Malembo Oyera
Mosiya 26


Mutu 26

Mamembala wochuluka a mu Mpingo atsogozedwa mu uchimo ndi wosakhulupilira—Alima alonjezedwa moyo wamuyaya—Amene alapa ndi kubatizidwa apeza chikhululukiro—Mamembala a mpingo a mu uchimo amene alapa ndi kuvomereza kwa Alima ndi kwa Ambuye adzakhululukidwa; kupatula apo, iwo sadzawerengedwa pakati pa anthu a Mpingo. Mdzaka dza pafupifupi 120–100 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti padali ambiri a m’badwo wa achinyamata amene sadathe kumvetsetsa mawu a mfumu Benjamini, pokhala ana ang’ono pa nthawi imene iye adayankhula kwa anthu ake; ndipo sadakhulupilire miyambo ya makolo awo.

2 Iwo sadakhulupilire zimene zidanenedwa zokhudza kuuka kwa akufa, ndipo sadakhulupilire za kubwera kwa Khristu.

3 Ndipo tsopano chifukwa cha kusakhulupilira kwawo sadathe kumvetsetsa mawu a Mulungu; ndipo mitima yawo idawumitsidwa.

4 Ndipo sadafune kubatizidwa; ngakhalenso iwo sadafune kulowa mu mpingo. Ndipo adali anthu osiyana pa chikhulupiliro chawo, ndipo adakhalabe choncho kuyambira pamenepo, ngakhale mu chikhalidwe chawo chathupi ndi uchimo; pakuti sadafune kuitana pa Ambuye Mulungu wawo.

5 Ndipo tsopano mu ulamuliro wa Mosiya iwo sadafike theka la kuchuluka monga anthu a Mulungu; koma chifukwa cha kugawanikana pakati pa abale iwo adachulukana.

6 Pakuti zidachitika kuti iwo adanyengeza ambiri ndi mawu awo osyasyalika, amene adali mu mpingo, ndipo adawapangitsa iwo kuchita machimo ambiri; kotero kudali koyenera kuti amene adachita tchimo, womwe adali mu mpingo, adayenera kuchenjezedwa ndi mpingo.

7 Ndipo zidachitika kuti adatengedwa pamaso pa ansembe, ndi kuperekedwa kwa ansembe ndi aphunzitsi; ndipo ansembe adawabweretsa iwo pamaso pa Alima, yemwe adali mkulu wansembe.

8 Tsopano mfumu Mosiya adapereka kwa Alima ulamuliro pa mpingo.

9 Ndipo zidachitika kuti Alima sadadziwe zokhudza iwo; koma padali mboni zambiri zowatsutsa iwo; inde, anthu adaimilira ndi kuchitira umboni za mphulupulu zawo zochuluka.

10 Tsopano padalibe kanthu kotere kamene kadachitikapo mu mpingo; kotero Alima adavutika mu mzimu wake, ndipo adachititsa kuti abweretsedwe pamaso pa mfumu.

11 Ndipo iye adati kwa mfumu: Taonani, apa pali ambiri amene tawabweretsa pamaso panu, amene akutsutsidwa ndi abale awo; inde, ndipo atengedwa mu mphulupulu zosiyanasiyana. Ndipo sakulapa mphulupulu zawo; kotero tawabweretsa kwa Inu, kuti muwaweruze monga mwa zolakwa zawo.

12 Koma mfumu Mosiya adati kwa Alima: Taona, sindiwaweruza iwo; kotero ndiwapereka m’manja mwako kuti aweruzidwe.

13 Ndipo tsopano mzimu wa Alima udavutikanso; ndipo Iye adapita kukafunsa kwa Ambuye chimene iye akuyenera kuchita zokhudza nkhani imeneyi, pakuti ankaopa kuti angachite zoipa pamaso pa Mulungu.

14 Ndipo zidachitika kuti atatsanulira moyo wake onse kwa Mulungu, mawu a Ambuye adadza kwa iye, kuti:

15 Odala ndi iwe, Alima, ndipo wodala ali iwo amene adabatizidwa m’madzi a Mormoni. Ndiwe odala chifukwa cha chikhulupiliro chako chopambana m’mawu wokha a mtumiki wanga Abinadi.

16 Ndipo wodala ali iwo chifukwa cha chikhulupiliro chawo chopambana m’mawu wokha amene iwe udayankhula kwa iwo.

17 Ndipo odala iwe chifukwa iwe wakhazikitsa mpingo pakati pa anthu awa; ndipo adzakhazikitsidwa, ndipo adzakhala anthu anga.

18 Inde, wodala anthu awa amene akufuna kunyamula dzina langa; pakuti adzatchedwa m’dzina langa; ndipo iwo ali anga.

19 Ndipo chifukwa chakuti wandifunsa za wolakwa, ndiwe odala.

20 Ndiwe mtumiki wanga; ndipo ndikupangana ndi iwe kuti udzakhala ndi moyo wamuyaya; ndipo udzanditumikira Ine, ndipo udzapita m’dzina langa, ndi kusonkhanitsa nkhosa zanga.

21 Ndipo iye amene adzamva mawu anga adzakhala nkhosa yanga; ndipo iye mudzamulandira mu mpingo, ndipo inenso ndidzamulandira.

22 Pakuti taona, uwu ndi mpingo wanga; aliyense amene abatizidwa adzabatizidwa mu kulapa. Ndipo yense amene udzamulandira adzakhulupilira dzina langa; ndipo ndidzamukhululukira mwa ulere.

23 Pakuti ine ndine amene ndatenga pa ine machimo a dziko lapansi; pakuti Ine ndine amene ndidawalenga iwo; ndipo ndine amene ndimapereka malo kwa iye amene akhulupilira kufikira chimaliziro pa dzanja langa lamanja.

24 Pakuti taona, m’dzina langa iwo akuyitanidwa; ndipo ngati andidziwa ine iwo adzabwera, ndipo adzakhala ndi malo amuyaya pa dzanja langa lamanja.

25 Ndipo zidzachitika kuti pamene lipenga lachiwiri lidzawomba, pamenepo iwo amene sadandidziwe Ine adzabwera, ndipo adzaima pamaso panga.

26 Ndipo pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu wawo, kuti Ine ndine Muwomboli wawo; koma sadawomboledwe.

27 Ndipo pamenepo ndidzavomereza kwa iwo kuti sindidawadziwe konse; ndipo adzapita kumoto wosatha wokonzedwera mdyerekezi ndi angelo ake.

28 Kotero ndikunena kwa iwe, kuti iye amene sadzamva mawu anga, yemweyo iwe siudzamulandira mu mpingo wanga, pakuti iye sindidzamulandira pa tsiku lomaliza.

29 Kotero ndikunena kwa iwe, Pita; ndipo aliyense amene alakwira ine, iyeyu iwe udzamuweruze monga mwa zolakwa zimene adazichita; ndipo ngati avomereza machimo ake pamaso pa iwe ndi ine, ndi kulapa moona mtima kwa mtima wake, iyeyu udzamukhululukira, ndipo inenso ndidzamukhululukira.

30 Inde, ndipo nthawi zonse pamene anthu anga alapa ndidzawakhululukira zolakwa zawo zotsutsana ndi ine.

31 Ndipo inunso mudzakhululukirana zolakwa zanu wina ndi mzake; pakuti indetu ndikunena kwa iwe, iye amene sakhululukira zolakwa za mnansi wake pamene akunena kuti iye walapa, yemweyo wadzibweretsa yekha pansi pa kutsutsidwa.

32 Tsopano ndikunena kwa iwe, Pita; ndipo aliyense amene sadzalapa machimo ake yemweyo sadzawerengedwa pakati pa anthu anga; ndipo izi zikuyenera kudzasungidwa kuyambira nthawi ino kupita mtsogolo.

33 Ndipo zidachitika pamene Alima adamva mawu awa adawalemba kuti akathe kukhala nawo, ndi kuti akathe kuweruza anthu a mpingo umenewo molingana ndi malamulo a Mulungu.

34 Ndipo zidachitika kuti Alima adapita naweruza iwo amene adatengedwa mu mphulupulu, monga mwa mawu a Ambuye.

35 Ndipo aliyense amene adalapa machimo awo ndi kuwavomereza, iwo adawawerenga pakati pa anthu a mpingo;

36 Ndipo iwo amene sadavomereze machimo awo ndi kulapa mphulupulu zawo, womwewo sadawerengedwe mwa anthu a mpingo, ndipo maina awo adafufutidwa.

37 Ndipo zidachitika kuti Alima adalamulira zochitika zonse za mpingo ndipo adayambanso kukhala ndi mtendere ndi kuchita bwino kwambiri m’zochitika za mpingo, kuyenda mosamala pamaso pa Mulungu, kulandira ambiri, ndi kubatiza ambiri.

38 Ndipo tsopano zinthu zonsezi Alima ndi antchito anzake adachita amene adali woyang’anira mpingo, kuyenda mu khama lonse, kuphunzitsa mawu a Mulungu m’zinthu zonse, kuzunzika mitundu yonse ya masautso, kuzunzidwa ndi onse amene sadali a mpingo wa Mulungu.

39 Ndipo iwo adachenjeza abale awo; ndipo iwo adachenjezedwanso, aliyense ndi mawu a Mulungu, malingana ndi machimo ake, kapena machimo amene iye adachita, polamulidwa ndi Mulungu kuti apemphere mosalekeza, ndi kuyamika m’zinthu zonse.

Print