Malembo Oyera
Mosiya 6


Mutu 6

Mfumu Benjamini ilemba maina a anthu ndipo aika ansembe kuti adziwaphunzitsa—Mosiya alamulira monga mfumu yolungama. Mdzaka dza pafupifupi 124–121 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, Mfumu Benjamini idaganiza kuti n’koyenera, itamaliza kuyankhula ndi anthu, kuti atenge mayina a onse amene adalowa mu pangano ndi Mulungu kusunga malamulo ake.

2 Ndipo zidachitika kuti padalibe munthu m’modzi, kupatula amene adali ana aang’ono, koma amene adalowa mu pangano ndipo adatenga pa iwo dzina la Khristu.

3 Ndipo kachiwiri, zidachitika kuti pamene mfumu Benjamini itamaliza zinthu zonsezi, ndipo idali atapatura mwana wake Mosiya kukhala olamulira ndi mfumu pa anthu ake, ndipo idampatsa malamulo wonse a ufumuwo ndipo idaikanso ansembe ophunzitsa anthu; kotero kuti akamve ndi kudziwa malamulo a Mulungu; ndi kuwachangamutsa iwo pokumbukira lumbiro limene adapanga; iyo idabalalitsa khamulo; ndipo adabwelera yense monga mwa mabanja awo, ku nyumba zawo.

4 Ndipo Mosiya adayamba kulamulira m’malo mwa atate ake. Ndipo adayamba kulamulira m’chaka cha makumi atatu cha msinkhu wake, kuphatikiza zonse, pafupifupi dzaka mazana anayi ndi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu.

5 Ndipo mfumu Benjamini idakhala ndi moyo dzaka zitatu ndipo idamwalira.

6 Ndipo zidachitika kuti mfumu Mosiya idayenda m’njira za Ambuye, ndipo idaonetsetsa ziweruzo zake ndi malamulo olembedwa ake, ndipo idasunga malamulo ake m’zinthu zonse zimene adamulamula.

7 Ndipo mfumu Mosiya idapangitsa anthu ake kuti azilima m’nthaka. Ndipo nayonso, idalima nthaka, kuti kotero isalemetse anthu ake; kuti athe kuchita molingana ndi zinthu zonse zimene adazichita atate ake. Ndipo padalibe mkangano pakati pa anthu ake onse kwa nthawi ya dzaka zitatu.

Print