Malembo Oyera
Mosiya 13


Mutu 13

Abinadi atetezedwa ndi mphamvu ya umulungu—Aphunzitsa Malamulo Khumi—Chipulumutso sichimabwera ndi lamulo la Mose lokha—Mulungu Mwiniwake adzachita chitetezero ndi kuwombola anthu Ake. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano pamene mfumu idamva mawu awa, adati kwa ansembe ake, Chotsani munthu uyu, ndipo mumuphe; pakuti tipanga naye chiyani, pakuti ndi wamisala.

2 Ndipo adayimilira, ndi kuyesera kuyika manja awo pa iye; koma iye adawakaniza, ndipo adati kwa iwo;

3 Musandigwire, pakuti Mulungu adzakukanthani ngati muika manja anu pa ine; pakuti sindidafikitse mawu amene Ambuye adandituma kuti ndipereke; kapena sindidakuuzeni chimene mudandipempha kuti ndikuuzeni; kotero, Mulungu sadzalora kuti ine ndionongedwe pa nthawi ino.

4 Koma ndiyenera kukwaniritsa malamulo amene Mulungu wandilamulira; ndipo chifukwa ndakuuzani choonadi, mwakwiya nane. Ndiponso, chifukwa ndayankhula mawu a Mulungu inu mwandiweruza ine kuti ndine wamisala.

5 Tsopano zidachitika atatha Abinadi kuyankhula mawu awa kuti anthu a mfumu Nowa sadayerekeze kuika manja awo pa iye; pakuti Mzimu wa Ambuye udali pa iye; ndipo nkhope yake idawala ndi kunyezimira kwakukulu, ngati monga Mose adachitira m’phiri la Sinai, poyankhula ndi Ambuye.

6 Ndipo adayankhula ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa Mulungu; ndipo adapitiriza mawu ake, nati:

7 Mukuona kuti mulibe mphamvu zondipha, kotero ndikumaliza uthenga wanga. Inde, ndipo ndikuona kuti zikukuchekani m’mitima yanu chifukwa ndikukuuzani zoona za mphulupulu zanu.

8 Inde, ndipo mawu anga akukudzadzani ndi kudabwitsika ndi kuzizwa, ndi mkwiyo.

9 Koma ndikumaliza uthenga wanga; ndipo ndikamaliza zilibe kanthu kumene nditapite, ngati kudzakhala kuti ndapulumutsidwa.

10 Koma izi ndikukuuzani, zomwe mutandichite, zikatha izi, zidzakhala ngati choimilira ndi chithunzithunzi cha zinthu zimene ziri nkudza.

11 Ndipo tsopano ine ndikuwerengerani inu otsala a malamulo a Mulungu, pakuti ndikuona kuti sadalembedwe m’mitima yanu; ine ndikuona kuti inu mwaphunzira ndi kuphunzitsa mphulupulu gawo lalikulu la moyo wanu.

12 Ndipo tsopano, mukukumbukira kuti ndidati kwa inu: Usadzipangire iwe fano losema, kapena chifaniziro chiri chonse cha zinthu za m’mwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko.

13 Ndiponso: Usazigwadire, kapena kuzitumikira; pakuti Ine Ambuye Mulungu wako ndine Mulungu wansanje; kulanga ana mphulupulu za atate, kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi wa iwo akundida Ine;

14 Ndi kuwachitira chifundo zikwizikwi a iwo amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.

15 Usatchule dzina la Ambuye Mulungu wako pachabe; pakuti Ambuye sadzamuyesa osalakwa iye amene atchula pachabe dzina lake.

16 Kumbukira tsiku la sabata, likhale lopatulika.

17 Masiku asanu ndi limodzi udzigwira ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse;

18 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, Sabata la Ambuye Mulungu wako, usamagwire ntchito ili yonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena kapolo wako wamwamuna, kapena kapolo wako wamkazi, kapena ng’ombe zako, kapena mlendo ali mzipata zako;

19 Pakuti m’masiku asanu ndi limodzi Ambuye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili mmenemo; kotero Ambuye adadalitsa tsiku la sabata, nalipatula.

20 Lemekeza atate ako ndi amako, kuti masiku ako achuluke m’dziko limene Ambuye Mulungu wako wakupatsa iwe.

21 Usaphe.

22 Usachite chigololo. Usabe.

23 Usachitire mnzako umboni onama.

24 Usasilire nyumba ya mnansi wako, usasilire mkazi wa mnansi wako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kali konse ka mnansi wako.

25 Ndipo zidachitika kuti Abinadi atatsiriza kunena mawu awa iye adanena kwa iwo: Kodi inu mwaphunzitsa anthu awa kuti akufunika kusunga ndikuchita zinthu zonsezi kuti asunge malamulo awa?

26 Ndinena kwa inu, Ayi; pakuti mukadakhala, Ambuye sakadandichititsa ine kubwera ndi kunenera zoipa za anthu awa.

27 Ndipo tsopano mwanena kuti chipulumutso chimadza mwa lamulo la Mose. Ndinena kwa inu kuti kuli koyenera kuti musunge lamulo la Mose; koma ndinena kwa inu, kuti idzafika nthawi imene sikudzakhalanso koyenera kusunga lamulo la Mose.

28 Komanso, ndinena kwa inu, kuti chipulumutso sichimabwera mwa lamulo lokha; ndipo pakadapanda chitetezero, chimene Mulungu mwiniyo adzachipanga chifukwa cha machimo ndi mphulupulu za anthu ake, kuti iwo akuyenera kuwonongeka mosapeweka, osatengera za lamulo la Mose.

29 Ndipo tsopano ine ndinena kwa inu kuti chidali choyenerera kuti kukhale lamulo loperekedwa kwa ana a Israeli, inde, ngakhale lamulo lolimba kwambiri; pakuti adali anthu osamvera, ofulumira kuchita mphulupulu; ndi ochedwa kukumbukira Ambuye Mulungu wawo;

30 Kotero kudali lamulo lidapatsidwa kwa iwo, inde lamulo la machitidwe ndi miyambo; lamulo limene adayenera kulisunga mosamalitsa tsiku ndi tsiku, kuwasunga iwo m’kukumbukira Mulungu ndi ntchito yawo kwa Iye.

31 Koma taonani, ndikunena kwa inu, kuti zinthu zonse izi zidali zoimira za zinthu zimene zili nkudza.

32 Ndipo tsopano, kodi iwo adamvetsetsa lamulo? Ndikunena kwa inu, Ayi, sadamvetsetse onse lamulo; ndipo izi chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo; pakuti iwo sadamvetse kuti sipakadatheka kupulumutsidwa munthu aliyense kupatulapo kudzera mu chiwombolo cha Mulungu.

33 Pakuti taonani, kodi Mose sadanenere kwa iwo za kubwera kwa Mesiya, ndi kuti Mulungu adzawombola anthu ake? Inde, ndipo ngakhale aneneri onse amene adanenera chiyambire dziko lapansi—kodi sadayankhule mochuluka kapena mochepera pa zinthu izi?

34 Kodi sadanene kuti Mulungu adzatsikira pakati pa ana a anthu, nadzatenga maonekedwe a munthu, ndi kupita pamaso pa dziko lapansi ndi mphamvu zazikulu?

35 Inde, ndipo sadanene kuti iye adzachititsa chiukitso cha akufa, ndi kuti iye, iyemwini, adzaponderezedwa ndi kusautsidwa?