Malembo Oyera
Mosiya 28


Mutu 28

Ana a Mosiya apita kukalalikira kwa Alamani—Pogwiritsa ntchito miyala iwiri ya ulosi, Mosiya amasulira mapale a Ayaredi. Mdzaka dza pafupifupi 92 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti pamene ana aamuna a Mosiya adachita zinthu zonsezi, iwo adatenga chiwerengero chochepa ndi iwo ndipo adabwelera kwa atate awo, mfumu, ndipo adapempha kwa iye kuti apereke kwa iwo kuti iwo akathe, ndi awa amene adawasankha, kupita ku dziko la Nefi kuti akalalikire zinthu zimene adamva, ndi kuti akagawire mawu a Mulungu kwa abale awo, Alamani—

2 Kuti mwina akawafikitse ku chidziwitso cha Ambuye Mulungu wawo, ndi kuwatsimikizira za mphulupulu za makolo awo; ndi kuti mwina angawachiritse iwo ku udani wawo kwa Anefi, kuti iwo akabweretsedwenso kuti asangalale mwa Ambuye Mulungu wawo, kuti akathe kukhala aubwenzi kwa wina ndi mzake, ndi kuti kusakhalenso mikangano m’dziko lonse limene Ambuye Mulungu wawo adawapatsa.

3 Tsopano iwo adali ofunitsitsa kuti chipulumutso chilengezedwe kwa cholengedwa chirichonse, pakuti sakadatha kulolera kuti munthu aliyense awonongeke; inde, ngakhale malingaliro omwewo akuti mzimu uliwonse ukuyenera kupilira chizunzo chosatha adawapangitsa iwo kunjenjemera ndi kuthunthumira.

4 Ndipo motero Mzimu wa Ambuye udagwira ntchito pa iwo, pakuti iwo adali oipitsitsa kwambiri a wochimwa. Ndipo Ambuye adaona koyenera mu chifundo chake chosatha kuwateteza; komabe iwo adavutika kuzowawa zazikulu kwa moyo chifukwa cha mphulupulu zawo, kuvutika kwambiri ndi kuopa kuti adzatayidwa kwamuyaya.

5 Ndipo zidachitika kuti iwo adachondelera atate awo masiku ambiri kuti athe kupita ku dziko la Nefi.

6 Ndipo mfumu Mosiya adapita ndipo adafunsa kwa Ambuye ngati angalore ana ake aamuna kupita pakati pa Alamani kukalalikira mawu.

7 Ndipo Ambuye adati kwa Mosiya: Aleke apite, pakuti ambiri adzakhulupilira mawu awo, ndipo adzakhala nawo moyo wamuyaya; ndipo ndidzawombola ana ako aamuna kuchokera m’manja mwa Alamani.

8 Ndipo zidachitika kuti Mosiya adalora kuti apite ndi kukachita monga mwa pempho lawo.

9 Ndipo iwo adanyamuka ulendo wawo kuchipululu kuti apite kukalalikira mawu pakati pa Alamani; ndipo ndidzapereka nkhani ya machitachita awo kutsogoloku.

10 Tsopano mfumu Mosiya idalibe wina woti amuveke ufumu pa iye, pakuti padalibe aliyense wa ana ake aamuna amene akadalandira ufumuwo.

11 Kotero iyo idatenga zolemba zimene zidali zozokotedwa pa mapale a mkuwa, ndiponso mapale a Nefi, ndi zinthu zonse zimene iyo idasunga ndi kuzisamala monga mwa malamulo a Mulungu, itatha kumasulira ndi kuchititsa kuti zilembedwe zolembedwa zimene zidali pa mapale a golide amene adapezedwa ndi anthu a Limuhi zomwe zidaperekedwa kwa iyo ndi dzanja la Limuhi;

12 Ndipo izi adazichita chifukwa cha nkhawa yaikulu ya anthu ake; pakuti adakhumba kwambiri kudziwa za anthu womwe adawonongedwa.

13 Ndipo tsopano adawamasulira ndi miyala iwiri ija yokhomeleredwa m’mbali ziwiri za uta.

14 Tsopano zinthu izi zidakonzedwa kuchokera pa chiyambi, ndipo zidaperekedwa kuchokera ku m’badwo kupita ku m’badwo, ndi cholinga cha kumasulira ziyankhulo;

15 Ndipo izo zasungidwa ndi kusamalidwa ndi dzanja la Ambuye, kuti aonetsere kwa cholengedwa chirichonse chimene chikuyenera kutenga dzikolo mphulupulu ndi zonyansa za anthu ake;

16 Ndipo iye amene ali nazo izi amatchedwa mlosi, monga mwa machitidwe akale.

17 Tsopano Mosiya atatsiriza kumasulira zolemba izi, taonani, zidapereka nkhani ya anthu amene adawonongedwa, kuchokera nthawi imene iwo adawonongedwa kubwelera ku kumanga kwa nsanja yaikulu, pa nthawi imene Ambuye adasokoneza chiyankhulo cha anthu ndipo adabalalikana pankhope ya dziko lonse lapasi, inde, ndipo ngakhale kuyambira nthawi imeneyo mpaka kulengedwa kwa Adamu.

18 Tsopano nkhani iyi idachititsa anthu a Mosiya kulira kwambiri, inde, adadzadzidwa ndi chisoni; komabe idawapatsa nzeru zambiri, zomwe adakondwera nazo.

19 Ndipo nkhani iyi idzalembedwa kutsogoloku; pakuti taonani, nkwabwino kuti anthu onse adziwe zinthu zolembedwa m’nkhaniyi.

20 Ndipo tsopano, monga ndidanena kwa inu, kuti mfumu Mosiya itachita zinthu izi, iyo idatenga mapale a mkuwa, ndi zinthu zonse zimene idasunga, ndipo idazipereka kwa Alima, amene adali mwana wa Alima; inde, zolemba zonse, ndiponso zomasulira, ndipo idazipereka pa iye, ndipo idamulamulira iye kuti azisunga ndi kuzisamala izo, ndiponso kusunga zolemba za anthu, kuzipereka izo pansi kuchokera ku m’badwo umodzi kupita ku umzake, monga momwe izo zidaperekedwera kuyambira pomwe Lehi adachoka ku Yerusalemu.