Malembo Oyera
3 Nefi 14


Mutu 14

Yesu alamula kuti: Musaweruze; pemphani kwa Mulungu; chenjerani ndi aneneri onyenga—Iye alonjeza chipulumutso kwa iwo amene amachita chifuniro cha Atate—Fananitsani ndi Mateyu 7. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa adatembenukiranso kwa khamulo, ndikutsegulanso pakamwa pake kwa iwo, nanena: Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, Musaweruze, kuti nanu musaweruzidwe.

2 Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, udzayesedwa kwa inunso.

3 Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma osaganizira chipika chili m’diso la iwe mwini?

4 Kapena unganene bwanji kwa m’bale wako: Ndilore ndichotse kachitsotso m’diso lako—ndipo taona, chipika chili m’diso lako?

5 Wonyenga iwe, tayamba wachotsa chipikacho m’diso lako; ndipo pamenepo udzapenyetsetsa nkutulutsa kachitsotso m’diso la m’bale wako.

6 Musapatse choyeracho kwa agalu, kapena musamaponye ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi awo, ndi kutembenukanso ndikung’amba inu.

7 Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.

8 Pakuti aliyense wakupempha, adzalandira; ndi wofunayo, adzapeza; ndipo kwa iye wogogoda, chidzatsegulidwa.

9 Kapena munthu ndani wa inu, amene mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala?

10 Kapena akadzampempha nsomba, adzampatsa njoka kodi?

11 Ndiye ngati inu, okhala oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nkoposa kotani nanga Atate anu a Kumwamba adzapereka zinthu zabwino kwa iwo akuwapempha Iwo?

12 Kotero, zinthu zili zonse mumafuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti ichi ndicho chilamulo ndi aneneri.

13 Lowani pa chipata chopapatiza; pakuti chipata chili chachikulu, ndipo njira ndiyotakata, imene imatsogolera ku chiwonongeko, ndipo ali ambiri amene amalowa m’menemo;

14 Chifukwa chipata chili chopapatiza, ndipo yaying’ono ndi njirayo imene imatsogolera ku moyo, ndipo ali owerengeka amene akuipeza iyo.

15 Chenjerani ndi aneneri onyenga, amene amadza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwawo ali mimbulu yolusa.

16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa paminga, kapena nkuyu pa mthula?

17 Momwemo mtengo wabwino uli wonse umapereka chipatso chabwino; koma mtengo wovunda umapereka chipatso choipa.

18 Mtengo wabwino sungathe kubala chipatso choipa, kapena mtengo wovunda kubala chipatso chabwino.

19 Mtengo uli wonse wosabereka zipatso zabwino, umadulidwa, ndi kuponyedwa pamoto.

20 Kotero, ndi zipatso zawo mudzawadziwa iwo.

21 Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma iye amene achita chifuniro cha Atate anga a Kumwamba.

22 Ambiri adzati kwa ine tsiku limenelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitidanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi m’dzina lanunso kuchita zodabwitsa zambiri?

23 Ndipo pamenepo ndidzanena kwa iwo, Sindidakudziweni konse; chokani kwa ine, inu akuchita mphulupulu.

24 Kotero, yense wakumva mawu angawa, ndi kuwachita, ndidzamufanizira iye ndi munthu wanzeru, amene adamanga nyumba yake pa thanthwe;

25 Ndipo idagwa mvula, ndipo kusefukira kwa madzi kudabwera, ndipo mphepo zidawomba, ndipo zidamenya pa nyumbayo; ndipo siidagwe, pakuti idamangidwa pa thanthwe.

26 Ndipo yense wakumva mawu angawa ndi kusawachita adzafanizidwa ndi munthu wopusa, amene adamanga nyumba yake pamchenga—

27 Ndipo mvula idagwa, ndipo kusefukira kwa madzi kudabwera, ndipo mphepo zidaomba, ndipo zidamenya pa nyumbayo; ndipo idagwa, ndipo kugwa kwake kudali kwakukulu.