Malembo Oyera
Mosiya 15


Mutu 15

Momwe Khristu aliri Atate ndi Mwana—Adzachita mapembedzero ndi kunyamula zolakwa za anthu ake. Iwo ndi aneneri wonse oyera ndiwo mbewu yake—Iye amakwaniritsa Chiukitso—Ana aang’ono ali ndi moyo wamuyaya. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano Abinadi adati kwa iwo: Ndikufuna kuti mumvetse kuti Mulungu iye mwini adzabwera pansi pakati pa ana a anthu, ndipo adzawombola anthu ake.

2 Ndipo popeza adzakhala m’thupi, adzatchedwa Mwana wa Mulungu; ndipo popereka thupi ku chifuniro cha Atate, kukhala Atate ndi Mwana—

3 Atate, chifukwa adabadwa ndi mphamvu ya Mulungu; ndi Mwana, chifukwa cha thupi; motero kukhala Atate ndi Mwana—

4 Ndipo iwo ali Mulungu m’modzi, inde, Atate Wamuyaya yemweyo wa kumwamba ndi wa dziko lapansi.

5 Ndipo motero thupi lidzakhala lomvera Mzimu, kapena Mwana kwa Atate, okhala Mulungu m’modzi, avutika m’mayesero, ndipo osagwa ku mayesero, koma alolera yekha kunyozedwa, ndi kukwapulidwa, ndi kutulutsidwa, ndi kukanidwa ndi anthu ake.

6 Ndipo patatha zonsezi, atachita zozizwitsa zambiri zamphamvu pakati pa ana a anthu, iye adzatsogozedwa, inde, monga Yesaya adati: ngati nkhosa pamaso pa woyisenga siyankhula, kotero iye sadatsegula pakamwa pake.

7 Inde, ngakhale kotero iye adzatsogozedwa, kupachikidwa, ndi kuphedwa, thupi lidzakhala logonjera ngakhale ku imfa, chifuniro cha Mwana kumezedwa mu chifuniro cha Atate.

8 Ndipo momwemonso Mulungu adula zingwe za imfa; atapeza chigonjetso pa imfa; kupatsa Mwana mphamvu ya kupembedzera ana a anthu—

9 Atakwera kumwamba, ali ndi zimphyo za chifundo; kudzadzidwa ndi chifundo kwa ana a anthu; kuima pakati pawo ndi chilungamo; atadula zingwe za imfa, adadzitengera pa iye yekha mphulupulu zawo ndi zolakwa zawo, atawawombola iwo, ndi kukwaniritsa zofuna za chilungamo.

10 Ndipo tsopano ndinena kwa inu, Ndani adzafotokozera za m’badwo wake? Taonani, ndinena kwa inu, kuti moyo wake utaperekedwa nsembe ya uchimo, adzaona mbewu yake. Ndipo tsopano inu mukuti chiyani? Ndipo ndani adzakhala mbewu yake?

11 Taonani ndinena kwa inu, kuti aliyense amene adamva mawu a aneneri, inde, aneneri oyera onse amene alosera ponena za kubwera kwa Ambuye—ndikunena kwa inu, kuti onse amene adamvera mawu awo, ndipo adakhulupilira kuti Ambuye adzawombola anthu ake, ndipo ayang’anira ku tsiku limenelo kuti akhululukidwe ku machimo awo, ndikunena kwa inu, kuti awa ndiwo mbewu yake; kapena ali olandira cholowa cha nyumba ya Ufumu wa Mulungu.

12 Pakuti awa ndiwo amene adasenza machimo awo; awa ndiwo amene adawafera, kuwawombola ku zolakwa zao. Ndipo tsopano, iwo si mbewu yake kodi?

13 Inde, ndipo kodi si aneneri, aliyense amene watsegula pakamwa pake kunenera, amene sadagwere m’cholakwa, ine ndikutanthauza aneneri onse oyera chiyambire dziko lapansi? Ine ndikunena kwa inu, kuti iwo ndiwo mbewu yake.

14 Ndipo iwowa ndi amene afalitsa za mtendere, amene abweretsa uthenga wabwino wazabwino, amene afalitsa za chipulumutso; nati kwa Ziyoni, Mulungu wako alamulira!

15 Ndipo O adali okongola bwanji pamapiri mapazi a iwo!

16 Ndiponso, ndi okongola bwanji nanga pamapiri mapazi a iwo amene akufalitsabe mtendere!

17 Ndiponso, ndi okongola bwanji pamapiri mapazi a iwo amene mtsogolo muno adzafalitsa mtendere, inde, kuchokera nthawi ino mpaka muyaya!

18 Ndipo taonani, ndikunena kwa inu, izi sizomwezi zokha. Pakuti O, ali okongola ndithu pamapiri mapazi a iye amene abwera ndi uthenga wabwino; ndiye woyambitsa mtendere, inde, ngakhale Ambuye, amene adawombola anthu ake; inde, amene adapereka chipulumutso kwa anthu ake;

19 Pakuti pakadapanda chiwombolo chimene adawapangira anthu ake, chimene chidakonzedwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi, ndikunena kwa inu, pakadapanda izi, anthu onse akadatayika.

20 Koma taonani, nsinga za imfa zidzadulidwa, ndipo Mwana alamulira, ndipo ali ndi mphamvu pa akufa; kotero, abweretsa chiukitso kwa akufa.

21 Ndipo padzabwera chiukitso, ngakhale chiukitso choyamba; inde, chiukitso cha iwo amene adakhalako; ndipo amene ali, ndi amene adzakhala, ngakhale kufikira ku chiukitso cha Khristu—pakuti motero iye adzatchedwa.

22 Ndipo tsopano, kuuka kwa aneneri onse, ndi onse akukhulupilira mawu awo; kapena onse amene adasunga malamulo a Mulungu, adzabwera mu chiukitso choyamba; kotero, iwo ali chiukitso choyamba.

23 Iwo aukitsidwa kukhala ndi Mulungu amene adawawombola; motero ali nawo moyo wamuyaya kudzera mwa Khristu, amene wadula nsinga za imfa.

24 Ndipo iwo ndiwo amene ali nawo gawo pa chiukitso choyamba; ndipo iwo ndiwo adamwalira Khristu asadabwere; mu kusadziwa kwawo, popeza sadalalikiridwe chipulumutso kwa iwo. Ndipo kotero Ambuye abweretsa za kubwezeretsedwa kwa awa; ndipo iwo ali ndi gawo mu chiukitso choyamba, kapena ali nawo moyo wamuyaya, pokhala atawomboledwa ndi Ambuye.

25 Ndipo ana aang’ono nawonso ali nawo moyo wamuyaya.

26 Koma taonani, ndi muope, ndi kunjenjemera pamaso pa Mulungu, pakuti mukuyenera kunjenjemera; pakuti Ambuye sawombola aliyense wotere amene ampandukira ndi kufa m’machimo awo; inde, ngakhale onse amene adatayika m’machimo awo chiyambire dziko lapansi, amene adapandukira Mulungu mwadala, amene adadziwa malamulo a Mulungu, ndipo sadawasunge; iwo ndiwo amene alibe gawo pa chiukitso choyamba.

27 Kotero simukuyenera kunjenjemera kodi? Pakuti chipulumutso sichifika kwa wotere; pakuti Ambuye sadawombole wotere; inde, ngakhalenso Ambuye sangawawombole wotere; pakuti samatha kudzikana yekha; pakuti iye sangakane chilungamo pamene chili ndi zonena zake.

28 Ndipo tsopano ine ndikunena kwa inu kuti nthawi idzafika pamene chipulumutso cha Ambuye chidzalengezedwa kwa dziko lirilonse, fuko, chinenero, ndi anthu.

29 Inde, Ambuye, alonda anu adzakweza mawu awo; ndi mawu pamodzi adzayimba; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Ambuye adzabwenzeretsanso Ziyoni.

30 Sangalalani, imbani pamodzi, inu mabwinja a Yerusalemu; pakuti Ambuye watonthoza anthu ake, wawombola Yerusalemu.

31 Ambuye waonetsera mkono wake woyera pamaso pa maiko onse; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

Print