Malembo Oyera
Mosiya 23


Nkhani ya Alima ndi anthu a Ambuye, amene adathamangitsidwira m’chipululu ndi anthu a Mfumu Nowa.

Zophatikizidwa ku Mitu 23 ndi 24.

Mutu 23

Alima akana kukhala mfumu—Iye atumikira monga mkulu wansembe—Ambuye alanga anthu ake, ndipo Alamani agonjetsa dziko la Helamu—Amuloni, mtsogoleri wa ansembe oipa a Mfumu Nowa, alamulira pansi pa mfumu yachilamani. Mdzaka dza pafupifupi 145–121 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano Alima, atachenjezedwa ndi Ambuye kuti ankhondo a mfumu Nowa adzabwera pa iwo, ndipo atachidziwitsa kwa anthu ake, kotero adasonkhanitsa pamodzi ziweto zawo, ndipo adatengako mbewu zawo, ndipo adanyamuka kupita kuchipululu asadabwere ankhondo a mfumu Nowa.

2 Ndipo Ambuye adawalimbikitsa, kotero kuti anthu a mfumu Nowa sadathe kuwapeza kuti awawononge.

3 Ndipo adathawira m’chipululu ulendo wa masiku asanu ndi atatu.

4 Ndipo iwo adafika ku dziko, inde, ngakhale dziko lokongola ndi lokondweretsa, dziko la madzi oyera bwino.

5 Ndipo iwo adakhoma mahema awo, ndipo adayamba kulima m’nthaka, ndipo adayamba kumanga manyumba; inde, iwo adali olimbikila, ndipo ankagwira ntchito mopitilira muyeso.

6 Ndipo anthu adali okhumbira kuti Alima akhale mfumu yawo, pakuti adali wokondedwa ndi anthu ake.

7 Koma iye adati kwa iwo, Taonani, sikuli koyenera kuti tikhale ndi mfumu; pakuti akutero Ambuye: Inu simudzatenga thupi limodzi kukhala lapamwamba kuposa linzake, kapena munthu m’modzi sadzadziyesa yekha kukhala wapamwamba pa mzake; kotero, ndikunena kwa inu sikuli koyenera kuti mukhale ndi mfumu.

8 Komabe, ngati kukadakhala kotheka kuti nthawi zonse mungakhale ndi anthu olungama kuti akhale mafumu anu zingakhale bwino kwa inu kukhala ndi mfumu.

9 Koma kumbukirani kusaweruzika kwa mfumu Nowa ndi ansembe ake; ndipo ine mwini ndidagwidwa mu msampha, ndipo ndidachita zinthu zambiri zimene zidali zonyansa pamaso pa Ambuye, zimene zidandichititsa ine kulapa kowawa;

10 Komabe, patatha masautso aakulu, Ambuye adamva kulira kwanga, ndipo adayankha mapemphero anga, ndipo wandipanga ine kukhala chipangizo m’manja mwake pobweretsa ambiri a inu ku chidziwitso cha choonadi chake.

11 Komabe, muzimenezi sindimadzitamandira, pakuti sindili oyenera kudzitamandira ndekha.

12 Ndipo tsopano ine ndikunena kwa inu, mwaponderezedwa ndi mfumu Nowa, ndipo mwakhala mu ukapolo kwa iye ndi ansembe ake, ndipo mwabweretsedwa mu kusaweruzika ndi iwo; kotero mudamangidwa ndi nsinga za kusaweruzika.

13 Ndipo tsopano monga mudamasulidwa ndi mphamvu ya Mulungu kuchokera ku nsinga izi; inde, ngakhale m’manja mwa mfumu Nowa ndi anthu ake, ndiponso ku nsinga za uchimo, kotero ine ndikukhumbira kuti muime mokhazikika muufulu uwu umene mudamasulidwa nawo, ndipo kuti musalore wina kuti akhale mfumu ya inu.

14 Komanso musakhulupilire aliyense kukhala mphunzitsi wanu kapena mtumiki wanu, kupatula iye akhale munthu wa Mulungu, woyenda m’njira zake ndi kusunga malamulo ake.

15 Motere Alima adaphunzitsa anthu ake, kuti munthu aliyense akuyenera kukonda mnansi wake monga iye mwini, kuti pasakhale mkangano pakati pawo.

16 Ndipo tsopano, Alima adali mkulu wawo wansembe, iye pokhala woyambitsa mpingo wawo.

17 Ndipo zidachitika kuti palibe amene adalandira ulamuliro wakulalikira kapena kuphunzitsa, kupatula udapatsidwa kwa iye kuchokera kwa Mulungu. Kotero iye adapatula ansembe awo onse, ndi aphunzitsi awo onse; ndipo palibe adapatulidwa kupatula wokhawo amene adali anthu wolungama.

18 Kotero iwo adayang’anira anthu awo, ndipo adawasamalira iwo ndi zinthu zokhudzana ndi kulungama.

19 Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kuchita bwino kwambiri m’dzikolo; ndipo adalitchula dzikolo Helamu.

20 Ndipo zidachitika kuti iwo adachulukana ndi kuchita bwino kwambiri m’dziko la Helamu; ndipo adamanga mzinda, umene adautchula mzinda wa Helamu.

21 Komabe Ambuye amaona kuti kuli koyenera kulanga anthu ake; inde amayesa kuleza mtima kwawo ndi chikhulupiliro chawo.

22 Komabe—aliyense amene amaika chikhulupiliro chake mwa iye yemweyo adzakwezedwa pa tsiku lotsiriza. Inde, ndipo motero zidali ndi anthu awa.

23 Pakuti, taonani, ndidzaonetsa kwa inu kuti iwo adabweretsedwa mu ukapolo, ndipo palibe amene akadatha kuwalanditsa koma Ambuye Mulungu wawo, inde, ngakhale Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi wa Yakobo.

24 Ndipo zidachitika kuti iye adawawombola iwo, ndipo adaonetsa mphamvu zake zazikulu kwa iwo, ndipo kwakukulu kudali kukondwera kwawo.

25 Pakuti taonani, zidachitika kuti pamene adali m’dziko la Helamu, inde, mu mzinda wa Helamu, pamene amalima minda yozungulira, taonani, gulu lankhondo la Alamani lidali m’malire a dzikolo.

26 Tsopano zidachitika kuti abale a Alima adathawa kuchoka m’minda yawo, ndipo adadzisonkhanitsa wokha pamodzi mumzinda wa Helamu; ndipo iwo adachita mantha kwambiri chifukwa cha kutulukira kwa Alamani.

27 Koma Alima adapita patsogolo ndipo adaima pakati pawo, ndipo adawalimbikitsa iwo kuti asachite mantha, koma kuti akumbukire Ambuye Mulungu wawo ndipo adzawawombola.

28 Kotero iwo adachotsa mantha awo, ndipo adayamba kufuula kwa Ambuye kuti afewetse mitima ya Alamani, kuti awaleke iwo, ndi akazi awo, ndi ana awo.

29 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adafewetsa mitima ya Alamani Ndipo Alima ndi abale ake adatuluka ndipo adadzipereka m’manja mwawo; ndipo Alamani adatenga dziko la Helamu.

30 Tsopano magulu a nkhondo a Alamani, omwe adatsatira anthu a mfumu Limuhi, adali atasochera m’chipululu kwa masiku ambiri.

31 Ndipo taonani, adapeza ansembe aja a mfumu Nowa, m’malo amene adawatchula Amuloni; ndipo iwo adali atayamba kutenga dziko la Amuloni ndipo adayamba kulima mthaka.

32 Tsopano dzina la mtsogoleri wa ansembe amenewo lidali Amuloni.

33 Ndipo zidachitika kuti Amuloni adachondelera Alamani; ndipo adatumizanso akazi awo, womwe adali ana aakazi a Alamani, kuti akachondelere abale awo, kuti asawawononge amuna awo.

34 Ndipo Alamani adali ndi chifundo pa Amuloni ndi abale ake, ndipo sadawawononge chifukwa cha akazi awo.

35 Ndipo Amuloni ndi abale ake adalumikizana ndi Alamani, ndipo iwo adali kuyenda m’chipululu kufunafuna dziko la Nefi pamene adapeza dziko la Helamu, lomwe limakhalidwa ndi Alima ndi abale ake.

36 Ndipo zidachitika kuti Alamani adalonjeza kwa Alima ndi abale ake, kuti ngati angawasonyeze iwo njira yomwe idatsogolera ku dziko la Nefi kuti apereka kwa iwo miyoyo yawo ndi ufulu wawo.

37 Koma Alima atawasonyeza iwo njira yomwe idatsogolera ku dziko la Nefi Alamani sadasunge lonjezo lawo; koma adaika alonda mozungulira dziko la Helamu, pa Alima ndi abale ake.

38 Ndipo otsala awo adapita ku dziko la Nefi; ndipo ena a iwo adabwelera ku dziko la Helamu, ndi kubweretsanso akazi ndi ana a alonda amene adatsala m’dzikomo.

39 Ndipo mfumu ya Alamani idali itapereka kwa Amuloni kuti akhale mfumu ndi wolamulira pa anthu ake, amene adali m’dziko la Helamu; komabe sadayenere kukhala ndi mphamvu yochitira chirichonse chotsutsana ndi zofuna za mfumu ya Alamani.