Malembo Oyera
Mosiya 9


Zolemba za Zenifi—Mbiri ya anthu ake, kuchokera nthawi imene adachoka m’dziko la Zarahemula mpaka nthawi imene adapulumutsidwa kuchokera m’manja mwa Alamani.

Zophatikizidwa mumitu 9 mpaka 22.

Mutu 9

Zenifu atsogolera gulu kuchokera ku Zarahemula kukatenga dziko la Lehi-Nefi—Mfumu ya Lamani iwaloleza iwo kuti alandire dzikolo—Pali nkhondo pakati pa Alamani ndi anthu a Zenifu. Mdzaka dza pafupifupi 200–187 Yesu asadabadwe.

1 Ine, Zenifu, nditaphunzitsidwa mu chinenero chonse cha Anefi, ndi kukhala ndi chidziwitso cha dziko la Nefi, kapena cha dziko la cholowa choyamba cha makolo athu, ndi kutumizidwa monga kazitape pakati pa Alamani kuti ndikazonde ankhondo awo, kuti gulu lathu lankhondo lidze pa iwo ndi kuwawononga—koma pamene ndidaona chimene chidali chabwino pakati pawo ndidafuna kuti iwo asawonongedwe.

2 Kotero, ndidakangana ndi abale anga m’chipululu, pakuti ndidafuna kuti olamulira wathu achite nawo mgwirizano; koma iye pokhala munthu ouma mtima ndi waludzu la mwazi adalamulira kuti ndiphedwe; koma ndidapulumutsidwa ndi kukhetsa mwazi wambiri; pakuti atate adamenyana ndi atate, ndipo m’bale kutsutsana ndi m’bale, kufikira unyinji wa ankhondo athu udawonongedwa m’chipululu; ndipo tidabwelera, iwo a ife amene tidasiyidwa, ku dziko la Zarahemula, kuti tikafotokoze nkhani imeneyi kwa akazi awo ndi ana awo.

3 Ndipo komabe, pokhala wachangu chopambana kuti ndilandire dziko la makolo athu, ndidasonkhanitsa ochuluka omwe adali kufuna kupitako kukatenga dzikolo, ndipo tidayambanso ulendo wathu opita kuchipululu kupita ku dzikolo; koma tidakanthidwa ndi njala ndi masautso owawa; pakuti tidali ochedwa kukumbukira Ambuye Mulungu wathu.

4 Komabe, titayendayenda kwa masiku ambiri m’chipululu tidamanga mahema athu m’malo amene abale athu adaphedwa, amene adali pafupi ndi dziko la makolo athu.

5 Ndipo zidachitika kuti ine ndidapitanso ndi azibambo anga anayi mu mzindawo, kwa mfumu, kuti ine ndidziwe za maganizo a mfumuyo, ndi kuti ine ndithe kudziwa ngati ine ndingathe kulowa ndi anthu anga ndi kutenga dzikolo mwamtendere.

6 Ndipo ndidapita kwa mfumuyo; ndipo adapangana nane kuti nditha kutenga dziko la Lehi-Nefi, ndi dziko la Shilomu.

7 Ndipo iye adalamuranso kuti anthu ake achoke m’dzikolo, ndipo ine ndi anthu anga tidalowa m’dzikolo kuti tikalitenge.

8 Ndipo tidayamba kumanga zomangamanga, ndi kukonza makoma a mzindawo, inde, ngakhale mpanda wa mzinda wa Lehi-Nefi, ndi mzinda wa Shilomu.

9 Ndipo tidayamba kulima nthaka, inde, ngakhale ndi mbewu zamitundu yonse, ndi mbewu za chimanga, ndi tirigu, ndi barele, ndi nisi, ndi sheyumu, ndi mbewu za mitundu yonse ya zipatso; ndipo tidayamba kuchulukana ndi kuchita bwino m’dzikolo.

10 Tsopano kudali kuchenjera ndi chinyengo cha mfumu Lamani, kutenga anthu anga mu ukapolo, kuti adapereka dzikolo kuti tilitenge.

11 Kotero zidachitika, kuti titakhala m’dzikomo kwa nthawi ya dzaka khumi ndi ziwiri kuti mfumu Lamani adayamba kusakhazikika, kuopa kuti mwa njira ina iriyonse anthu anga akakula mu mphamvu m’dzikolo, ndipo kuti sakadatha kuwagonjetsa iwo ndi kuwabweretsa iwo mu ukapolo.

12 Tsopano iwo adali anthu aulesi ndi opembedza mafano; chifukwa chake adafuna kutitengera ife mu ukapolo; kuti adzitha kudzikhutitsa okha ndi ntchito za manja athu; inde, kuti iwo athe kumadzidyetsa pa ziweto za kuminda yathu.

13 Kotero zidachitika kuti mfumu Lamani adayamba kuutsa anthu ake kuti alimbane ndi anthu anga; kotero kudayamba kukhala nkhondo ndi mikangano m’dzikolo.

14 Pakuti, m’chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wanga m’dziko la Nefi, kutali kumwera kwa dziko la Shilomu, pamene anthu anga adali kumwetsa ndi kudyetsa ziweto zawo, ndi kulima minda yawo, khamu lalikulu la Alamani lidadza pa iwo ndipo adayamba kuwapha, ndi kuwalanda ziweto zawo, ndi chimanga cha m’minda mwawo

15 Inde, ndipo zidachitika kuti iwo adathawa, onse amene sadagonjetsedwe, ngakhale mu mzinda wa Nefi, ndipo adaitanira pa ine kuti ndiwateteze.

16 Ndipo zidachitika kuti ndidawapangira zida za mauta, ndi mivi, ndi malupanga, ndi dzikwanje, ndi mikwingwiri, ndi gulaye, ndi mitundu yonse ya zida zimene tikadapanga, ndipo ine ndi anthu anga tidapita kukamenyana ndi Alamani kunkhondo.

17 Inde, mu mphamvu ya Ambuye tidapita kukamenyana ndi Alamani; pakuti ine ndi anthu anga tidalilira mwamphamvu kwa Ambuye kuti atipulumutse m’manja mwa adani athu; pakuti tidadzutsidwa m’kukumbukira chiwombolo cha makolo athu.

18 Ndipo Mulungu adamva kulira kwathu ndipo adayankha mapemphero athu; ndipo tidapita mu mphamvu yake; inde, ife tidapita kukamenyana ndi Alamani, ndipo usana umodzi ndi usiku tidapha zikwi zitatu mphambu makumi anayi kudza atatu; tidawapha mpaka tidawatulutsa m’dziko lathu.

19 Ndipo ine, mwini, ndi manja anga omwe, ndidathandiza kuyika akufa awo. Ndipo taonani, ku chisoni chathu chachikulu ndi kulira, mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi zinayi za abale athu adaphedwa.