Malembo Oyera
Mosiya 25


Mutu 25

Dzidzukulu dza Muleki ku Zarahemula zidakhala Anefi—Iwo aphunzira za anthu a Alima ndi a Zenifu—Alima abatiza Limuhi ndi anthu ake onse—Mosiya aloreza Alima kupanga mpingo wa Mulungu. Mdzaka dza pafupifupi 120 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano mfumu Mosiya idapangitsa kuti anthu onse asonkhanitsidwe pamodzi.

2 Tsopano padalibe ambiri a ana a Nefi, kapena ochuluka kwambiri a iwo amene adali dzidzukulu dza Nefi, monga adaliri mwa anthu a ku Zarahemula, amene adali dzidzukulu dza Muleki, ndi iwo amene adabwera ndi iye mu chipululu.

3 Ndipo kudalibe wochuluka kwambiri a anthu a Nefi ndi a anthu a Zarahemula monga adaliri a Alamani; inde, iwo sadakwane theka lochuluka motero.

4 Ndipo tsopano anthu onse a Nefi adasonkhana pamodzi, ndipo nawonso anthu onse a Zarahemula, ndipo adasonkhana pamodzi m’magulu awiri.

5 Ndipo zidachitika kuti Mosiya adawerenga, ndi kuchititsa kuti ziwerengedwe, zolemba za Zenifu kwa anthu ake; inde, adawerenga malembo a anthu a Zenifu, kuchokera pamene adasiya dziko la Zarahemula mpaka pamene adabweleranso.

6 Ndipo adawerenganso nkhani ya Alima ndi abale ake, ndi zosautsa zawo zonse, kuchokera pamene adachoka m’dziko la Zarahemula mpaka pamene adabweleranso.

7 Ndipo tsopano, pamene Mosiya atamaliza kuwerenga zolembazo, anthu ake amene adatsalira m’dzikolo adakhudzidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa.

8 Pakuti sadadziwe choti aganize; pakuti pamene iwo adawona amene adamasulidwa kuchokera mu ukapolo adadzadzidwa ndi chisangalalo chachikulu kwambiri.

9 Ndiponso, pamene iwo adaganiza za abale awo amene adaphedwa ndi Alamani iwo adadzadzidwa ndi chisoni, ndipo mpakana adakhetsa misozi yambiri ya chisoni.

10 Ndiponso, pamene adaganiza za ubwino wa nthawi yomweyo wa Mulungu, ndi mphamvu yake m’kuwombola Alima ndi abale ake kuchokera m’manja mwa Alamani ndi mu ukapolo, iwo adakweza mawu awo ndipo adayamika Mulungu.

11 Ndiponso, pamene adalingalira pa Alamani, amene adali abale awo, za mkhalidwe wawo wauchimo ndi wodetsedwa, iwo adadzadzidwa ndi ululu ndi kuwawidwa pa kufunikira kwa miyoyo yawo.

12 Ndipo zidachitika kuti amene adali ana a Amuloni ndi abale ake, amene adatenga kuti akhale akazi awo ana aakazi a Alamani, adaipidwa ndi khalidwe la makolo awo, ndipo sadafune kutchulidwanso ndi maina a makolo awo, choncho adadzitengera pa wokha dzina la Nefi, kuti adzitha kutchulidwa ana a Nefi ndi kuwerengedwa m’kati mwa iwo amene adaitanidwa Anefi.

13 Ndipo tsopano anthu onse a Zarahemula adawerengedwa ndi Anefi, ndipo izi chifukwa ufumu udali usadaperekedwe pa wina aliyense koma iwo amene adali zidzukulu dza Nefi.

14 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Mosiya adatha kuyankhula ndi kuwerenga kwa anthu, adafuna kuti Alima nayenso ayankhule kwa anthu.

15 Ndipo Alima adayankhula kwa iwo, pamene adasonkhana pamodzi m’magulu aakulu, ndipo iye adapita kuchokera ku gulu limodzi kupita ku lina, kulalikira kwa anthu kulapa ndi chikhulupiliro pa Ambuye.

16 Ndipo iye adalimbikitsa anthu a Limuhi ndi abale ake, onse amene adawawombola ku ukapolo, kuti akumbukire kuti adali Ambuye amene adawawombola.

17 Ndipo zidachitika kuti Alima atamaliza kuphunzitsa anthu zinthu zambiri, ndipo atamaliza kuyankhula kwa iwo, mfumu Limuhi adafuna kuti abatizidwe; ndi anthu ake onse adafuna kuti abatizidwenso.

18 Kotero, Alima adapita m’madzi ndipo adawabatiza iwo; inde, iye adawabatiza iwo mwa njira imene adachitira abale ake m’madzi a Mormoni; inde, ndipo wochuluka amene iye adawabatiza adalowa mu mpingo wa Mulungu; ndipo izi chifukwa cha chikhulupiliro chawo pa mawu a Alima.

19 Ndipo zidachitika kuti mfumu Mosiya idapereka kwa Alima kuti akhonza kukhazikitsa mipingo mozungulira dziko lonse la Zarahemula; ndipo adampatsa iye mphamvu yakudzodza ansembe ndi aphunzitsi pa mpingo uliwonse.

20 Tsopano zidachitika kuti chifukwa padali anthu ambiri kotero kuti sakadatha kutsogoleredwa onse ndi mphunzitsi m’modzi; kapena sakadatha kumva mawu a Mulungu mu msonkhano umodzi;

21 Kotero iwo adasonkhana iwo wokha pamodzi m’magulu osiyana, wotchedwa mipingo; mpingo uliwonse kukhala ndi ansembe awo ndi aphunzitsi awo, ndi wansembe aliyense kulalikira mawu monga momwe adaperekedwa kwa iye mwa pakamwa pa Alima.

22 Ndipo motero, posaona kuti kudali mipingo yambiri iyo yonse idali mpingo umodzi, inde, ngakhale mpingo wa Mulungu; pakuti padalibe china chimene chidalalikidwa m’mipingo yonse kupatula icho chidali kulapa ndi chikhulupiliro mwa Mulungu.

23 Ndipo tsopano mudali mipingo isanu ndi iwiri m’dziko la Zarahemula. Ndipo zidachitika kuti aliyense amene adafuna kutenga pa iwo dzina la Khristu, kapena la Mulungu, iwo adalowa mipingo ya Mulungu;

24 Ndipo adatchedwa anthu a Mulungu. Ndipo Ambuye adatsanulira Mzimu wake pa iwo, ndipo iwo adadalitsidwa, ndipo adachita bwino m’dzikolo.