Malembo Oyera
Mosiya 11


Mutu 11

Mfumu Nowa alamulira moipa—Iye asangalala m’moyo wachisokonezo ndi akazi ake ndi adzakazi ake—Abinadi alosera kuti anthu adzatengedwa muukapolo—Moyo wake ufunidwa ndi Mfumu Nowa. Mdzaka dza pafupifupi 160–150 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Zenifu adapereka ufumu kwa Nowa, m’modzi wa ana ake aamuna; kotero Nowa adayamba kulamulira m’malo mwake; ndipo sadayende m’njira za atate ake.

2 Pakuti, taonani, sadasunge malamulo a Mulungu, koma adayenda monga mwa zokhumba za mtima wake. Ndipo adali ndi akazi ambiri ndi adzakazi. Ndipo adachititsa anthu ake kuchita tchimo, ndipo adachita zomwe zidali zonyasa pamaso pa Ambuye. Inde, ndipo iwo adachita zadama ndi zoipa zamtundu uliwonse.

3 Ndipo adakhometsa msonkho wa limodzi mwa magawo asanu a zonse adali nazo, limodzi mwa magawo asanu a golidi wawo, ndi siliva wawo, ndi limodzi la magawo asanu a zifi wawo, ndi kopa wawo, ndi mkuwa wawo, ndi zitsulo zawo; ndi limodzi mwa magawo asanu a ziweto zawo; ndi limodzi mwa magawo asanu a mbewu zawo zonse.

4 Ndipo zonsezi amatenga kuti adzizisamalira yekha, ndi akazi ake, ndi adzakazi ake; ndi ansembe ake, ndi akazi awo, ndi adzakazi awo; choncho adasintha zochitika za ufumu.

5 Pakuti iye adatsitsa pansi ansembe onse amene adapatulidwa ndi atate ake, ndikupatula atsopano m’malo mwawo, odzikweza m’kunyada kwa mitima yawo.

6 Inde, ndipo motero iwo adathandizidwa mu ulesi wawo, ndi m’kupembedza kwawo kwa mafano, ndi m’zadama zawo, ndi misonkho imene mfumu Nowa adaika pa anthu ake; motero anthu adagwira ntchito molimbika kuthandizira mphulupulu.

7 Inde, ndipo iwonso adakhala opembedza mafano, chifukwa adanyengedwa ndi mawu opanda pake ndi osyasyalika a mfumu ndi ansembe; pakuti adayankhula nawo zinthu zosyasyalika.

8 Ndipo zidachitika kuti Mfumu Nowa idamanga nyumba zambiri zokongola ndi zazikulu; ndipo idazikongoletsa ndi ntchito yabwino ya mitengo, ndi mitundu yonse ya zinthu zamtengo wapatali, za golidi, ndi siliva, ndi zitsulo, ndi mkuwa, ndi zifi, ndi kopa;

9 Ndipo idadzimangiranso nyumba yaikulu yachifumu; ndi mpando wachifumu pakati pake, zonse zimene zidali za mitengo yabwino, zokongoletsedwa ndi golidi, ndi siliva, ndi zinthu zamtengo wapatali.

10 Ndipo iyo idapangitsanso kuti antchito ake agwire ntchito zamtundu uliwonse zabwino mkati mwa makoma a kachisi, za matabwa abwino, ndi za kopa, ndi za mkuwa.

11 Ndipo mipando imene idapatulidwa ya akulu ansembe, imene idali pamwamba pa mipando ina yonse, adaikongoletsa ndi golidi weniweni; ndipo adapangitsa chotchinga pachifuwa kumangidwa patsogolo pawo, kuti adzitha kukhazika matupi awo ndi manja awo pamenepo pamene iwo akuyankhula zonama ndi mawu opanda pake kwa anthu ake.

12 Ndipo zidachitika kuti idamanga nsanja pafupi ndi kachisi; inde, nsanja yaitali kwambiri, ngakhale yaitali kwambiri kotero kuti imatha kuyima pamwamba pake ndi kuyang’ana dziko la Shilomu, ndiponso dziko la Shemuloni, limene lidatengedwa ndi Alamani; ndipo imayang’ana dziko lonse lozungulira.

13 Ndipo zidachitika kuti idamangitsa nyumba zambiri m’dziko la Shilomu; ndipo idamangitsa nsanja yaikulu paphiri la kumpoto kwa dziko la Shilomu; yomwe idakhala malo ochezera a ana a Nefi pa nthawi imene iwo adathawa m’dzikomo; ndi zotero iye adachita ndi chuma chimene iye adachipeza mwa misonkho ya anthu ake.

14 Ndipo zidachitika kuti iyo idaika mtima wake pa chuma chake, ndipo adathera nthawi yake m’makhalidwe achisawawa ndi akazi ake ndi adzakazi ake; momwemonso ansembe ake adathera nthawi yawo ndi akazi achiwerewere.

15 Ndipo zidachitika kuti idadzala minda yampesa pozungulira dziko; ndi kumanga moponderamo vinyo, ndi kuchurukitsa vinyo; ndipo kotero iyo idakhala yokumwa vinyo, ndiponso anthu ake.

16 Ndipo zidachitika kuti Alamani adayamba kubwera pa anthu ake, pa ochepa, ndi kumawapha m’minda mwawo, ndi pamene adali kuweta ziweto zawo.

17 Ndipo mfumu Nowa idatumiza alonda kuzungulira dzikolo kumawathamangitsa; koma sadatumize chiwerengero chokwanira, ndipo Alamani adadza pa iwo ndipo adawapha, ndipo adathamangitsa zambiri za ziweto zawo kutuluka m’dzikomo; motero Alamani adayamba kuwawononga iwo, ndi kuonetsa udani wawo pa iwo.

18 Ndipo zidachitika kuti mfumu Nowa idatumiza ankhondo ake kukamenyana nawo, ndipo iwo adabwenzedwa, kapena iwo adabwenzedwa kwa kanthawi; kotero, adabwelera akusangalala ndi katundu wolanda wawo.

19 Ndipo tsopano, chifukwa cha chigonjetso chachikulu ichi iwo adakuzidwa m’kunyada kwa mitima yawo; adadzitamandira ndi mphamvu zawo; kunena kuti makumi asanu awo akhonza kuima motsutsana ndi zikwi za Alamani; ndipo iwo adadzitama motero; ndipo adakondwera ndi mwazi, ndi kukhetsedwa kwa mwazi wa abale awo, ndipo ichi n’chifukwa cha kuipa kwa mfumu yawo ndi ansembe.

20 Ndipo zidachitika kuti kudali munthu pakati pawo amene dzina lake lidali Abinadi; ndipo iye adapita patsogolo pakati pawo, nayamba kulosera, kuti: Taonani, akutero Ambuye, ndipo kotero wandilamulira ine, kuti, Pita, ndipo ukanene kwa anthu awa, akutero Ambuye—Tsoka liri kwa anthu awa, pakuti ndaona zonyansa zawo, ndi zoipa zawo, ndi zadama zawo; ndipo pokhapokha atalapa ndidzawayendera mu mkwiyo wanga.

21 Ndipo kupatula iwo alape mtima ndi kutembenukira kwa Ambuye Mulungu wawo, taonani, ndidzawapereka m’manja mwa adani awo; inde, ndipo adzabweretsedwa mu ukapolo; ndipo adzasautsidwa ndi dzanja la adani awo.

22 Ndipo zidzachitika kuti iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu wawo, ndipo ndine Mulungu wansanje, wakuyendera mphulupulu za anthu anga.

23 Ndipo zidzachitika kuti kupatula anthu awa alapa ndi kutembenukira kwa Ambuye Mulungu wawo, iwo adzabweretsedwa mu ukapolo; ndipo palibe amene adzawawombole, koma Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse.

24 Inde, ndipo zidzachitika kuti pamene adzafuulira kwa ine ndidzachedwa kumva kulira kwawo; inde, ndipo ine ndidzawalolera kuti iwo adzakanthidwe ndi adani awo.

25 Ndipo pokhapokha atalapa atavala ziguduli ndi phulusa; ndi kufuulira kwa Ambuye Mulungu wawo mwamphamvu, sindidzamva mapemphero awo, kapena kuwawombola kuchoka m’masautso awo; ndipo akutero Ambuye, ndipo motero wandilamulira ine.

26 Tsopano zidachitika kuti pamene Abinadi adayankhula mawu awa kwa iwo adakwiya naye, ndipo adafuna kutenga moyo wake; koma Ambuye adamuwombola m’manja mwawo.

27 Tsopano pamene mfumu Nowa adamva za mawu amene Abinadi adayankhula kwa anthu, iyenso adakwiya; ndipo adati: Abinadi ndi ndani, kuti ine ndi anthu anga tiweruzidwe ndi iye, kapena Ambuye ndi ndani, amene adzawabweretsere anthu anga masautso aakulu motere?

28 Ndikulamula inu kuti mubweretse Abinadi kuno, kuti ine ndimuphe iye, pakuti iye wanena zinthu izi kuti akhonze kuutsa anthu anga kuti akwiyirane wina ndi mzake, ndi kudzutsa mikangano pakati pa anthu anga; kotero ndidzamupha.

29 Tsopano maso a anthu adachititsidwa khungu; kotero iwo adaumitsa mitima yawo motsutsana ndi mawu a Abinadi, ndipo kuyambira pamenepo adafunafuna kumugwira iye. Ndipo mfumu Nowa idaumitsa mtima wake motsutsana ndi mawu a Ambuye, ndipo sidalape zoipa zake.

Print