Mutu 14
Yesaya ayankhula mwaumesiya—Kunyozedwa kwa Mesiya ndi zowawa zikhazikitsidwa—Iye apanga moyo Wake kukhala nsembe ya uchimo ndi kupanga chipembedzero cha olakwa—Fananitsani ndi Yesaya 53. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.
1 Inde, ngakhale Yesaya sakunena kuti: Ndani wakhulupilira mbiri yathu, ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?
2 Pakuti adzaphuka pamaso pake ngati mphukira; ndi monga muzu m’nthaka youma; alibe maonekedwe kapena kukongola; ndipo pamene tidzamuona palibe kukongola kuti timukhumbire.
3 Iye adanyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi omvetsetsa zowawa; ndipo zidali ngati kuti tidabisa nkhope zathu kwa iye; iye adanyozedwa, ndipo ife sitidamulemekeze iye.
4 Zoonadi iye adanyamula zowawa zathu, nanyamula zisoni zathu; komabe ife tidamuyesa omenyedwa, okanthidwa ndi Mulungu, ndi ozunzidwa.
5 Koma iye adalasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, iye adavulazidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango cha mtendere wathu chidali pa Iye; ndipo ndi mabala ake ife tachiritsidwa.
6 Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera; tapambuka yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Ambuye adaika pa Iye mphulupulu za ife tonse.
7 Iye adaponderezedwa, ndipo adazunzidwa, koma sadatsegule pakamwa pake; watengedwa ngati mwana wa nkhosa wopita kukaphedwa, ndi ngati mwana wankhosa ali wosayankhula pamaso pa omsenga wake, momwemo sadatsegula pakamwa pake.
8 Iye adachotsedwa ku ndende ndi ku chiweruzo; ndipo ndani adzaufotokozera za m’badwo wake? Pakuti adachotsedwa m’dziko la amoyo; chifukwa cha zolakwa za anthu anga adamenyedwa.
9 Ndipo adaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi olemera mu imfa yake; chifukwa sadachite choipa, ndipo m’kamwa mwake mudalibe chinyengo.
10 Koma kudakomera Ambuye kuvulaza iye; iye wamuika mu chisoni; pamene mudzapereka moyo wake nsembe ya uchimo, iye adzaona mbewu yake, adzatalikitsa masiku ake, ndipo chomkondweretsa Ambuye chidzakula m’dzanja lake.
11 Iye adzaona zowawa za moyo wake, ndikudzakhutitsidwa; ndi kudziwa kwake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri; pakuti adzasenza mphulupulu zawo.
12 Kotero ndidzamugawira gawo limodzi ndi akulu; ndipo adzagaŵa zofunkha pamodzi ndi amphamvu; chifukwa adathira moyo wake kuimfa; ndipo adawerengedwa pamodzi ndi olakwa; ndipo adanyamula machimo a ambiri, ndikupembedzera olakwa.