Malembo Oyera
Mosiya 5


Mutu 5

Oyera mtima akhala ana aamuna ndi aakazi a Khristu kudzera mu chikhulupiliro—Iwo kenako atchedwa ndi dzina la Khristu—Mfumu Benjamini awalimbikitsa kuti akhale okhazikika ndi osasunthika mu ntchito zabwino. Mdzaka dza pafupifupi 124 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti pamene mfumu Benjamini idayankhula motero kwa anthu ake; idatumiza kwa iwo, kufuna kudziwa za anthu ake ngati akhulupilira mawu amene idawayankhula.

2 Ndipo iwo onse adafuula ndi mawu amodzi, kuti: Inde, ife tikhulupilira mawu onse amene inu mwayankhula kwa ife; komanso, Ife tikudziwa za chitsimikiziro ndi choonadi chawo chifukwa cha Mzimu wa Ambuye Wamphamvu zonse, amene wabweretsa kusintha kwamphamvu mwa ife, kapena m’mitima yathu, kuti tilibenso mitima yofuna kuchita zoipa, koma kuchita zabwino kosalekeza.

3 Ndipo ife, eninso, kudzera mu ubwino opanda malire wa Mulungu, ndi mawonetseredwe a Mzimu wake, tiri ndi malingaliro aakulu a zomwe ziri nkudza; ndipo ngati kudali koyenera, tikadatha kunenera za zinthu zonse.

4 Ndipo ndi chikhulupiliro chimene takhala nacho pa zinthu zimene mfumu yathu yayankhula kwa ife zimene zatifikitsa ife ku chidziwitso chachikulu ichi, chimene ife tikusangalala ndi chisangalalo chachikulu chotere.

5 Ndipo ife tiri okonzeka kulowa m’chipangano ndi Mulungu wathu kuchita chifuniro chake, ndi kumvera malamulo ake mu zonse zimene adzatilamulira, masiku athu onse otsala, kuti tisadzitengere tokha mazunzo osatha, monga adanenera mngelo; kuti tisamwe kuchokera m’chikho cha mkwiyo wa Mulungu.

6 Ndipo tsopano, awa ndi mawu amene mfumu Benjamini idafuna kwa iwo; ndipo kotero adati kwa iwo: Mwanena mawu amene ndidawafuna; ndipo pangano limene mwapanga ndi pangano lolungama.

7 Ndipo tsopano, chifukwa cha pangano limene mwapanga inu mudzatchedwa ana a Khristu, ana ake aamuna ndi aakazi; pakuti taonani, lero iye wakubalani inu muuzimu; pakuti mukunena kuti mitima yanu yasinthidwa kudzera m’chikhulupiliro pa dzina lake; kotero, mwabadwa mwa iye, ndipo mudzakhala ana ake aamuna ndi aakazi.

8 Ndipo pansi pa mutu uwu mwamasulidwa; ndipo palibe mutu wina umene mungakhale nawo mfulu. Palibe dzina lina loperekedwa limene chipulumutso chimabwera; kotero, ndikufuna kuti mutenge pa inu dzina la Khristu, nonse inu amene mwalowa m’pangano ndi Mulungu kuti mukuyenera kukhala omvera mpaka kumapeto kwa moyo wanu.

9 Ndipo zidzachitika kuti yense wakuchita ichi adzapezedwa pa dzanja lamanja la Mulungu; pakuti adzadziwa dzina limene akutchedwa nalo; pakuti adzatchedwa dzina la Khristu.

10 Ndipo tsopano zidzachitika, kuti yense osatenga pa iye dzina la Khristu akuyenera kutchedwa dzina lina; kotero, adzipeza yekha pa dzanja lamanzere la Mulungu.

11 Ndipo ndikufuna kuti inu mukumbukirenso, kuti ili ndilo dzina limene ndidati kuti ndipereke kwa inu lomwe silidzafufutidwa konse, kupatulapo kukhala kudzera m’kulakwitsa; kotero, chenjerani kuti musalakwe, kuti dzinalo lisafufutidwe m’mitima yanu.

12 Ndikunena kwa inu, ndikufuna kuti mukumbukire kusunga dzina lolembedwa nthawi zonse mu mitima yanu; kuti musapezeke pa dzanja lamanzere la Mulungu; koma kuti mumve ndi kudziwa liwu limene mudzaitanidwa nalo; ndiponso, dzina limene adzakuyitanani nalo.

13 Pakuti munthu adziwa bwanji mbuye amene sadamtumikire ndi amene ali mlendo kwa iye, ndipo ali kutali ndi malingaliro ndi zolinga za mtima wake?

14 Ndiponso, kodi munthu atenga bulu wa mnansi wake, ndi kumusunga? Ndikunena kwa inu, Iyayi; sadzalora kuti adye pakati pa zoweta zake; koma adzamthamangitsa, ndi kumponya kunja. Ndikunena kwa inu, kuti momwemonso zidzakhala pakati panu ngati simudziwa dzina limene mumatchedwa nalo.

15 Kotero, ndikufuna kuti mukhale okhazikika ndi osasunthika odzala ndi ntchito zabwino nthawi zonse, kuti Khristu, Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse, atsindikize inu ake, kuti mukatengeredwe kumwamba, kuti mukhale nacho chipulumutso chosatha ndi moyo wamuyaya; mwa nzeru, ndi mphamvu, ndi chilungamo, ndi chifundo cha Iye amene adalenga zonse, zakumwamba ndi zapadziko lapansi, amene ali Mulungu oposa zonse. Ameni

Print