Malembo Oyera
Mosiya 7


Mutu 7

Amoni apeza dziko la Lehi-Nefi, kumene Limuhi ali mfumu—Anthu a Limuhi ali mu ukapolo kwa Alamani—Limuhi apereka mbiri yawo—Mneneri (Abinadi) achitira umboni kuti Khristu ndi Mulungu ndi Atate wa zinthu zonse—Amene amafesa zonyasa adzakolola kamvulumvulu, ndipo iwo amene akhulupilira Ambuye adzapulumutsidwa. Mdzaka dza pafupifupi 121 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti mfumu Mosiya itakhala ndi mtendere kosalekeza kwa nthawi ya dzaka dzitatu, iyo idali yofunitsitsa kudziwa zokhudzana ndi anthu amene adapita kukakhala m’dziko la Lehi-Nefi, kapena mu mzinda wa Lehi-Nefi; pakuti anthu ake sadamve kanthu kuchokera kwa iwo kuchokera pamene iwo adachoka mu dziko la Zarahemula; kotero adamtopetsa ndi zoseka zonyazitsa zawo.

2 Ndipo zidachitika kuti mfumu Mosiya idalora kuti khumi ndi asanu ndi m’modzi a amuna awo amphamvu apite ku dziko la Lehi-Nefi, kukafunsa za abale awo.

3 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake adayamba kupita, ali ndi iwo wina Amoni, iye pokhala mwamuna wadzitho ndi wamphamvu, ndi mbadwa ya Zarahemula; ndipo adalinso mtsogoleri wawo.

4 Ndipo tsopano, iwo sadadziwe njira yomwe adayenera kuyenda mchipululu kuti apite ku dziko la Lehi-Nefi; kotero adayendayenda m’chipululu masiku ambiri, ndipo adayendayenda masiku makumi anayi.

5 Ndipo pamene adayendayenda masiku makumi anayi adafika ku phiri, ndilo kumpoto kwa dziko la Shilomu, ndipo iwo adakhoma mahema awo kumeneko.

6 Ndipo Amoni adatenga atatu a abale ake, ndipo maina awo adali Amaleki, Helemu, ndi Hemu, ndipo iwo adatsikira ku dziko la Nefi.

7 Ndipo taonani, adakumana ndi mfumu ya anthu amene adali m’dziko la Nefi, ndi m’dziko la Shilomu; ndipo adazingidwa ndi alonda a mfumu, ndipo adatengedwa, ndipo adamangidwa, ndipo adaikidwa m’ndende.

8 Ndipo zidachitika kuti pamene adakhala m’ndende masiku awiri adabweretsedwanso pamaso pa mfumu ndipo zomangira zawo zidamasulidwa; naima pamaso pa mfumu, ndipo adaloledwa, kapena makamaka adalamulidwa kuti ayankhe mafunso amene iyo iwafunse iwo.

9 Ndipo adati kwa iwo: Taonani, ine ndine Limuhi, mwana wa Nowa, amene adali mwana wa Zenifi, amene adabwera kuchokera m’dziko la Zarahemula kuti akalandire dziko lino, limene lidali dziko la makolo awo, amene adapangidwa mfumu ndi mawu a anthu.

10 Ndipo tsopano ndikufuna kudziwa chifukwa chake mudali olimba mtima kuyandikira makoma a mzindawu, pamene ine ndekha ndidali ndi alonda anga kunja kwa chipata?

11 Ndipo tsopano, m’chifukwa cha ichi ndidalola kuti musungidwe, kuti ndithe kufunsa za inu, kapena ndikadachititsa kuti alonda anga akupheni. Inu mwaloledwa kuyankhula.

12 Ndipo tsopano, pamene Amoni adaona kuti adaloledwa kuyankhula, adapita patsogolo ndipo adagwada pamaso pa mfumu; nadzukanso nati: O mfumu, ndiyamika kwambiri pamaso pa Mulungu lero kuti ndidakali ndi moyo, ndipo ndaloledwa kuyankhula; ndipo ndidzayesera kuyankhula molimba mtima;

13 Pakuti ndatsimikiziridwa kuti ngati mukadandidziwa inu simukadalola kuti ndivekedwe dzingwe izi. Pakuti ine ndine Amoni, ndipo ndine mbadwa ya Zarahemula, ndipo tabwera kuchokera m’dziko la Zarahemula kuti tikafunse zokhudza abale athu, amene Zenifi adawatulutsa m’dzikolo.

14 Ndipo tsopano, zidachitika kuti Limuhi atamva mawu a Amoni, iye adali wokondwa kwambiri, ndipo adati: Tsopano, ine ndikudziwa motsimikiza kuti abale anga amene adali m’dziko la Zarahemula akadali ndi moyo. Ndipo tsopano ndidzakondwera; ndipo mawa ndidzachititsa kuti anthu anga akondwerenso.

15 Pakuti, taonani, tiri mu ukapolo kwa Alamani, ndipo timakhometsedwa msonkho ndipo ndi msonkho umene uli owawa kuti tiunyamule. Ndipo tsopano, taonani, abale athu adzatiwombole ku ukapolo wathu; kapena kuchokera m’manja mwa Alamani, ndipo ife tidzakhala akapolo awo; pakuti n’kwabwino kuti ife tikhale akapolo kwa Anefi kuposa kupereka msonkho kwa mfumu ya Alamani.

16 Ndipo tsopano, Mfumu Limuhi adalamula alonda ake kuti asamangenso Amoni kapena abale ake, koma adapangitsa kuti apite ku phiri lomwe lidali kumpoto kwa Shilomu, ndi kulowa nawo munzinda abale awo, kuti akathe kudya ndi kumwa; ndikukapumula ku ntchito za ulendo wawo; pakuti adamva zowawa zambiri; ndipo adavutika ndi njala, ludzu, ndi kutopa.

17 Ndipo tsopano, zidachitika mawa lake limene mfumu Limuhi adatumiza chilengezo pakati pa anthu ake onse, kotero kuti akasonkhane pamodzi ku kachisi, kuti akamve mawu amene Iye adzanene kwa iwo.

18 Ndipo zidachitika kuti pamene adasonkhana pamodzi, adanena nawo motero, kuti: O inu anthu anga, kwezani mitu yanu ndi kutonthozedwa; pakuti taonani, nthawi yayandikira, kapena siili kutali; pamene sitidzakhalanso omvera kwa adani athu, pakusatengera kulimbana kwathu kwambiri; kumene kwakhala kwa pachabe; komabe ndikhulupilira kuti kwatsala kulimbana kothandiza kuti kuchitike.

19 Kotero, kwezani mitu yanu, ndi kusangalala, ndipo khulupilirani Mulungu; mwa Mulungu yemweyo amene adali Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; komanso, Mulungu yemweyo amene adaturutsa ana a Israeli m’dziko la Igupto, ndikupangitsa kuti awoloke Nyanja Yofiira pa nthaka yowuma, ndipo adawadyetsa iwo mana kuti asatayike m’chipululu; ndi zina zambiri adawachitira iwo.

20 Ndipo kachiwiri, Mulungu yemweyo watulutsa makolo athu m’dziko la Yerusalemu; ndipo wasamala ndi kusunga anthu ake kufikira tsopano; ndipo taonani, chifukwa cha mphulupulu zathu ndi zonyansa zathu watibweretsa muukapolo.

21 Ndipo inu nonse ndinu mboni lero, kuti Zenifi, amene adapangidwa kukhala mfumu ya anthu awa, ndi kufunitsitsa kwake kulandira dziko la makolo ake, kotero ponyengedwa ndi chinyengo ndi luntha la mfumu Lamani, amene adachita pangano ndi mfumu Zenifi, ndipo m’mene adapereka m’manja mwake chuma cha gawo la dziko, kapena ngakhale mzindawo wa Lehi-Nefi, ndi mzinda wa Shilomu; ndi malo ozungulira-

22 Ndipo zonse adazichita, ndi cholinga chokhacho chowabweletsa anthu awa kukhala akugonjera kapena muukapolo. Ndipo taonani, ife pa nthawi ino tikupereka msonkho kwa mfumu ya Alamani, mpaka theka la chimanga chathu, ndi tiligu wathu, ndi mbewu zathu zonse zamtundu uliwonse, ndi theka la zokolola za nkhosa zathu ndi ng’ombe zathu; ndipo ngakhale theka limodzi la zonse zomwe tiri nazo kapena tapeza mfumu ya Alamani imayeza ndendende pa ife, kapena miyoyo yathu.

23 Ndipo tsopano, kodi ichi sichiri chowawa kuchinyamula? Ndipo, masautso athuwa, siaakulu? Tsopano taonani, ndi chifukwa chachikulu bwanji chomwe tiri nacho cholilira.

24 Inde, ndikunena kwa inu, zazikulu ndi zifukwa zomwe tikuyenera kulilira; pakuti taonani angati a abale athu adaphedwa; ndipo mwazi wawo wakhetsedwa pachabe; ndi zonse chifukwa cha kusaweruzika.

25 Pakuti ngati anthu awa akadapanda kugwa mu kulakwitsaa Ambuye sakadalora kuti choipa chachikulu ichi chibwere pa iwo. Koma taonani, sadamvetsere mawu ake; koma kudabuka mikangano pakati pawo; ngakhale kuti adakhetsa mwazi pakati pawo.

26 Ndipo mneneri wa Ambuye adamupha; inde munthu wosankhidwa wa Mulungu, amene adawauza zoipa zawo ndi zonyansa zawo; ndipo adanenera za zinthu zambiri zimene ziri nkudza, inde, ngakhale kubwera kwa Khristu.

27 Ndipo chifukwa adanena kwa iwo kuti Khristu ndiye Mulungu, Atate wa zinthu zonse, ndipo adanena kuti akuyenera kutenga pa iye chifaniziro cha munthu; ndipo chikuyenera kukhala chifaniziro chimene munthu adalengedwa nacho pachiyambi; kapena m’mawu ena, adanena kuti munthu adalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, ndi kuti Mulungu akuyenera kutsika pakati pa ana a anthu, ndi kutenga pa iye mnofu ndi mwazi, ndi kupita pa nkhope ya dziko lapansi—

28 Ndipo tsopano, chifukwa adanena izi, adamupha; ndi zinthu zina zambiri zomwe adazichita zomwe zidatsitsa mkwiyo wa Mulungu pa iwo. Kotero, ndani akudabwa kuti ali muukapolo, ndi kuti adakanthidwa ndi masautso owawa?

29 Pakuti, taonani, Ambuye adati: sindidzathandiza anthu anga pa tsiku la kulakwitsa kwawo; koma ndidzatchinga njira zawo kuti asachite bwino; ndipo zochita zawo zidzakhala ngati chophunthwitsa pamaso pawo.

30 Ndiponso, iye adati: Ngati anthu anga adzabzala zonyansa iwo adzakolola mankhusu pamenepo mu kamvuluvulu; ndipo zotsatira zake ndi chiphe.

31 Ndipo adanenanso kuti: ngati anthu anga adzabzala chidetso adzakolola mphepo ya kum’mawa, yomwe imabweretsa chiwonongeko chofulumira.

32 Ndipo tsopano, taonani, lonjezo la Ambuye lakwaniritsidwa, ndipo inu mwakanthidwa ndi kusautsidwa.

33 Koma mukatembenukira kwa Ambuye ndi cholinga chonse cha mtima; ndi kuika chikhulupiliro chanu mwa iye; ndi kutumikira iye ndi khama lonse la m’maganizo anu, ngati muchita izi, adzatero, monga mwa chifuniro chake ndi chikondwelero chake, kukuwombolani ku ukapolo.