Malembo Oyera
3 Nefi 9


Mutu 9

Mu mdima, mawu a Khristu alengeza chiwonongeko cha anthu ambiri ndi mizinda chifukwa cha kuipa kwawo—Iye alengezanso umulungu Wake, alengeza kuti chilamulo cha Mose chakwaniritsidwa, ndipo aitana anthu kuti adze kwa Iye ndi kupulumutsidwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo zidachitika kuti padali liwu lidamveka pakati pa onse okhala padziko lapansi, pa nkhope yonse ya dziko ili, kufuula;

2 Tsoka, tsoka, tsoka kwa anthu awa; tsoka kwa okhala padziko lonse lapansi pokhapokha iwo adzalape; pakuti mdyerekezi akuseka, ndipo angelo ake akondwera, chifukwa cha ophedwa a ana aamuna ndi aakazi okongola a anthu anga; ndipo ndi chifukwa cha mphulupulu ndi zonyansa zawo kuti iwo agwa!

3 Taonani, mzindawo uwo waukulu Zarahemula ndawotcha ndi moto, ndi okhalamo ake.

4 Ndipo taonani, mzindawo waukulu Moroni ndapangitsa kuti umire mu kuya kwa m’nyanja, ndi okhalamo ake kukamizidwa.

5 Ndipo taonani, mzinda waukuluwo Moroniha ndaphimba ndi donthi, ndi okhala m’menemo, kubisa mphulupulu zawo ndi zonyansa zawo pamaso panga, kuti mwazi wa aneneri ndi oyera mtima usadzandibwelerenso motsutsana nawo.

6 Ndipo taonani, mzinda wa Giligala ndapangitsa kuti umile, ndipo kuti anthu okhalamo akwiliridwe mu kuya kwa minthaka;

7 Inde, mzinda wa Oniha ndi okhala m’menemo, ndi mzinda wa Mokumu ndi okhala m’menemo, ndi mzinda wa Yerusalemu ndi okhala m’menemo; ndipo ndachititsa kuti madzi atuluke m’malo mwake, kuti ndibise kuipa kwawo ndi zonyansa pamaso panga, kuti mwazi wa aneneri ndi oyera mtima usadzabwerenso kwa ine motsutsana nawo.

8 Ndipo taonani, mzindawo wa Gadiyandi, ndi mzindawo wa Gadiomuna, ndi mzinda wa Yakobo, ndi mzinda wa Gimugimuno, yonseyi ndaimiza, ndi kupanga zitunda ndi zigwa m’malo mwake; ndipo anthu okhala m’menemo ndawakwilira mu kuya kwa minthaka, kuti ndibise kuipa kwawo ndi zonyansa kuchokera pamaso panga, kuti mwazi wa aneneri ndi oyera mtima usadzabwerenso kwa ine motsutsana nawo.

9 Ndipo taonani, mzinda waukuluwo Yakobogati, umene mudali kukhala anthu a mfumu Yakobo, ndawutentha ndi moto chifukwa cha machimo awo, ndi kuipa kwawo, kumene kudali pamwamba pa kuipa konse kwa dziko lapansi, chifukwa cha kupha ndi magulu awo achinsinsi; pakuti adali iwo amene adawononga mtendere wa anthu anga ndi boma la dziko; kotero ndidawachititsa kuti atenthedwe, kuti awonongeke kuchoka pamaso panga, kuti mwazi wa aneneri ndi oyera mtima usadzabwerenso kwa Ine motsutsana nawo.

10 Ndipo taonani, mzindawo wa Lamani, ndi mzindawo wa Yosi, ndi mzindawo wa Gadi, ndi mzindawo wa Kisikumeni, ndachititsa kuti utenthedwe ndi moto, ndi anthu okhala mwa iwo, chifukwa cha kuipa kwawo m’kuthamangitsa aneneri, ndi kuponya miyala iwo amene ndidawatuma kuti alengeze kwa iwo zokhudza kuipa kwawo ndi zonyansa zawo.

11 Ndipo chifukwa adawaponya onsewo kunja, kuti padalibe olungama olo m’modzi pakati pawo, ndidatumiza moto pansi ndi kuwawononga, kuti zoipa ndi zonyansa zawo zibisike pamaso pa nkhope yanga, kuti mwazi wa aneneri ndi oyera mtima amene ndidawatumiza pakati pawo usalilire kwa ine kuchokera mu nthaka motsutsa iwo.

12 Ndipo ziwonongeko zazikulu zambiri ndachititsa kuti zidze pa dziko lino, ndi pa anthu awa, chifukwa cha kuipa kwawo ndi zonyansa zawo.

13 O nonse amene mudasiyidwa chifukwa mudali olungama kuposa iwo, kodi tsopano simudzabwelera kwa ine, ndi kulapa machimo anu, ndi kutembenuka, kuti ndikuchizeni inu?

14 Inde, indetu ndinena kwa inu, ngati mudzabwera kwa ine mudzakhala nawo moyo wosatha. Taonani, mkono wanga wachifundo watambasulidwa kwa inu, ndipo aliyense amene adzabwere, iye ndidzamulandira; ndipo odala iwo amene adza kwa ine.

15 Taonani, ine ndine Yesu Khristu Mwana wa Mulungu. Ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse ziri m’menemo. Ine ndidali ndi Atate kuyambira pachiyambi. Ine ndiri mwa Atate, ndipo Atate ali mwa ine; ndipo mwa ine Atate adalemekeza dzina lawo.

16 Ndidadza kwa anga, ndipo anga sadandilandire. Ndipo malemba woyera okhudza kubwera kwanga akwaniritsidwa.

17 Ndipo ambiri onse amene adandilandira ine, kwa iwo ndapereka kuti akhale ana a Mulungu; ndipo chimodzimodzinso ndidzatero kwa onse amene adzakhulupilira dzina langa, pakuti taonani, mwa ine chiwombolo chidzafika, ndipo mwa ine, chilamulo cha Mose chakwaniritsidwa.

18 Ine ndine kuwala ndi moyo wa dziko lapansi. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza.

19 Ndipo simudziperekanso nsembe kwa ine yakukhetsa mwazi; inde nsembe zanu ndi zopereka zanu zopsereza zidzathetsedwa; pakuti sindidzalandira nsembe zanu zonse, ndi zopereka zanu zopsereza.

20 Ndipo mudzipereka kwa ine nsembe ya mtima wosweka ndi mzimu wolapa. Ndipo amene adza kwa ine ndi mtima wosweka ndi mzimu wolapa; ameneyo ndidzamubatiza ndi moto ndi Mzimu Woyera, monganso ngati Alamani; chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa ine pa nthawi ya kutembenuka kwawo, adabatizidwa ndi moto ndi Mzimu Woyera, ndipo iwo sadadziwe izo.

21 Taonani, ndabwera ku dziko lapansi kudzabweretsa chiwombolo pa dziko lapansi, kuti ndipulumutse dziko lapansi ku uchimo.

22 Choncho amene walapa ndipo adza kwa Ine ngati kamwana, ameneyo ndidzamulandira; pakuti ufumu wa Mulungu uli wa otere. Taonani, chifukwa cha otere ndapereka moyo wanga, ndipo ndautenganso; kotero lapani, ndipo idzani kwa ine inu malekezero a dziko lapansi, ndikupulumutsidwa.