Malembo Oyera
Mosiya 4


Mutu 4

Mfumu Benjamini ipitiriza kuyankhula kwake—Chipulumutso chimabwera chifukwa cha Chitetezero—Khulupilirani mwa Mulungu kuti mupulumutsidwe—Pezani kukhululukidwa kwa machimo anu kudzera m’kukhulupirika—Perekani chuma chanu kwa osauka—Chitani zonse mwanzeru ndi dongosolo. Mdzaka dza pafupifupi 124 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti pamene mfumu Benjamini idatha kuyankhula mawu amene adaperekedwa kwa iyo ndi mngelo wa Ambuye, kuti iyo adayang’ana maso ake mozungulira khamulo, ndipo taonani, adagwa pansi, pakuti kuopa Ambuye kudawagwera iwo.

2 Ndipo iwo adali atadziona okha mu mkhalidwe wawo wakuthupi, ngakhale wocheperapo kuposa fumbi la dziko lapansi. Ndipo onse adafuula mokweza ndi mawu amodzi, nanena: O tichitireni chifundo, ndipo pangitsani mwazi wotetezera wa Khristu kuti tilandire chikhululukiro cha machimo athu, ndi mitima yathu iyeretsedwe; pakuti tikukhulupilira mwa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zinthu zonse; amene adzatsika pakati pa ana a anthu.

3 Ndipo zidachitika kuti atatha kuyankhula mawu awa Mzimu wa Ambuye udadza pa iwo, ndipo adadzadzidwa ndi chisangalalo, atalandira chikhululukiro cha machimo awo, ndi kukhala ndi mtendere wa chikumbu mtima, chifukwa cha chikhulupiliro choposa chimene iwo adali nacho mwa Yesu Khristu amene ayenera kudzabwera, molingana ndi mawu amene mfumu Benjamini adayankhula kwa iwo.

4 Ndipo mfumu Benjamini idatsegulanso pakamwa pake ndipo adayamba kuyankhula kwa iwo, kuti: Abwenzi anga ndi abale anga, afuko langa ndi anthu anga, ndidzaitaniranso chidwi chanu, kuti inu mukamve ndi kumvetsetsa otsala a mawu anga amene ndidzayankhula kwa inu.

5 Pakuti, taonani, ngati chidziwitso cha ubwino wa Mulungu pa nthawi ino chakudzutsani inu kuti mumve kuti ndinu wopanda pake, ndi mkhalidwe wanu wopanda pake ndi wakugwa—

6 Ndikunena kwa inu, ngati mwazindikira ubwino wa Mulungu; ndi mphamvu zake zosayerekezeka, ndi nzeru zake, ndi chipiliro chake, ndi kuleza mtima kwake kwa ana a anthu; ndiponso, chitetezero chimene chidakonzedwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi, kotero kuti chipulumutso chifike kwa iye amene akhulupilira Ambuye; ndipo ayenera kukhala wakhama mukusunga malamulo ake, ndi kupitiriza m’chikhulupiliro kufikira mapeto a moyo wake, ine ndikutanthauza moyo wa thupi lachivundi—

7 Ndikunena, kuti uyu ndi munthu amene amalandira chipulumutso, kudzera mu chitetezero chimene chidakonzedwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi kwa anthu wonse, amene adalipo kuyambira pa kugwa kwa Adamu, kapena amene ali, kapena amene adzakhala, ngakhale ku mapeto a dziko.

8 Ndipo iyi ndi njira imene chipulumutso chimadzera. Ndipo palibe chipulumutso china koma ichi chimene chayankhulidwa; ndiponso palibe chikhalidwe china chimene munthu angapulumutsidwe nacho kupatula chikhalidwe chimene ine ndakuwuzani inu.

9 Khulupilirani mwa Mulungu; khulupilirani kuti iye ali, ndi kuti adalenga zinthu zonse, kumwamba ndi padziko lapansi; khulupilirani kuti ali ndi nzeru zonse, ndi mphamvu zonse, kumwamba ndi padziko lapansi; khulupilirani kuti munthu sangamvetse zinthu zonse zimene Ambuye angamvetse.

10 Ndiponso, khulupilirani kuti mukuyenera kulapa machimo anu ndi kuwasiya, ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu; ndipo mupempheni moona mtima kuti akukhululukireni; ndipo tsopano, ngati mukukhulupilira zinthu zonsezi onetsetsani kuti mukuzichita.

11 Ndipo ndinenanso kwa inu monga ndanena kale, kuti monga mwafikira pa chidziwitso cha ulemelero wa Mulungu; kapena ngati mwadziwa za ubwino wake, ndipo mwalawa za chikondi chake, ndipo mwalandira chikhululukiro cha machimo anu; chimene chidzetsa chisangalalo chachikulu chotero m’miyoyo yanu; kotero ine ndikufuna kuti inu mukumbukire, ndipo sungani mukukumbukira nthawi zonse; ukulu wa Mulungu, ndi kupanda pake kwanu, ndi ubwino ndi kuleza mtima kwake kwa inu, zolengedwa zopanda pake, ndipo dzichepetseni ngakhale mu kuya kwa kudzichepetsa, kuyitana pa dzina la Ambuye tsiku ndi tsiku, ndi kuima mokhazikika m’chikhulupiliro cha chimene chirinkudza, chimene chidayankhulidwa ndi pakamwa pa mngelo.

12 Ndipo taonani, ine ndikunena kwa inu kuti ngati muchita izi inu mudzasangalala nthawi zonse, ndi kudzadzidwa ndi chikondi cha Mulungu, ndi kusunga chikhululukiro cha machimo anu nthawi zonse; ndipo mudzakula m’chidziwitso cha ulemelero wa iye amene adakulengani, kapena m’chidziwitso cha izo zimene ziri zolungama ndi zoona.

13 Ndipo simudzakhala ndi maganizo wovulazana wina ndi mzake, koma kukhala mwamtendere, ndi kupereka kwa aliyense molingana ndi zomwe zikuyenera kwa iye.

14 Ndipo simudzalora ana anu kuti akhale ndi njala, kapena amaliseche; ngakhalenso inu simudzalora kuti iwo akalakwire malamulo a Mulungu, ndi kumenyana ndi kukangana wina ndi mzake, ndi kutumikira mdyerekezi, amene ali mbuye wa tchimo, kapena amene ali mzimu oipa amene adayankhulidwa ndi makolo athu, iye kukhala mdani wa chilungamo chonse.

15 Koma mudzawaphunzitsa kuyenda m’njira za choonadi ndi kudziletsa; mudzawaphunzitsa kukondana wina ndi mzake, ndi kutumikirana wina ndi mzake.

16 Ndiponso, inu eni nokha mudzathandiza iwo amene akusowa thandizo lanu; mudzapereka chuma chanu kwa iye amene ali osowa; ndipo simudzalora kuti opemphapempha achite chopempha chake kwa inu pachabe, ndi kumuthamangitsa kuti awonongeke.

17 Mwina mudzanena kuti: Munthuyo wadzibweretsera chisoni chake; choncho ndichotsa dzanja langa, ndipo sindidzapereka kwa iye chakudya changa, kapena kupereka kwa iye chuma changa kuti asazunzike, pakuti zilango zake ndi zolungama—

18 Koma ndikunena kwa inu, O munthu, amene achita izi ali ndi chifukwa chachikulu cha kulapa; ndipo kupatula alape zimene adachita adzawonongeka kwamuyaya, ndipo alibe chidwi ndi ufumu wa Mulungu.

19 Pakuti taonani, kodi sitiri tonse opempha? Kodi ife tonse sitidalira pa Munthu m’modzi, ngakhale Mulungu, pa zinthu zonse zimene tiri nazo, zonse chakudya ndi zovala, ndi golidi, ndi siliva, ndi chuma chonse chimene tiri nacho cha mitundu yonse?

20 Ndipo taonani, ngakhale pa nthawi ino, inu mwakhala mukuyitana pa dzina lake, ndi kumapempha chikhululukiro cha machimo anu. Ndipo kodi adalora kuti inu mukapemphe pachabe? Ayi; iye watsanulira Mzimu wake pa inu, ndipo wapangitsa kuti mitima yanu idzadzidwe ndi chisangalalo, ndipo wapangitsa kuti milomo yanu itsekedwe kuti musapeze zonena, kotero kuti chisangalalo chanu chidali chachikulu kwambiri.

21 Ndipo tsopano, ngati Mulungu, amene adakulengani inu, amene mumadalira pa moyo wanu ndi zonse zomwe muli nazo ndi zomwe muli, amakupatsani chilichonse chimene mumapempha chomwe chili cholondola, ndi chikhulupiliro, ndikukhulupilira kuti mudzalandira, O ndiye, chomwecho mukuyenera kugawirana chuma chomwe muli nacho wina ndi mzake.

22 Ndipo ngati muweruza munthu amene apereka pempho lake kwa inu chifukwa cha chuma chanu kuti asatayike, ndi kumutsutsa, kudzakhala kolungama kutsutsidwa kwakukulu motani nanga kwanu chifukwa chokaniza chuma chanu, chomwe sichili chanu, koma cha Mulungu amene moyo wanunso uli wake; ndipo komabe simupempha kanthu, kapena kulapa pa chimene mudachichita.

23 Ndikunena kwa inu, tsoka likhala kwa munthu ameneyo, chifukwa chuma chake chidzawonongeka pamodzi ndi iye; ndipo tsopano, ine ndikunena zinthu izi kwa iwo amene ali olemera monga pa zinthu za dziko lino.

24 Ndipo kachiwiri, ndikunena kwa osauka, inu amene mulibe ndipo komabe muli nazo zokwanira, kuti mukhalebe tsiku ndi tsiku; Ndikutanthauza inu nonse amene mumakana opemphapempha, chifukwa mulibe; Ndikadakonda kuti mudzinena m’mitima mwanu kuti: Sindipereka chifukwa ndilibe, koma ndikadapereka ndikadakhala nazo.

25 Ndipo tsopano, ngati munena ichi m’mitima yanu mukhala opanda cholakwa; kupanda apo ndinu wotsutsidwa; ndipo kutsutsidwa kwanu kuli kolungama chifukwa mukusilira chimene simudachilandire.

26 Ndipo tsopano, chifukwa cha zinthu izi zimene ndayankhula kwa inu—kapena, chifukwa cha kusunga chikhululukiro cha machimo anu tsiku ndi tsiku, kuti mukayende opanda cholakwa pamaso pa Mulungu—ndikufuna kuti mugawireko chuma chanu kwa osauka, munthu aliyense molingana ndi zomwe ali nazo, monga kudyetsa anjala, kuveka amaliseche, kuyendera odwala ndi kupereka chithandizo cha mpumulo wawo, kuuzimu ndi mwakuthupi, malinga ndi zofuna zawo.

27 Ndipo onani kuti zinthu zonsezi zachitidwa mwanzeru ndi dongosolo; pakuti sikuyenera kuti munthu athamange koposa mphamvu zake. Ndipo kachiwiri, kuli koyenera kuti akhale wakhama, kuti mwakutero akalandire mphotho; kotero, zinthu zonse zikuyenera kuchitidwa mwadongosolo.

28 Ndipo ine ndikufuna kuti inu mukumbukire, kuti aliyense wa inu amene abwereka kwa mnansi wake akuyenera kubweza chinthu chimene iye adabwereka; monga wavomerezera, kapena udzachita tchimo; ndipo kapena udzachititsa mnasi wakoyo kuti achimwenso.

29 Ndipo potsiriza, sindingathe kukuuzani inu zinthu zonse zimene mungachitire uchimo; pakuti pali njira zambiri ndi zochuluka, ngakhale zambiri kotero kuti sindingathe kuziwerenga.

30 Koma izi zambiri ndikhonza kukuuzani inu, kuti ngati simudziyang’anira nokha, ndi maganizo anu, ndi mawu anu, ndi ntchito zanu, ndi kusunga malamulo a Mulungu, ndi kupitirizabe m’chikhulupiliro cha zomwe mudamva za kubwera kwa Ambuye wathu, ngakhale mpaka kumapeto kwa moyo wanu, muyenera kuwonongeka. Ndipo tsopano, Iwe munthu, kumbukira, ndipo usawonongeke.

Print