Malembo Oyera
Mosiya 27


Mutu 27

Mosiya aletsa mazunzo ndipo alamulira kufanana—Alima wamng’ono ndi ana aamuna anayi a Mosiya afunafuna kuwononga Mpingo—Mngelo awonekera ndi kuwalamulira iwo kusiya njira yawo yoipa—Alima akanthidwa kukhala wosayankhula—Anthu onse ayenera kubadwa mwatsopano kuti alandire chipulumutso—Alima ndi ana aamuna a Mosiya alalikira uthenga wabwino. Mdzaka dza pafupifupi 100–92 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti mazunzo amene adachitidwa pa mpingo ndi wosakhulupilira adakhala aakulu kotero kuti mpingo udayamba kung’ung’udza, ndi kudandaula kwa atsogoleri awo zokhudza nkhaniyo; ndipo adadandaula kwa Alima. Ndipo Alima adaika mlanduwo pamaso pa mfumu yawo, Mosiya. Ndipo Mosiya adakambilana ndi ansembe ake.

2 Ndipo zidachitika kuti mfumu Mosiya adatumiza chilengezo m’dziko lonselo kuti pasakhale osakhulupilira aliyense akuzunza iwo amene adali a mpingo wa Mulungu.

3 Ndipo padali lamulo lokhwima m’mipingo yonse, kuti pasakhale mazunzo pakati pawo, kuti pakhale kufanana mwa anthu onse;

4 Kuti asalore kunyada, kapena kudzikuza kusokoneza mtendere wawo; kuti aliyense adzimuganizira mnansi wake monga iye mwini, kugwira ntchito ndi manja awo pa chithandizo chawo.

5 Inde, ndipo ansembe awo onse ndi aphunzitsi agwire ntchito ndi manja awo pa chithandizo chawo, m’zochitika zonse kupatula mu matenda, kapena m’kusowa kwakukulu; ndipo pochita izi adasefukira m’chisomo cha Mulungu

6 Ndipo mudayambanso kukhala mtendere wambiri m’dzikomo; ndipo anthu adayamba kukhala ochuluka kwambiri, ndipo adayamba kumwazikana pa nkhope ya dziko lapansi, inde, kumpoto ndi kummwera, kummawa ndi kumadzulo, akumanga mizinda ikuluikulu ndi midzi m’madera onse a dzikolo.

7 Ndipo Ambuye adawayendera ndi kuwachititsa bwino, ndipo adakhala anthu aakulu ndi olemera.

8 Tsopano ana aamuna a Mosiya adawerengedwa pakati pa wosakhulupilira; ndiponso m’modzi wa ana aamuna a Alima adawerengedwa pakati pawo, iye otchedwa Alima, pambuyo pa abambo ake; komabe, adakhala munthu oipa kwambiri ndi wopembedza mafano. Ndipo iye adali munthu wa mawu ambiri, ndipo adayankhula zosyasyalika zambiri kwa anthu; kotero adatsogolera anthu ambiri kuchita monga mwa mphulupulu zake.

9 Ndipo iye adakhala chotchinga chachikulu mu kupita patsogolo kwa Mpingo wa Mulungu; kuba mitima ya anthu; kuyambitsa kusagwirizana kwambiri pakati pa anthu; kupereka mwayi kwa mdani wa Mulungu kuti agwiritse ntchito mphamvu zake pa iwo.

10 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene iye adali kupita kowononga mpingo wa Mulungu, pakuti iye adapita mobisa ndi ana aamuna a Mosiya kufunafuna kukawononga mpingo, ndi kusokeretsa anthu a Ambuye, motsutsana ndi malamulo a Mulungu, kapena ngakhale mfumu—

11 Ndipo monga ndidanena kwa inu, pamene adali kupita motsutsana ndi Mulungu, taonani, mngelo wa Ambuye adaonekera kwa iwo; ndipo adatsika ngati mumtambo; ndipo adayankhula monga ngati ndi mawu a bingu, limene lidachititsa dziko kugwedezeka pamene iwo adaima;

12 Ndipo kwakukulu kudali kuzizwa kwawo, kuti iwo adagwa pansi, ndipo sadamve mawu amene iye adayankhula kwa iwo.

13 Komabe adafuula kachiwiri, kuti: Alima, nyamuka ndipo imilira, n’chifukwa chiyani iwe ukuzunza mpingo wa Mulungu? Pakuti Ambuye adati: Uwu ndi mpingo wanga, ndipo ndidzaukhazikitsa; ndipo palibe chimene chidzaugwetse, kupatula kuti ndi kulakwa kwa anthu anga.

14 Ndiponso, mngeloyo adati, Taona, Ambuye amva mapemphero a anthu ake, ndiponso mapemphero a mtumiki wake, Alima, amene ali atate ako; pakuti wapemphera ndi chikhulupiliro chochuluka zokhudza iwe kuti uthe kubweretsedwa ku chidziwitso cha choonadi; kotero, chifukwa cha ichi ndabwera kudzakutsimikizira iwe za mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu, kuti mapemphero a atumiki ake ayankhidwe monga mwa chikhulupiliro chawo.

15 Ndipo tsopano taona, kodi ungathe kutsutsana ndi mphamvu ya Mulungu? Pakuti taona, kodi mawu anga sakugwedeza dziko lapansi? Ndipo siukundionanso Ine pamaso pako kodi? Ndipo Ine ndidatumidwa kuchokera kwa Mulungu.

16 Tsopano ndikunena kwa iwe: Pita, ndipo kumbukira ukapolo wa makolo ako m’dziko la Helamu, ndi m’dziko la Nefi; ndipo kumbukira zazikulu zimene adawachitira; pakuti adali akapolo, ndipo iye adawapulumutsa. Ndipo tsopano ndikunena kwa iwe, Alima, pita njira yako, ndipo usafunenso kuwononga mpingo, kuti mapemphero awo ayankhidwe, ndipo ichi ngakhale udzataidwa mwa iwe wekha.

17 Ndipo tsopano zidachitika kuti awa adali mawu otsiriza amene mngelo adayankhula kwa Alima, ndipo adachoka.

18 Ndipo tsopano Alima ndi iwo amene adali naye adagwanso pansi, pakuti kuzizwa kwawo kudali kwakukulu; pakuti ndi maso awo womwe adaona mngelo wa Ambuye; ndipo mawu ake adali ngati bingu limene lidagwedeza dziko lapansi; ndipo iwo ankadziwa kuti padalibe china koma mphamvu ya Mulungu imene ingathe kugwedeza dziko lapansi ndi kulichititsa kunjenjemera ngati kuti ling’ambika.

19 Ndipo tsopano kuzizwa kwa Alima kudali kwakukulu kotero kuti adakhala osayankhula, kuti sadathe kutsegula pakamwa pake; inde, ndipo adakhala wofooka, ngakhale kuti sadathe kusuntha manja ake; kotero adatengedwa ndi iwo amene adali naye, ndikumunyamula opanda mphamvu, kufikira atamugoneka pamaso pa atate ake

20 Ndipo iwo adabwereza kwa atate ake zonse zidawachitikira; ndipo atate ake adakondwera, pakuti adadziwa kuti idali mphamvu ya Mulungu.

21 Ndipo iwo adachititsa kuti khamu la anthu lisonkhane pamodzi kuti lione zimene Ambuye adamuchitira mwana wawo, ndiponso kwa iwo amene adali naye.

22 Ndipo adapangitsa kuti ansembe asonkhane pamodzi; ndipo adayamba kusala kudya, ndi kupemphera kwa Ambuye Mulungu wawo kuti atsegule pakamwa pa Alima, kuti ayankhule, ndiponso kuti ziwalo zake zilandire mphamvu zake—kuti maso a anthu atseguke kuti aone ndi kudziwa za ubwino ndi ulemelero wa Mulungu.

23 Ndipo zidachitika atasala kudya ndi kupemphera kwa nthawi ya masiku awiri usana ndi usiku, ziwalo za Alima zidalandira mphamvu zake, ndipo adaimilira ndipo adayamba kuyankhula kwa iwo, kuwauza kuti akhale wosangalala.

24 Pakuti, adati iye, ndalapa machimo anga, ndipo ndawomboledwa ndi Ambuye; taonani, ndabadwa mwa Mzimu.

25 Ndipo Ambuye adati kwa ine: Usadabwe kuti anthu onse, inde, amuna ndi akazi, maiko onse, mafuko, zinenero ndi anthu, akuyenera kubadwa mwatsopano; inde, wobadwa mwa Mulungu, wosandulika kuchokera ku mkhalidwe wawo wathupi ndi wakugwa, kupita ku mkhalidwe wa chilungamo, atawomboledwa ndi Mulungu, kukhala ana ake aamuna ndi aakazi;

26 Ndipo kotero iwo amakhala zolengedwa zatsopano; ndipo pokhapokha ngati angachite izi, sangalandire konse ufumu wa Mulungu.

27 Ine ndikunena kwa inu, ngati si kutero, iwo akuyenera kutaidwa; ndipo ichi ndikudziwa, chifukwa ndidali ngati wotayidwa.

28 Komabe, nditadutsa m’chisautso chambiri, kulapa kufupi ndi imfa, Ambuye mu chifundo adaona koyenera kundilanditsa ine kuchokera mu kupsa kosatha, ndipo ndidabadwa mwa Mulungu.

29 Moyo wanga wawomboledwa ku ndulu ya zowawa ndi nsinga za mphulupulu. Ndidali muphompho lamdima waukulu; koma tsopano ndikuona kuwala kodabwitsa kwa Mulungu. Moyo wanga udazunzika ndi mazunzo amuyaya; koma ndalanditsidwa, ndipo moyo wanga su kuwawanso.

30 Ndidakana Muwomboli wanga, ndipo ndidakana chimene chidanenedwa ndi makolo athu; koma tsopano, kuti aoneretu kuti adzabwera, ndipo kuti iye amakumbukira zolengedwa zonse za chilengedwe chake, adzadzionetsa yekha kwa onse.

31 Inde bondo lirilonse lidzagwada, ndi lilime lirilonse lidzavomereza pamaso pake. Inde, ngakhale pa tsiku lomaliza, pamene anthu onse adzaimilira kuti aweruzidwe ndi iye, pamenepo iwo adzavomereza kuti iye ndi Mulungu; pamenepo iwo adzavomereza, wokhala wopanda Mulungu m’dziko lapansi, kuti chiweruzo cha chilango chosatha chiri cholungama pa iwo; ndipo iwo adzanjenjemera, ndi kunthunthumira, ndi kugwa pansi pa kuyang’ana kwa diso lake lofufuza zonse.

32 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima adayamba kuchokera nthawi iyi kupita m’tsogolo kuphunzitsa anthu, ndi iwo amene adali ndi Alima pa nthawi imene mngelo adaonekera kwa iwo, kuyenda kuzungulira dziko lonse, kulalikira kwa anthu onse zinthu zimene adamva ndi kuziona, ndi kulalikira mawu a Mulungu m’chisautso chambiri, pozunzidwa kwambiri ndi iwo wosakhulupilira, ndikukanthidwa ndi ambiri a iwo.

33 Koma pakusaona zonsezi, iwo adapereka chitonthozo chachikulu kwa mpingo, kutsimikizira chikhulupiliro chawo, ndi kuwalimbikitsa iwo ndi kuleza mtima ndi kuvutika kwambiri ku kusunga malamulo a Mulungu.

34 Ndipo anayi a iwo adali ana aamuna a Mosiya; ndipo maina awo ndiwo Amoni, ndi Aroni, ndi Omineri, ndi Himuni; awa adali maina a ana aamuna a Mosiya.

35 Ndipo iwo adayenda m’dziko lonse la Zarahemula, ndipo pakati pa anthu onse amene adali pansi pa ulamuliro wa mfumu Mosiya, kuyesetsa mwachangu kukonza zovulaza zonse zimene adachita ku mpingo, kuulura machimo awo onse, ndi kufalitsa zinthu zonse zimene adaona, ndi kufotokoza mauneneri ndi malemba kwa onse amene adafuna kumva iwo.

36 Ndipo motero iwo adali zipangizo m’manja mwa Mulungu m’kubweretsa ambiri ku chidziwitso cha choonadi, inde, ku chidziwitso cha Muwomboli wawo.

37 Ndipo ndi wodala motani nanga! Pakuti adalalikira mtendere; adalengeza nkhani yabwino; ndipo iwo adalengeza kwa anthu kuti Ambuye akulamulira.