Malembo Oyera
Mosiya 24


Mutu 24

Amuloni azunza Alima ndi anthu ake—Iwo akuyenera kuphedwa ngati apemphera—Ambuye apanga zolemetsa zawo kukhala zopepuka—Awawombola iwo kuchokera mu ukapolo, ndipo abwelera ku Zarahemula. Mdzaka dza pafupifupi 145–120 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Amuloni adalandira chisomo pamaso pa mfumu ya Alamani; kotero, mfumu ya Alamani idapereka kwa iye ndi abale ake kuti iwo asankhidwe kukhala aphunzitsi pa anthu ake, inde; ngakhale pa anthu okhala m’dziko la Shemuloni, ndi m’dziko la Shilomu, ndi m’dziko la Amuloni.

2 Pakuti Alamani adali atatenga maiko onsewa; kotero, mfumu ya Alamani idayika mafumu pa maiko onsewa.

3 Ndipo tsopano dzina la mfumu ya Alamani lidali Lamani, otchedwa pambuyo pa dzina la atate ake; ndipo kotero iye adatchedwa mfumu Lamani. Ndipo adali mfumu ya anthu ambiri.

4 Ndipo adasankha aphunzitsi a abale a Amuloni m’dziko lirironse limene lidali ndi anthu ake; ndipo motero chiyankhulo cha Nefi chidayamba kuphunzitsidwa pakati pa anthu onse a Alamani.

5 Ndipo adali anthu okondana wina ndi mzake; komabe sankamudziwa Mulungu; ngakhale abale a Amuloni sadawaphunzitse iwo kalikonse kokhudzana ndi za Ambuye Mulungu wawo, kapena lamulo la Mose; ngakhale kuwaphunzitsa iwo mawu a Abinadi;

6 Koma adawaphunzitsa kuti adzisunga zolemba zawo, ndi kuti adzilemberana wina ndi mzake.

7 Ndipo motero Alamani adayamba kuwonjezeka mu chuma, ndipo adayamba kugulitsana wina ndi mzake ndi kukhala wolemera, ndipo adayamba kukhala anthu wochenjeretsa ndi anzeru, monga ku nzeru za dziko, inde, anthu ochenjera kwambiri, wokondwera ndi mtundu uliwonse wa kuipa ndi kulandana; kupatula pamene padali pakati pa abale awo.

8 Ndipo tsopano zidachitika kuti Amuloni adayamba kutenga ulamuliro pa Alima ndi abale ake, ndipo adayamba kumuzunza, ndi kuchititsa kuti ana ake azunze ana awo.

9 Pakuti Amuloni ankadziwa Alima, kuti adali m’modzi wa ansembe a mfumu, ndipo kuti adali iye amene adakhulupilira mawu a Abinadi ndipo adathamangitsidwa pamaso pa mfumu, ndipo kotero iye adamukwiyira iye; pakuti iye adali womvera kwa mfumu Lamani, komabe iye adagwiritsa ulamuliro pa iwo, ndipo adaika ntchito zolemetsa pa iwo, ndipo adaika akapitawo a ntchito pa iwo.

10 Ndipo zidachitika kuti aakulu adali masautso awo kuti iwo adayamba kulira mwamphamvu kwa Mulungu.

11 Ndipo Amuloni adawalamulira iwo kuti asiye kulira kwawo; ndipo adaika alonda kuti adziwayang’anira iwo, kuti aliyense opezeka akuitanira pa Mulungu aphedwe.

12 Ndipo Alima ndi anthu ake sadakweze mawu awo kwa Ambuye Mulungu wawo, koma adatsanulira mitima yawo kwa iye; ndipo iye adadziwa malingaliro a mitima yawo.

13 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adadza kwa iwo m’kusautsidwa kwawo, kuti: Kwezani mitu yanu ndipo khalani wosangalala, pakuti ndikudziwa za pangano limene mwapanga kwa ine; ndipo ndidzapangana ndi anthu anga ndi kuwawombola ku ukapolo.

14 Ndipo ndidzapeputsa zolemetsa zimene zaikidwa pa mapewa anu, kuti ngakhale inu simungathe kuzimva pa misana yanu, ngakhale pamene inu muli mu ukapolo; ndipo izi ndichita kuti inu mukathe kuima ngati mboni zanga kuyambira tsopano, ndi kuti inu muthe kudziwa motsimikiza kuti ine, Ambuye Mulungu, ndimayendera anthu anga m’masautso awo.

15 Ndipo tsopano zidachitika kuti zolemetsa zimene zidaikidwa pa Alima ndi abale ake zidapeputsidwa; inde, Ambuye adawalimbikitsa iwo kuti iwo adatha kusenza zolemetsa zawo mosavuta, ndipo iwo adagonjera mokondwera ndi kuleza mtima ku chifuniro chonse cha Ambuye.

16 Ndipo zidachitika kuti chachikulu chidali chikhulupiliro chawo ndi kuleza mtimakwawo kuti mawu a Ambuye adabwera kwa iwo kachiwiri, kuti: Khalani wosangalala, pakuti mawa ndidzakuwombolani inu kuchokera mu ukapolo.

17 Ndipo iye adati kwa Alima: Iwe udzatsogolera anthu awa, ndipo ine ndidzapita nawe ndi kuwombola anthu awa mu ukapolo.

18 Tsopano zidachitika kuti Alima ndi anthu ake mu nthawi ya usiku adasonkhanitsa nkhosa zawo pamodzi, ndiponso mbewu zawo; inde, ngakhale usiku onse adali akusonkhanitsa ziweto zawo pamodzi.

19 Ndipo m’mawa Ambuye adachititsa tulo lalikulu kuti lidze pa Alamani, inde, ndipo woyang’anira ntchito awo onse adali mu tulo tofanato.

20 Ndipo Alima ndi anthu ake adanyamuka kupita kuchipululu; ndipo pamene iwo adayenda tsiku lonse iwo adamanga mahema awo mu chigwa, ndipo iwo adatcha chigwacho Alima, chifukwa iye adatsogolera njira yawo mu chipululu.

21 Inde, ndipo mu chigwa cha Alima adatsanulira mayamiko awo kwa Mulungu chifukwa adawachitira chifundo, ndi kuwapeputsira zolemetsa zawo, ndipo adawapulumutsa kutuluka mu ukapolo; pakuti iwo adali mu ukapolo, ndipo palibe amene akadatha kuwawombola iwo kupatula adali Ambuye Mulungu wawo.

22 Ndipo iwo adayamika Mulungu, inde, abambo awo onse ndi amayi awo onse ndi ana awo onse amene akadatha kuyankhula adakweza mawu awo m’mayamiko a Mulungu wawo.

23 Ndipo tsopano Ambuye adati kwa Alima: Fulumira iwe ndipo dzitulutse ndi anthu awa m’dziko lino, pakuti Alamani adzuka ndipo akukulondolani; kotero tulukani inu m’dziko lino, ndipo ndidzaimitsa Alamani m’chigwa ichi kuti asapitilire kulondora anthu awa.

24 Ndipo zidachitika kuti adaturuka m’chigwacho, ndipo adayenda ulendo wawo wa kuchipululu.

25 Ndipo atakhala m’chipululu masiku khumi ndi awiri adafika m’dziko la Zarahemula; ndipo mfumu Mosiya nayenso adawalandira iwo ndi chisangalalo.

Print