwera kwa Buku la Mormoni ndi chizindikiro chakuti Ambuye wayamba kusonkhanitsa Israeli ndi kukwaniritsa mapangano Ake—Awo amene amakana mavumbulutso ndi mphatso Zake za masiku otsiriza adzatembeleredwa. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34–35.
1 Ndipo tsopano taonani, ine ndinena kwa inu kuti pamene Ambuye adzaona kuti nkoyenera, mu nzeru zake, kuti mawu awa adzafike kwa Amitundu monga mwa mawu ake, pamenepo inu mudzadziwa kuti pangano limene Atate adapanga ndi ana a Israeli, zokhudzana ndi kubwenzeretsedwa kwawo ku maiko a cholowa chawo, kwayamba kale kukwaniritsidwa.
2 Ndipo mutha kudziwa kuti mawu a Ambuye, amene adayankhulidwa ndi aneneri oyera, onse adzakwaniritsidwa; ndipo simukuyenera kunena kuti Ambuye akuchedwa kubwera kwa ana a Israeli.
3 Ndipo simukuyenera kuganiza m’mitima yanu kuti mawu amene adayankhulidwa ali opanda pake, pakuti taonani, Ambuye adzakumbukira pangano lake limene adapanga kwa anthu ake a nyumba ya Israeli.
4 Ndipo pamene mudzaona mawu awa akutuluka pakati pa inu, pamenepo simukufunikira kunyozanso zochita za Ambuye; pakuti lupanga la chilungamo chake liri m’dzanja lake lamanja; ndipo taonani, pa tsiku limenelo, ngati inu mudzanyoza zochita zake iye adzachititsa kuti izo zidzakupezeni posachedwa.
5 Tsoka kwa iye amene amanyoza zochita za Ambuye; inde, tsoka kwa iye amene adzakana Khristu ndi ntchito zake!
6 Inde, tsoka kwa iye amene adzakana mavumbulutso a Ambuye, ndi amene adzati Ambuye sagwiranso ntchito ndi vumbulutso, kapena ndi uneneri, kapena ndi mphatso, kapena ndi malilime, kapena ndi machiritso, kapena ndi mphamvu ya Mzimu Woyera!
7 Inde, ndipo tsoka kwa iye amene adzanena pa tsiku limenelo, kuti apeze phindu, kuti sipadzakhala chozizwitsa chochitidwa ndi Yesu Khristu; pakuti iye amene amachita ichi adzakhala ngati mwana wa chitayiko, kwa amene sadachitiridwe chifundo, molingana ndi mawu a Khristu!
8 Inde, ndipo simudzasowanso m’nyozo, kapena kunyoza, kapena kuchita masewera pa Ayuda, kapena otsala ena aliwonse a nyumba ya Israeli; pakuti taonani, Ambuye amakumbukira pangano lake kwa iwo, ndipo adzawachitira molingana ndi umo momwe adalumbilira.
9 Kotero simukuyenera kuganiza kuti mungatembenuzire dzanja lamanja la Ambuye ku lamanzere, kuti iye asathe kuchita chiweruzo m’kukwaniritsidwa kwa pangano limene iye adapanga kwa nyumba ya Israeli.