Malembo Oyera
Mosiya 16


Mutu 16

Mulungu amawombola anthu kuchokera ku mkhalidwe wawo wotayika ndi wakugwa—Awo amene ali athupi amakhala ngati kuti palibe chiwombolo—Khristu amadzetsa chiukitso ku moyo wosatha kapena ku chilango chosatha. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti Abinadi atamaliza kuyankhula mawu awa adatambasula dzanja lake ndipo adati: Nthawi idzafika pamene onse adzaona chipulumutso cha Ambuye; pamene dziko lirilonse, fuko, chinenero, ndi anthu adzaonana maso ndi maso ndipo adzavomereza pamaso pa Mulungu kuti ziweruzo zake ndi zolungama.

2 Ndipo pamenepo oipa adzatayidwa; ndipo adzakhala ndi chifukwa chofuulira, ndi kulira, ndi kubuula, ndi kukukuta mano; ndipo izi chifukwa iwo sadamvere mawu a Ambuye; kotero Ambuye sadawawombole.

3 Pakuti iwo ali achithupithupi ndi aumdyerekezi, ndipo mdyerekezi ali ndi mphamvu pa iwo; inde, ngakhale njoka yakale ija imene idanyenga makolo athu oyamba, chimene chidali chifukwa cha kugwa kwawo; chimene chidali chochititsa kuti anthu wonse akhale achithupithupi, azadama, aumdyerekezi, podziwa choipa kwa chabwino, akudzigonjera okha kwa mdyerekezi.

4 Motero anthu onse adatayika; ndipo taonani, akadatayika kotheratu pakadapanda kuti Mulungu adawombola anthu ake ku mkhalidwe wotayika ndi wakugwa.

5 Koma kumbukirani kuti iye amene apitiriza mu chikhalidwe chake chakuthupi, ndi kupitilira m’njira za uchimo ndi kupandukira Mulungu, akhalabe mu mkhalidwe wake wa kugwa ndipo mdyerekezi ali ndi mphamvu zonse pa iye. Kotero ali ngati kuti palibe chiwombolo chomwe chidapangidwa, kukhala mdani kwa Mulungu; ndiponso mdyerekezi ali mdani wa Mulungu.

6 Ndipo tsopano Khristu akadapanda kubwera kudziko lapansi, kunena za zinthu zimene zirinkudza ngati kuti zidadza kale, sipakadakhala chiwombolo.

7 Ndipo ngati Khristu akadapanda kuuka kwa akufa, kapena kudula nsinga za imfa kuti manda asakhale ndi chigonjetso, ndi kuti imfa isakhale ndi mbola, sipakadakhala chiukitso.

8 Koma pali chiukitso, kotero manda alibe chigonjetso, ndipo mbola ya imfa yamezedwa mwa Khristu.

9 Iye ndiye kuwala ndi moyo wapadziko lapansi; inde, kuwala kosatha, kumene sikungadetsedwe konse; inde, ndiponso moyo umene uli wosatha, kuti sipadzakhalanso imfa.

10 Ngakhale thupi lakufa ili lidzavala chisavundi, ndi chivundi ichi chidzabvala chisabvundi, ndipo lidzaimitsidwa pamaso pa bwalo lamilandu la Mulungu; kuti liweruzidwe ndi iye molingana ndi ntchito zawo kaya zili zabwino kapena zoipa—

11 Ngati iwo ali abwino, ku chiukitso cha moyo wosatha ndi chisangalalo; ndipo ngati ali oipa, ku chiukitso cha chiwonongeko chosatha, kuperekedwa kwa mdyerekezi, amene adawagonjetsa, chimene chili chiwonongeko.

12 Atapita molingana ndi zofuna zawo zathupi ndi zokhumba zawo; osamuitana Ambuye pamene manja achifundo adatambasulidwa kwa iwo; pakuti manja achifundo adatambasulidwa kwa iwo; ndipo sadafune; pochenjezedwa za mphulupulu zawo, koma sadapatuke kwa izo; ndipo iwo adalamulidwa kuti alape komabe iwo sadalape.

13 Ndipo tsopano, kodi simukuyenera kunjenjemera ndi kulapa machimo anu, ndi kukumbukira kuti mokhamo ndi kudzera mwa Khristu inu mungapulumutsidwe?

14 Kotero, ngati mumaphunzitsa lamulo la Mose, phunzitsaninso kuti ndi chithunzithunzi cha zinthu zimene zili nkudza—

15 Aphunzitseni iwo kuti chiwombolo chimabwera kudzera mwa Khristu Ambuye, yemwe ali Atate Wamuyaya yemwe. Ameni