Malembo Oyera
Mosiya 10


Mutu 10

Mfumu Lamani imwalira—Anthu ake ndi olusa ndi ankhanza ndipo amakhulupilira m’miyambo yabodza—Zenifu ndi anthu ake awagonjetsa. Mdzaka dza pafupifupi 187–160 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti tidayambanso kukhazikitsa ufumu ndipo tidayambanso kukhala m’dzikolo mwamtendere. Ndipo ndidapangitsa kuti pakhale zida zankhondo zopangidwa zamtundu uliwonse, kuti potero ndikhonza kukhala ndi zida za anthu anga pa nthawi yomwe Alamani angabwerenso kudzamenyana ndi anthu anga.

2 Ndipo ndidaika alonda kuzungulira dzikolo; kuti Alamani asadzathe kudzabwera pa ife kachiwiri mosawazindikira ndi kutiwononga ife; ndi motero ndidasunga anthu anga ndi nkhosa zanga, kuti zisagwe m’manja mwa adani athu.

3 Ndipo zidachitika kuti tidalandira dziko la makolo athu kwa dzaka zambiri, inde, kwa nthawi ya dzaka makumi awiri ndi ziwiri.

4 Ndipo ine ndidachititsa kuti anthu adzilima nthaka, ndi kudzala mbewu zamitundumitundu, ndi zipatso zamtundu uliwonse.

5 Ndipo ine ndidachititsa kuti akazi adzipota, ndi kugwira nchito molimbika ndi kugwira mitundu yonse ya nsalu za bafuta, inde, ndi nsalu za mtundu uliwonse, kuti ife tikaveke umaliseche wathu; ndipo momwemo tidachita bwino m’dzikomo; choncho tidakhala ndi mtendere kosalekeza m’dzikomo kwa nthawi ya dzaka makumi awiri ndi ziwiri.

6 Ndipo zidachitika kuti mfumu Lamani adamwalira, ndipo mwana wake adayamba kulamulira m’malo mwake. Ndipo adayamba kuutsa anthu ake kupandukira anthu anga; choncho iwo adayamba kukonzekera nkhondo, ndi kuti abwere kudzamenyana ndi anthu anga.

7 Koma ine ndidali nditatumiza akazitape anga kukazungulira dziko la Shemuloni, kuti ndikazindikire zokonzekera zawo, kuti ndichenjere pa iwo, kuti asabwere pa anthu anga ndi kuwawononga.

8 Ndipo zidachitika kuti adakwera cha kumpoto kwa dziko la Shilomu, ndi makamu awo aunyinji, amuna onyamula mauta, ndi mivi, ndi malupanga, ndi dzikwanje, ndi miyala, ndi malegeni; ndipo adali atameta mitu yawo kotero kuti idali yampala; ndipo adadzimangilira lamba wachikopa m’chiuno mwawo.

9 Ndipo zidachitika kuti ndidachititsa kuti akazi ndi ana a anthu anga abisale m’chipululu; ndipo inenso ndidachititsa kuti azibambo anga onse aakulu amene akadatha kunyamula zida, ndi anyamata anga onse amene akadatha kunyamula zida; adayenera kudzisonkhanitsa okha kuti apite kukamenyana ndi Alamani; ndipo ndidawaika iwo m’mizere yawo, munthu aliyense molingana ndi msinkhu wake.

10 Ndipo zidachitika kuti tidapita kukamenyana ndi Alamani; ndipo ine, ngakhale ine, mu ukalamba wanga, ndidapita kukamenyana ndi Alamani. Ndipo zidachitika kuti tidapitadi mu mphamvu ya Ambuye kukamenya nkhondo.

11 Tsopano, Alamani sankadziwa kalikonse zokhudza Ambuye, kapena mphamvu ya Ambuye, kotero iwo adadalira pa mphamvu zawo zokha. Koma iwo adali anthu amphamvu, monga ku mphamvu za anthu.

12 Iwo adali anthu olusa, ndi ankhanza, ndi a ludzu la mwazi, akukhulupilira mu miyambo ya makolo awo, imene ili iyi—Kukhulupilira kuti adathamangitsidwa kuchokera m’dziko la Yerusalemu chifukwa cha mphulupulu za makolo awo, ndipo adalakwiridwa m’chipululu ndi abale awo, ndipo iwonso adalakwiridwa powoloka nyanja;

13 Ndiponso, kuti iwo adalakwiridwa pamene adali m’dziko la cholowa chawo choyamba, atawoloka nyanja, ndipo zonsezi chifukwa chakuti Nefi adali wokhulupirika kwambiri m’kusunga malamulo a Ambuye—choncho iye adakonderedwa ndi Ambuye, pakuti Ambuye adamva mapemphero ake ndipo adawayankha, ndipo iye adatsogolera ulendo wawo m’chipululu.

14 Ndipo abale ake adamukwiyira, popeza sadazindikire machitidwe a Ambuye; iwonso adamukwiyira pamadzi chifukwa adaumitsa mitima yawo motsutsana ndi Ambuye.

15 Ndiponso, iwo adamukwiyira iye pamene iwo adafika mu dziko la lonjezano, chifukwa iwo adanena kuti iye adatenga ulamuliro wa anthu kuchokera m’manja mwawo; ndipo adafuna kumupha iye.

16 Ndiponso, adakwiya naye chifukwa iye adachoka m’chipululu monga m’mene Ambuye adamulamulira, ndipo adatenga zolemba zimene zidali zozokotedwa pa mapale a mkuwa, pakuti iwo adanena kuti iye adawabera izo.

17 Ndipo kotero adaphunzitsa ana awo kuti adzidana nawo, ndi kuti adziwapha, ndi kuti adziwabera ndi kuwalanda, ndi kuchita zonse akadatha kuwaononga; choncho iwo ali ndi udani wamuyaya kwa ana a Nefi.

18 Pachifukwa chimenechi mfumu Lamani, mwa kuchenjera kwake, ndi chinyengo chake, ndi malonjezo ake abwino, adandinyenga ine, kuti ndabweretsa anthu angawa m’dziko lino, kuti athe kuwawononga; inde, ndipo ife tavutika dzaka dzambirizi m’dzikoli.

19 Ndipo tsopano ine, Zenifu, nditayankhula zinthu zonsezi kwa anthu anga ponena za Alamani, ndidawalimbikitsa kupita kunkhondo ndi nyonga zawo, kuika chikhulupiliro chawo mwa Ambuye; kotero, tidalimbana nawo, maso ndi maso.

20 Ndipo zidachitika kuti tidawathamangitsanso kuchoka m’dziko lathu; ndipo tidawapha ndi kupha kwakukulu kotero kuti sitidawawerenge.

21 Ndipo zidachitika kuti tidabweleranso ku dziko lathu, ndipo anthu anga adayambanso kuweta ziweto zawo, ndi kulima minda yawo.

22 Ndipo tsopano ine, pokhala wokalamba, ndidapereka ufumu pa m’modzi wa ana anga aamuna; kotero, sindiyankhulanso. Ndipo Ambuye adalitse anthu anga. Ameni