Malembo Oyera
Mosiya 8


Mutu 8

Amoni aphunzitsa anthu a Limuhi—Aphunzila za mapale makumi awiri ndi anayi a Yaredi—Malemba akale angamasuliridwe ndi alosi—Palibe mphatso yoposa ya ulosi. Mdzaka dza pafupifupi 121 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti mfumu Limuhi atamaliza kuyankhula kwa anthu ake, pakuti adayankhula nawo zambiri, ndipo zowerengeka za izo ndazilemba m’buku ili; adawauza anthu ake zinthu zonse zokhudzana ndi abale awo omwe adali m’dziko la Zarahemula.

2 Ndipo iye adapangitsa kuti Amoni aimilire pamaso pa khamulo, ndi kufotokoza kwa iwo zonse zimene zidachitika kwa abale awo kuyambira nthawi yomwe Zenifi adakwera kuchokera m’dzikolo kufikira nthawi imene iye mwini adadza kuchokera m’dzikolo.

3 Ndipo adawafotokozeranso mawu otsiriza amene mfumu Benjamini idawaphunzitsa, ndipo adawafotokoza iwo kwa anthu a mfumu Limuhi, kotero kuti amvetsetse mawu onse amene iye adanena.

4 Ndipo zidachitika kuti atatha kuchita zonsezi, kuti mfumu Limuhi idabalaritsa khamulo, ndipo idapangitsa kuti iwo abwelere aliyense ku nyumba yake.

5 Ndipo zidachitika kuti adapangitsa kuti mapale omwe adali ndi zolemba za anthu ake kuchokera pamene iwo adachoka m’dziko la Zarahemula, akuyenera kubweretsedwa pamaso pa Amoni, kuti athe kuwawerenga.

6 Tsopano, Amoni atangowerenga zolembazo, mfumu idafunsa kwa iye kuti adziwe ngati angatanthauzire zinenero, ndipo Amoni adamuwuza iye kuti sakadatha.

7 Ndipo mfumu idati kwa iye: Ndikumva chisoni chifukwa cha masautso a anthu anga, ndidapangitsa kuti makumi anayi ndi atatu a anthu anga atenge ulendo wopita m’chipululu, kuti mwa kutero akapeze dziko la Zarahemula, kuti tikapemphe abale athu kuti atiwombole ku ukapolo.

8 Ndipo iwo adatayika m’chipululu kwa masiku ambiri, komabe iwo adali akhama, ndipo sadapeze dziko la Zarahemula koma adabwelera ku dziko lino, atayenda m’dziko lapakati pa madzi ambiri, atapeza dziko lokutidwa ndi mafupa a anthu ndi a nyama; ndipo lidakutidwanso ndi mabwinja a nyumba zamitundumitundu; atapeza dziko limene lidali ndi anthu amene adali ochuluka ngati makamu a Israeli.

9 Ndipo mwa umboni kuti zimene adanena ndi zoona adabwera nawo mapale makumi awiri mphambu zinayi zodzadza ndi zozokota, za golidi weniweni.

10 Ndipo taonani, abweretsanso za pachifuwa, zomwe ndi zazikulu, ndipo ziri zamkuwa ndi zakopa, ndipo ndi za bwino.

11 Ndipo kenako, adabweretsano malupanga, zogwilira zake zawonongeka, ndi mipeni yake idachita dzimbiri; ndipo palibe aliyense m’dzikomu amene angathe kumasulira chinenero kapena zozokota zimene ziri pa mapale. N’chifukwa chake ndidanena kwa iwe: Kodi siungathe kumasulira?

12 Ndipo ndikunenanso kwa iwe; Kodi ukudziwa aliyense amene angamasulire? Pakuti ine ndikufuna kuti zolemba izi zimasuliridwe mu chinenero chathu; chifukwa, mwina, zidzatidziwitsa za otsala a anthu amene adawonongedwa; kumene zolembedwa izi zidachokera; kapena, mwina, zidzatidziwitsa za anthu awa amene adawonongeka; ndipo ndikufuna kudziwa chifukwa cha chiwonongeko chawo.

13 Tsopano Amoni adati kwa iye: Ndithu ndikukuuzani, O mfumu, za munthu wokutha kumasulira malemba; pakuti ali nacho chimene angayang’ane nacho; ndi kumasulira zolembedwa zonse zakale; ndipo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndipo zinthuzo zimatchedwa zomasulira, ndipo palibe munthu angayang’ane mwaizo pokhapokha atalamulidwa, kuti angayang’ane zimene sakuyenera ndi kuwonongeka. Ndipo amene walamulidwa kuyang’ana mwaizo; yemweyo amatchedwa mlosi.

14 Ndipo taonani, mfumu ya anthu amene ali m’dziko la Zarahemula ndiye munthu amene akulamulidwa kuchita zinthu izi; ndi amene ali nayo mphatso yapamwambayi yochokera kwa Mulungu.

15 Ndipo mfumu idanena kuti mlosi ndi wamkulu kuposa mneneri.

16 Ndipo Amoni adanena kuti mlosi ndi mvumbulutsi ndi mneneri; ndi mphatso imene ili yaikulu palibe munthu angakhale nayo pokhapokha atakhala ndi mphamvu ya Mulungu; imene palibe munthu angathe; koma munthu angakhale nayo mphamvu yaikulu yopatsidwa kwa iye yochokera kwa Mulungu.

17 Koma mlosi amatha kudziwa zinthu zakale, komanso za zinthu zimene ziri nkudza, ndipo mwa iwo zinthu zonse zidzaululidwa, kapena, kuti, zobisika zidzaonekera, ndi zobisika zidzaonekera poyera; ndipo zinthu zomwe sizidziwika zidzadziwika ndi iwo, ndipo zinthu zidzadziwika ndi iwo zomwe sizikadatheka kudziwika.

18 Kotero Mulungu wapereka njira kuti munthu, mwa chikhulupiliro, akhonza kuchita zozizwitsa zamphamvu; kotero amakhala waphindu lalikulu kwa anthu anzake.

19 Ndipo tsopano, pamene Amoni adatha kunena mawu awa, mfumu idakondwera kwambiri; ndipo idayamika Mulungu, nati: Mosakaikira chinsinsi chachikulu chiri mkati mwa mapale awa, ndipo zomasulirazi mosakayikira zidakonzekeretsedwa ndi cholinga chovumbulutsa zinsinsi zonsezi kwa ana a anthu.

20 Ndi zodabwitsa bwanji ntchito za Ambuye, ndipo mpaka liti adzakhala akuzunzika ndi anthu ake; inde, ndipo ndi khungu lanji ndi kusafikirika kotani zili nzeru za ana a anthu; pakuti sadzafunafuna nzeru; ndipo safuna kuti iyo ziwalamulire;

21 Inde, ali ngati nkhosa zakuthengo zothawa m’busa, ndi zobalalika; ndi kuthamangitsidwa, ndipo zimadyedwa ndi zilombo za m’nkhalango.