Malembo Oyera
Mosiya 3


Mutu 3

Mfumu Benjamini ipitiliza kuyankhula kwake—Ambuye Wamphamvu zonse adzatumikira pakati pa anthu m’chihema cha dothi—Mwazi udzachokera m’mabowo onse pamene Iye adzatetezera machimo a dziko lapansi—Lake ndi dzina lokhalo limene chipulumutso chimabwelera—Anthu akhonza kuvula umunthu wachilengedwe ndi kukhala Oyera kudzera mwa Chitetezero—Mazunzo a oipa adzakhala ngati nyanja ya moto ndi sulufure. Mdzaka dza pafupifupi 124 Yesu asadabadwe.

1 Ndiponso abale anga, ndikuyitanira chidwi chanu, pakuti ndiri ndi zina zambiri zoti ndiyankhule kwa inu; pakuti taonani, ndiri nazo zinthu zoti ndikuuzeni zokhudzana ndi icho chimene chiri nkudza.

2 Ndipo zinthu zimene ndidzakuuzani zadziwitsidwa kwa ine ndi mngelo wochokera kwa Mulungu. Ndipo adati kwa ine, Dzuka; ndipo ndidadzuka, ndipo taonani, adaima pamaso panga.

3 Ndipo adati kwa ine: Dzuka, ndipo mvera mawu amene ndidzakuuza iwe; pakuti taona, ndadza kudzalengeza kwa iwe Uthenga Wabwino wa chisangalalo chachikulu.

4 Pakuti Ambuye amva mapemphero ako; ndipo aweluza za chilungamo chako, ndipo wandituma ine kuti ndilengeze kwa iwe kuti usangalale; ndi kuti iwe uthe kulengeza kwa anthu ako, kuti iwonso akadzadzidwe ndi chisangalalo.

5 Pakuti taonani, nthawi ikudza, ndipo siili patali, kuti ndi mphamvu, Ambuye Wamphamvu zonse amene akulamulira, amene adali, ndipo ali kuchokera ku nthawi zonse mpaka muyaya, adzatsika kuchokera kumwamba pakati pa ana a anthu, ndipo adzakhala muchihema chadothi, nadzatulukira pakati pa anthu, kuchita zozizwa zamphamvu, monga kuchiritsa odwala, kuwukitsa akufa, kupangitsa olumala kuyenda, akhungu kuti alandire kuona kwawo, ndi ogontha kumva, ndi kuchiritsa mitundu yonse ya matenda.

6 Ndipo iye adzatulutsa ziwanda, kapena mizimu yoipa imene imakhala m’mitima ya ana a anthu.

7 Ndipo taonani, iye adzazunzika m’mayesero, ndi ululu wa thupi, njala, ludzu, ndi kutopa, ngakhale kuposa momwe munthu angavutikire, kupatula kuti kukhale ku imfa; pakuti taonani, mwazi udzatuluka m’mabowo onse, kotero kudzakhala kwakukulu kuwawa kwake chifukwa cha kuipa ndi zonyansa za anthu ake.

8 Ndipo adzatchedwa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Atate wa kumwamba ndi dziko lapansi, Mlengi wa zinthu zonse kuyambira pachiyambi; ndipo amake adzatchedwa Mariya.

9 Ndipo taonani, iye abwera kwa ake wokha, kuti chipulumutso chikabwere kwa ana a anthu ngakhale kudzera mu chikhulupiliro pa dzina lake; ndipo ngakhale pambuyo pa zonsezi iwo adzamuyesa iye munthu, ndipo adzanena kuti ali ndi chiwanda, ndipo adzamkwapula iye, ndipo adzampachika iye.

10 Ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu; ndipo taonani, ayimilira kuti aweruze dziko; ndipo taonani, zinthu zonsezi zachitidwa kuti chiweruzo cholungama chidze pa ana a anthu.

11 Pakuti taonani, ndiponso mwazi wake umatetezera machimo a iwo amene adagwa chifukwa cha kulakwitsa kwa Adamu; amene adafa osadziwa chifuniro cha Mulungu chokhudza iwo, kapena amene adachimwa mosadziwa.

12 Koma tsoka, tsoka kwa amene akudziwa kuti akupandukira Mulungu! Pakuti chipulumutso sichifika kwa wotere kupatulapo kukhala kuti chikudzera mu kulapa ndi chikhulupiliro pa Ambuye Yesu Khristu.

13 Ndipo Ambuye Mulungu watumiza aneneri ake oyera pakati pa ana onse a anthu, kulengeza zinthu izi kwa mafuko onse, ndi maiko, ndi chinenero; kuti mwa ichi wonse akukhulupilira kuti Khristu adzabwera, omwewo akalandire chikhululukiro cha machimo awo; ndipo asangalale ndi chisangalalo chachikulu, monga ngati adafika kale pakati pawo.

14 Komabe Ambuye Mulungu adaona kuti anthu ake adali anthu osamvai, ndipo adaika kwa iwo lamulo, ngakhale lamulo la Mose.

15 Ndi zizindikiro zambiri, ndi zodabwitsa, ndi zoyimira, ndipo zithunzithunzi zidasonyezedwa kwa iwo, zokhudzana ndi kubwera kwake; komanso aneneri oyera adayankhula kwa iwo zokhudzana ndi kubwera kwake; ndipo adaumitsa mitima yawo, ndipo sadazindikire kuti chilamulo cha Mose sichithandiza kanthu, koma kudzera mu chitetezero cha mwazi wake.

16 Ndipo ngakhale kukadakhala kotheka kuti ana ang’ono angathe kuchimwa iwo sakadatha kupulumutsidwa; koma ndinena kwa inu iwo ali odala; pakuti taonani, monga mwa Adamu, kapena mwa chilengedwe, adagwa, inde ngakhale mwazi wa Khristu uwatetezera ku machimo awo.

17 Komanso, ine ndikunena kwa inu, kuti sipadzakhala dzina lina limene lidzaperekedwa, kapena njira ina iliyonse, kapena njira imene chipulumutso chingadze kwa ana a anthu; kupatula kudzera mudzina la Khristu lokha, Ambuye Wamphamvu zonse.

18 Pakuti taonani iye aweruza, ndipo chiweruzo chake ndi cholungama; ndipo wakhanda sawonongeka amene amafa mu ukhanda wake; koma anthu amadzimwera chilango ku miyoyo yawo kupatula iwo adzichepetse iwo eni ndi kukhala monga ana aang’ono, ndi kukhulupilira kuti chipulumutso chidali, ndipo chiri, ndipo chirinkudza, kudzera mwa mwazi wotetezera wa Khristu, Ambuye Wamphamvu zonse.

19 Pakuti munthu wachibadwidwe ndi m’dani wa Mulungu; ndipo wakhala kuchokera mu kugwa kwa Adamu, ndipo adzakhala, kunthawi za nthawi, pokhapokha alore kukopa kwa Mzimu Woyera; ndi kuvula munthu wachilengedwe, ndikukhala woyera mtima kudzera mu chitetezero cha Khristu Ambuye; ndikukhala ngati mwana, womvera, wofatsa, wodzichepetsa, wopilira, wodzadza ndi chikondi, wofunitsitsa kugonjera zonse zimene Ambuye aona kuti n’koyenera kumupatsa iye, monga mwana amvera atate ake.

20 Ndipo kuposa apo, ine ndikunena kwa inu, kuti nthawi idzafika pamene chidziwitso cha Mpulumutsi chidzafalikira ku dziko lirilonse, fuko, chinenero, ndi anthu.

21 Ndipo taonani, nthawi imeneyo ikadzafika, palibe amene atadzapezeke wopanda cholakwa pamaso pa Mulungu, kupatula ana ang’ono, koma kudzera mu nkulapa kokha ndi chikhulupiliro pa dzina la Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse.

22 Ndipo ngakhale pa nthawi ino, pamene mudzaphunzitsa anthu anu zinthu zimene Ambuye Mulungu wanu adakulamulirani; ngakhale pamenepo sapezedwanso osalakwa pamaso pa Mulungu, koma molingana ndi mawu amene ndayankhula ndi iwe.

23 Ndipo tsopano ine ndayankhula mawu amene Ambuye Mulungu wandilamulira ine.

24 Ndipo motero akutero Ambuye: Iwo adzaima monga mboni yowala yotsutsa anthu awa; pa tsiku lachiweruzo; lomwe adzaweruzidwa; munthu aliyense monga mwa ntchito zake, kaya zili zabwino, kapena zoipa.

25 Ndipo ngati iwo ali oipa amatumizidwa ku kawonedwe kowopsya ka zolakwa zawo ndi zonyansa, zimene zimawapangitsa iwo kunyetchera kuchoka pamaso pa Ambuye kupita ku mkhalidwe wachisoni ndi mazunzo osatha, kumene iwo sangathenso kubwelera; kotero iwo amwa chiwonongeko kwa miyoyo yawo.

26 Kotero, iwo amwa kuchokera m’chikho cha mkwiyo wa Mulungu, chimene chilungamo sichikadakananso kwa iwo monga momwe sichikadakana kuti Adamu adayenera kugwa chifukwa cha kudya kwake chipatso choletsedwacho; kotero, chifundo sichikadakhalanso pa iwo ku nthawizonse.

27 Ndipo mazunzo awo ali ngati nyanja ya moto ndi sulufure, imene malawi ake sazimitsidwa, ndipo utsi wake umakwera m’mwamba kunthawi za nthawi. Motere Ambuye wandilamulira ine. Ameni.