Malembo Oyera
Mosiya 22


Mutu 22

Madongosolo apangidwa kuti anthu athawe ku ukapolo wa Alamani—Alamani aledzera—Anthu athawa, abwelera ku Zarahemula, ndipo akhala omvera kwa Mfumu Mosiya. Mdzaka dza pafupifupi 121–120 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Amoni ndi mfumu Limuhi adayamba kukambirana ndi anthu m’mene angadziwombolere wokha kuchoka mu ukapolo; ndipo ngakhale iwo adapangitsa kuti anthu wonse adzisonkhanitse pamodzi; ndipo izi adachita kuti akhale ndi mawu a anthu pa nkhaniyo.

2 Ndipo zidachitika kuti sadapeze njira yodzipulumutsira okha ku ukapolo, koma kutenga akazi ndi ana awo; ndi nkhosa zawo, ndi ng’ombe zawo, ndi mahema awo, ndi kupita ku chipululu; pakuti Alamani adali ochuluka kwambiri, kudali kosatheka kuti anthu a Limuhi alimbane nawo, kuganizira kuti angadziwombole iwo okha kutuluka mu ukapolo ndi lupanga.

3 Tsopano zidachitika kuti Gideoni adapita patsogolo ndipo adayima patsogolo pa mfumu, ndipo adati kwa iyo: Tsopano O mfumu, mpaka pano mwamvetsera mawu anga nthawi zambiri pamene ife tidali kulimbana ndi abale athu, Alamani.

4 Ndipo tsopano, O mfumu, ngati simudandipeze ine kukhala kapolo wopanda pake, kapena ngati mpaka pano mwamvera mawu anga mu mlingo uliwonse, ndipo akhala akutumikira inu, kotero ine ndikufuna kuti inu mumvere mawu anga pa nthawi ino, ndipo ndidzakhala mtumiki wanu ndi kuwombola anthu awa kutuluka mu ukapolo.

5 Ndipo mfumu idamulora kuti ayankhule. Ndipo Gideoni adati kwa iye:

6 Taonani njira yakumbuyo, kudutsa khoma lakumbuyo, kuseri kwa mzindawo. Alamani, kapena alonda a Alamani, usiku amaledzera; kotero tiyeni tilengeze pakati pa anthu awa onse, kuti asonkhanitse nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, kuti azikankhire m’chipululu usiku.

7 Ndipo ndidzapita monga mwa lamulo lanu ndi kukapereka msonkho wotsiriza wa vinyo kwa Alamani; ndipo adzaledzera; ndipo tidzadutsa njira yobisika yakumanzere kwa chihema chawo pamene iwo aledzera ndi kugona.

8 Potero tidzapita kuchipululu, ndi akazi athu, ndi ana athu, ndi nkhosa zathu, ndi ng’ombe zathu; ndipo tidzayenda kuzungulira dziko la Shilomu.

9 Ndipo zidachitika kuti mfumu idamvera mawu a Gideoni.

10 Ndipo mfumu Limuhi idapangitsa kuti anthu ake asonkhanitse pamodzi ziweto zawo; ndipo idatumiza msonkho wa vinyo kwa Alamani; ndipo idatumizanso vinyo wochuluka, monga mphatso kwa iwo; ndipo iwo adamwa vinyo mwaufulu umene mfumu Limuhi idatumiza kwa iwo.

11 Ndipo zidachitika kuti anthu a mfumu Limuhi adanyamuka usiku kupita m’chipululu ndi nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, ndi kupita mozungulira dziko la Shilomu m’chipululu, ndi kupinda njira yawo ku dziko la Zarahemula, akutsogozedwa ndi Amoni ndi abale ake.

12 Ndipo adatenga golide wawo yense, ndi siliva, ndi zinthu zawo zamtengo wapatali, zimene akadatha kunyamula, ndiponso zakudya zawo pamodzi ndi iwo, kulowa m’chipululu; ndipo adatsata ulendo wawo.

13 Ndipo atakhala masiku ambiri mu chipululu adafika m’dziko la Zarahemula, ndipo adaphatikizana ndi anthu a Mosiya, ndipo adakhala anthu ake.

14 Ndipo zidachitika kuti Mosiya adawalandira iwo mwa chisangalalo; ndipo adalandiranso zolemba zawo, ndiponso zolemba zimene zidapezedwa ndi anthu a Limuhi.

15 Ndipo tsopano zidachitika pamene Alamani adapeza kuti anthu a Limuhi achoka m’dzikomo usiku; kuti adatumiza ankhondo m’chipululu kuwalondola;

16 Ndipo atawalondola masiku awiri, sadathenso kutsatira mayendedwe awo; kotero iwo adatayika mu chipululu.

Print