Malembo Oyera
Mosiya 18


Mutu 18

Alima alalikira mwachinsinsi—Iye aika patsogolo pangano la ubatizo ndipo abatiza pa madzi a Mormoni—Iye akonza Mpingo wa Khristu ndi kudzoza ansembe—Adzithandiza okha ndi kuphunzitsa anthu—Alima ndi anthu ake athawa kwa Mfumu Nowa kupita m’chipululu. Mdzaka dza pafupifupi 147–145 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti Alima, amene adathawa kwa antchito a mfumu Nowa, adalapa machimo ake ndi mphulupulu zake, ndipo adapita mwamseri pakati pa anthu, ndipo adayamba kuphunzitsa mawu a Abinadi—

2 Inde, zokhudzana ndi chimene chidali nkudza, ndiponso zokhudzana ndi chiukitso cha akufa, ndi chiwombolo cha anthu, chimene chidayenera kuchitika mwa mphamvu, ndi mazunzo, ndi imfa ya Khristu, ndi chiukitso chake ndi kukwera kumwamba.

3 Ndipo onse amene adamva mawu ake adawaphunzitsa. Ndipo adawaphunzitsa iwo mwamseri, kuti asafike ku chidziwitso cha mfumu. Ndipo ambiri adakhulupilira mawu ake.

4 Ndipo zidachitika kuti monga ochuluka amene adakhulupilira iye adapita patsogolo ku malo amene ankatchedwa Mormoni, atalandira dzina lake kuchokera kwa mfumu, pokhala m’malire a dziko lodzala mu nthawi kapena nyengo zina, ndi zilombo zakuthengo.

5 Tsopano, mu Mormoni mudali kasupe wa madzi oyera, ndipo Alima adapita kumeneko, padali pafupi ndi madzi m’mitsinde ya mitengo yaing’ono; kumene amabisala masana kuti amfumu asamupeze.

6 Ndipo zidachitika kuti onse amene adakhulupilira iye adapita komweko kukamva mawu ake.

7 Ndipo zidachitika patatha masiku ambiri padali chiŵerengero chabwino chidasonkhana pamodzi pa malo a Mormoni, kuti amve mawu a Alima. Inde, adasonkhana onse akukhulupilira mawu ake, kudzamvera Iye. Ndipo adawaphunzitsa, ndipo adalalikira kwa iwo kulapa, ndi chiwombolo, ndi chikhulupiliro pa Ambuye.

8 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa iwo: Taonani, pano pali madzi a Mormoni (pakuti momwemo adatchedwa) ndipo tsopano, monga mukufuna kubwera m’khola la Mulungu, ndi kutchedwa anthu ake, ndi kulolera kunyamulilana zothodwetsa za wina ndi mzake, kuti zikakhale zopepuka;

9 Inde, ndipo ali okonzeka kulira ndi iwo akulira; inde, ndi kutonthoza iwo amene akusowa chitonthozo, ndi kuyimilira monga mboni za Mulungu nthawi zonse ndi m’zinthu zonse, ndi m’malo onse omwe mungakhalemo, mpaka imfa, kuti muwomboledwe ndi Mulungu, ndi kuwerengedwa pamodzi ndi iwo a chiukitso choyamba, kuti inu mukhale ndi moyo wamuyaya—

10 Tsopano ine ndinena kwa inu, ngati ichi chiri chikhumbo cha mitima yanu, kodi inu muli ndi chiyani chotsutsana ndi kubatizidwa m’dzina la Ambuye, monga umboni pamaso pake kuti inu mudalowa mu pangano ndi iye, kuti mudzamutumikira ndi kusunga malamulo ake, kuti atsanulire Mzimu wake mochuluka pa inu?

11 Ndipo tsopano pamene anthu adamva mawu awa, iwo adawomba manja awo ndi chisangalalo, ndipo adafuula: Ichi ndi chokhumba cha mitima yathu.

12 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima adatenga Helamu, iye pokhala m’modzi wa oyambilira, ndipo adapita ndikuyimilira m’madzi, ndipo adafuula, kuti: O Ambuye, tsanulirani Mzimu wanu pa wantchito wanu, kuti akachite ntchito iyi ndi chiyero cha mtima.

13 Ndipo pamene iye adanena mawu awa, Mzimu wa Ambuye udali pa iye, ndipo iye adati: Helamu, ine ndikukubatiza iwe, pokhala ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu Wamphamvu zonse, monga umboni kuti iwe walowa m’chipangano chomutumikira iye kufikira utafa monga ku thupi lakufa; ndipo Mzimu wa Ambuye utsanulidwire pa iwe; ndipo iye akupatse iwe moyo wamuyaya, mwa chiwombolo cha Khristu, amene adakonzedweratu ku maziko a dziko lapansi.

14 Ndipo Alima atanena mawu awa, onse Alima ndi Helamu adaikidwa m’madzi; ndipo adanyamuka, natuluka m’madzi ali okondwera, atadzadzidwa ndi Mzimu.

15 Ndipo kenako, Alima adatenga wina, ndikupita ulendo wachiwiri m’madzi, nam’batiza iye monga mwa woyamba, koma sadadzimizenso m’madzi.

16 Ndipo motere iye adabatiza aliyense amene adapita ku malo a Mormoni; ndipo iwo adali mu chiwerengero cha mazana awiri mphambu zinayi; inde, ndipo adabatizidwa m’madzi a Mormoni, ndipo adadzadzidwa ndi chisomo cha Mulungu.

17 Ndipo iwo ankatchedwa mpingo wa Mulungu, kapena mpingo wa Khristu, kuyambira nthawi imeneyo kupita mtsogolo. Ndipo zidachitika kuti aliyense amene adabatizidwa ndi mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu adawonjezedwa ku mpingo wake.

18 Ndipo zidachitika kuti Alima, okhala nawo ulamuliro wochokera kwa Mulungu, adadzoza ansembe; inde wansembe m’modzi kwa makumi asanu a iwo onse adawadzoza kuti alalikire kwa iwo, ndi kuwaphunzitsa za zinthu za Ufumu wa Mulungu.

19 Ndipo adawalamulira kuti asaphunzitse kanthu koma zokhazo zimene iye adaphunzitsa, ndi zimene zidayankhulidwa ndi m’kamwa mwa aneneri oyera.

20 Inde, ngakhale iye adawalamula iwo kuti asalalikire kalikonse kupatula kulapa ndi chikhulupiliro pa Ambuye; amene adawombola anthu ake.

21 Ndipo adawalamulira kuti pasakhale mkangano wina ndi mzake, koma kuti ayang’ane kutsogolo ndi diso limodzi, kukhala ndi chikhulupiliro chimodzi ndi ubatizo umodzi, ndi mitima yawo yolumikizika pamodzi mu umodzi ndi chikondi kwa wina ndi mzake.

22 Ndipo kotero adawalamulira iwo kulalikira. Ndipo kotero iwo adakhala ana a Mulungu.

23 Ndipo adawalamula kuti azisunga tsiku la sabata, ndi kulisunga lopatulika, ndiponso tsiku lirilonse adzipereka chiyamiko kwa Ambuye Mulungu wawo.

24 Ndipo adawalamulanso kuti ansembe amene iye adawaika adzigwira ntchito ndi manja awo kuti adzizithandiza.

25 Ndipo padali tsiku limodzi mu mlungu uliwonse limene lidapatulidwa kuti asonkhane pamodzi kuti aphunzitse anthu, ndi kupembedza Ambuye Mulungu wawo, ndiponso, monga momwe zidaliri mu mphamvu yawo, kusonkhana okha pamodzi.

26 Ndipo ansembe sadafunikire kudalira anthu kuti awathandize; koma chifukwa cha ntchito yawo adayenera kulandira chisomo cha Mulungu, kuti akakule mphamvu mu Mzimu, pokhala nacho chidziwitso cha Mulungu; kuti akaphunzitse ndi mphamvu ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu.

27 Ndipo kachiwiri Alima adalamulira kuti anthu a mpingo akuyenera kugawana chuma chawo, aliyense monga adali nazo; ngati ali nazo zochuluka, agawireko zochuluka; ndi iye amene adali nazo zochepa, koma zochepa zikuyenera kufunidwa; ndi kwa iye amene alibe kukapatsidwa.

28 Ndipo kotero akuyenera kupereka chuma chawo mwakufuna kwawo ndi zokhumba zabwino kwa Mulungu, ndi kwa ansembe aja amene adali osowa, inde; ndi kwa waumphawi wamaliseche aliyense.

29 Ndipo ichi adanena nawo, polamulidwa ndi Mulungu; ndipo adayenda mowongoka pamaso pa Mulungu; kugawirana wina ndi mzake mwakuthupi ndi mwakuuzimu molingana ndi zosowa zawo ndi zofuna zawo.

30 Ndipo tsopano zidachitika kuti zonsezi zidachitidwa mu Mormoni, inde, pa madzi a Mormoni, m’nkhalango yomwe idali pafupi ndi madzi a Mormoni; inde, malo a Mormoni, madzi a Mormoni, Nkhalango ya Mormoni, ndi yokongola bwanji ku maso a iwo amene adabwera ku chidziwitso cha Mombolo wawo; inde, ndipo ali odala bwanji, pakuti adzayimba zomlemekeza kwamuyaya.

31 Ndipo zinthu izi zidachitika m’malire a dzikolo, kuti zisafike ku chidziwitso cha mfumu.

32 Koma taonani, zidachitika kuti mfumu, atazindikira kuyendayenda pakati pa anthu, adatumiza antchito ake kuti akawalondere. Choncho pa tsiku limenelo adasonkhana pamodzi kudzamva mawu a Ambuye, adadziwika kwa mfumu.

33 Ndipo tsopano mfumu idanena kuti Alima adali kusonkhezera anthu kuti apandukire iye; kotero adatumiza ankhondo ake kuti akawawononge.

34 Ndipo zidachitika kuti Alima ndi anthu a Ambuye adadziwitsidwa za kubwera kwa gulu lankhondo la mfumu; kotero iwo adatenga mahema awo ndi mabanja awo ndipo adanyamuka kupita kuchipululu.

35 Ndipo iwo adali anthu pafupifupi mazana anayi ndi makumi asanu.