Malembo Oyera
Mosiya 19


Mutu 19

Gideoni afuna kupha Mfumu Nowa—Alamani awukira dziko—Mfumu Nowa azunzika ndi imfa ya moto—Limuhi alamulira monga mfumu yopereka msonkho. Mdzaka dza pafupifupi 145–121 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti gulu lankhondo la mfumu lidabwelera, litafunafuna anthu a Ambuye pachabe.

2 Ndipo tsopano taonani, anthu a mfumu adali ochepa; pokhala atachepetsedwa, ndipo kudayamba kukhala kugawikana pakati pa otsala a anthu.

3 Ndipo gawo laling’ono lidayamba kuopseza mfumu, ndipo kudayamba kukhala mkangano waukulu pakati pawo.

4 Ndipo tsopano padali munthu pakati pawo amene dzina lake lidali Gideoni, ndipo iye pokhala munthu wamphamvu ndi m’dani wa mfumu, kotero iye adasolola lupanga lake, ndipo adalumbira mu mkwiyo wake kuti iye adzapha mfumu.

5 Ndipo zidachitika kuti adamenyana ndi mfumu; ndipo pamene mfumu idaona kuti ikufuna kugonjetsedwa; idathawa, nithamanga, nikwera pa nsanja imene idali pafupi ndi kachisi.

6 Ndipo Gideoni adamulondola ndipo adali pafupi kukwera pansanja kuti aphe mfumu, ndipo mfumu idaponya maso ake mozungulira dziko la Shemuloni; ndipo taonani, gulu lankhondo la Alamani lidali mkati mwa malire a dzikolo.

7 Ndipo tsopano mfumu idafuula mu kuwawidwa kwa moyo wake, kuti: Gideoni, ndileke ine; pakuti Alamani ali pa ife, ndipo adzatiwononga; inde adzawononga anthu anga.

8 Ndipo tsopano mfumu sidali kudera nkhawa kwambiri za anthu ake monga iyo idaliri ndi moyo wake; komabe, Gideoni adayisiyira moyo wake.

9 Ndipo mfumu idalamura anthu kuti athawe pamaso pa Alamani, ndipo nayo iyo mwini idapita patsogolo pawo, ndipo adathawira m’chipululu, ndi akazi awo ndi ana awo.

10 Ndipo zidachitika kuti Alamani adawalondola, ndipo adawapeza, ndikuyamba kuwapha.

11 Tsopano zidachitika kuti mfumu idawauza kuti amuna onse asiye akazi awo ndi ana awo; ndi kuthawa pamaso pa Alamani.

12 Tsopano padali ambiri amene sadawasiye, koma makamaka kukhala ndi kuwonongeka nawo pamodzi. Ndipo otsalawo adasiya akazi awo ndi ana awo ndikuthawa.

13 Ndipo zidachitika kuti awo amene adatsalira ndi akazi awo ndi ana awo adachititsa kuti ana awo aakazi okongola aimilire ndi kuchondelera Alamani kuti asawaphe.

14 Ndipo zidachitika kuti Alamani adali ndi chifundo pa iwo, chifukwa adali atatengeka ndi kukongola kwa azimayi awo.

15 Kotero Alamani adawasiyira miyoyo yawo, ndipo adawatenga iwo akapolo ndipo adawatenga iwo kubwelera nawo ku dziko la Nefi, ndipo adapereka kwa iwo kuti akatenge dzikolo, pansi pa mgwirizano wakuti akapereka mfumu Nowa m’manja mwa Alamani; ndikukapereka chuma chawo, ngakhale theka la zonse adali nazo, theka la golidi wawo, ndi siliva wawo, ndi zinthu zawo zonse zamtengo wapatali; ndipo choncho iwo akuyenera kumakapereka msonkho kwa mfumu ya Alamani chaka ndi chaka.

16 Ndipo tsopano padali m’modzi wa ana a mfumu mwa otengedwa ukapolo; dzina lake lidali Limuhi.

17 Ndipo tsopano Limuhi ankafuna kuti abambo ake asawonongedwe; komabe, Limuhi sadali mbuli pa za mphulupulu za atate ake; iye mwini pokhala munthu wolungama.

18 Ndipo zidachitika kuti Gideoni adatumiza anthu m’chipululu kuti akafufuze mfumu ndi iwo amene adali nayo. Ndipo zidachitika kuti iwo adakumana ndi anthuwo m’chipululu, onse kupatulapo mfumu ndi ansembe ake.

19 Tsopano iwo adali atalumbira m’mitima mwawo kuti adzabwelera ku dziko la Nefi, ndipo ngati akazi awo ndi ana awo aphedwa; ndi iwo amene adali nawo, kuti akafuna kubwenzera chilango, ndi kuwonongeka nawo pamodzi.

20 Ndipo mfumu idawalamula kuti asabwelere; ndipo adakwiya ndi mfumuyo; ndi kuchititsa kuti azunzike, ngakhale ku imfa ya moto.

21 Ndipo adatsala pang’ono kutenganso ansembe ndi kuwapha, ndipo adathawa pamaso pawo.

22 Ndipo zidachitika kuti iwo adali pafupi kubwelera ku dziko la Nefi, ndipo adakumana ndi azibambo a Gideoni. Ndipo azibambo a Gideoni adawafotokozera zonse zidachitikira akazi awo ndi ana awo; ndi kuti Alamani adapereka kwa iwo kuti akatenge dzikolo popereka msonkho kwa Alamani wa theka limodzi la zonse zimene adali nazo.

23 Ndipo anthuwo adauza azibambo a Gideoni kuti adapha mfumu, ndipo ansembe ake adathawira kuchipululu.

24 Ndipo zidachitika kuti atamaliza mwambowo, kuti iwo adabwelera ku dziko la Nefi, akusangalala, chifukwa akazi awo ndi ana awo sadaphedwe; ndipo adamuuza Gideoni zimene adamchitira mfumu.

25 Ndipo zidachitika kuti mfumu ya Alamani idalumbira kwa iwo, kuti anthu ake sadzawapha.

26 Komanso Limuhi, pokhala mwana wa mfumu, atapatsidwa ufumu ndi anthu; adalumbira kwa mfumu ya Alamani kuti anthu ake adzapereka msonkho kwa iye, ngakhale theka limodzi la zonse zomwe adali nazo.

27 Ndipo zidachitika kuti Limuhi adayamba kukhazikitsa ufumu ndi kukhazikitsa mtendere pakati pa anthu ake.

28 Ndipo mfumu ya Alamani idaika alonda kuzungulira dzikolo, kuti akhazike anthu a Limuhi m’dzikomo, kuti iwo asachoke kupita kuchipululu; ndipo iye ankathandiza alonda ake kuchokera mu msonkho umene ankalandira kuchokera kwa Anefi.

29 Ndipo tsopano mfumu Limuhi adakhala ndi mtendere wosatha mu ufumu wake kwa nthawi ya dzaka dziwiri kuti Alamani sadawavutitse iwo kapena kufuna kuwawononga.

Print