Malembo Oyera
Mosiya 20


Mutu 20

Ana aakazi ena a Alamani abedwa ndi ansembe a Nowa—Alamani achita nkhondo pa Limuhi ndi anthu ake—Makamu a Alamani abwenzedwa ndi kutonthozedwa. Mdzaka dza pafupifupi 145–123 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano kudali malo mu Shemuloni kumene ana aakazi a Alamani ankasonkhana pamodzi kuti ayimbe, ndi kuvina, ndi kukondwera.

2 Ndipo zidachitika kuti padali tsiku limodzi owerengeka a iwo adasonkhana kuti akayimbe ndi kuvina.

3 Ndipo tsopano ansembe a mfumu Nowa, pochita manyazi kubwelera ku mzinda wa Nefi, inde; komanso kuopa kuti anthu angawaphe, choncho sadayerekeze kubwelera kwa akazi awo ndi kwa ana awo.

4 Ndipo atakhala m’chipululu, ndikuwapeza ana aakazi a Alamani, adamyata ndi kuwasunzumira;

5 Ndipo pamene adasonkhana koma owerengeka a iwo kukavina, adatuluka m’malo awo obisika ndipo adawatenga ndikuwatengera kuchipululu; inde, makumi awiri mphambu zinayi za ana akazi a Alamani adawatengera m’chipululu.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adapeza kuti ana awo aakazi asowa, adakwiyira anthu a Limuhi, pakuti iwo ankaganiza kuti adali anthu a Limuhi.

7 Kotero adatumiza ankhondo awo; inde, ngakhale mfumu iye mwini idapita patsogolo pa anthu ake; ndipo adakwera kupita m’dziko la Nefi kuti akawononge anthu a Limuhi.

8 Ndipo tsopano Limuhi adali atawatulukira iwo kuchokera ku nsanja, ngakhale makonzedwe awo onse ankhondo adawapeza; kotero adasonkhanitsa anthu ake; ndipo adawadikira iwo m’minda ndi m’nkhalango.

9 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adabwera, kuti anthu a Limuhi adayamba kugwera pa iwo kuchokera kumalo awo odikilira, ndipo adayamba kuwapha.

10 Ndipo zidachitika kuti nkhondoyo idakula kwambiri, pakuti adamenyana ngati mikango pofunafuna nyama.

11 Ndipo zidachitika kuti anthu a Limuhi adayamba kuthamangitsa Alamani patsogolo pawo; komabe iwo sadali ndi theka la kuchuluka ngati Alamani. Koma adamenyera miyoyo yawo, ndi akazi awo, ndi ana awo; kotero adadzipereka ndipo monga ngati zilombo adamenyana.

12 Ndipo zidachitika kuti adapeza mfumu ya Alamani mwa chiwerengero cha akufa awo; komabe iye sadafe, atavulazidwa ndi kusiyidwa pansi, kotero kuthawa kwa anthu ake kudali kofulumira.

13 Ndipo adamgwira, nam’manga mabala ake; ndipo adamubweretsa iye pamaso pa Limuhi, ndipo adati: Taonani, iyi ndi mfumu ya Alamani; iyo itavulazidwa yagwa pakati pa akufa awo, ndipo yasiyidwa; ndipo taonani, tabwera nayo pamaso panu; ndipo tsopano tiyeni tiyiphe.

14 Koma Limuhi adati kwa iwo: Inu musaiphe iyo, koma mubwere nayo kuno kuti ndidzayione. Ndipo adabwera nayo. Ndipo Limuhi adati kwa iyo: Muli ndi chifukwa chanji chobwelera kudzamenyana ndi anthu anga? Taonani, anthu anga sadaphwanye lumbiro limene ndidalumbira kwa inu; choncho, bwanji mukuphwanya lumbiro limene mudawapangira anthu anga?

15 Ndipo tsopano mfumu idati, Ndaphwanya lumbiro chifukwa anthu ako adaba ana aakazi a anthu anga; kotero, m’kukwiya kwanga ndidachititsa anthu anga kubwera kudzamenyana ndi anthu ako.

16 Ndipo tsopano Limuhi sadamve kalikonse pa nkhani iyi; kotero adati, ndifufuza pakati pa anthu anga, ndipo yense wakuchita ichi adzawonongeka. Kotero adachititsa kafukufuku kupangika pakati pa anthu ake.

17 Tsopano pamene Gideoni adamva zimenezi, iye pokhala wamkulu wa ankhondo a mfumu, adatuluka nati kwa mfumu; ndikupempha kuti muleke, ndipo musafufuze anthu awa; ndipo musawaikire iwo chinthu ichi.

18 Pakuti kodi simukukumbukira ansembe a atate anu, amene anthu awa adafuna kuwawononga? Ndipo sali m’chipululu kodi? Ndipo si iwo amene adaba ana aakazi a Alamani?

19 Ndipo tsopano, taonani, ndipo muuzeni mfumu za zinthu izi, kuti iye akauze anthu ake kuti mtima wawo ukhazikike kwa ife; pakuti taonani akukonzekera kale kubwera motsutsana ndi ife; ndipo taonani, tiri owerengeka.

20 Ndipo taonani, akubwera ndi makamu awo aunyinji; ndipo kupatula mfumu iwakhazike mtima pansi kwa ife tikuyenera kuwonongeka.

21 Pakuti kodi mawu a Abinadi sadakwaniritsidwe, zimene adanenera motsutsa ife—ndipo zonsezi chifukwa chakuti sitidamvetsere mawu a Ambuye, ndi kutembenuka kuleka mphulupulu zathu?

22 Tsopano tiyeni titonthoze mfumuyi, ndipo tikakwaniritse lumbiro limene tidalumbilira kwa lye; pakuti n’kwabwino kuti ife tikhale akapolo koposa kuti titaye miyoyo yathu; kotero, tiyeni tileke kukhetsa mwazi wochuluka chotero.

23 Ndipo tsopano Limuhi adauza mfumu zinthu zonse za atate ake, ndi ansembe amene adathawira m’chipululu, ndipo adapereka kwa iwo kutengedwa kwa ana awo aakazi.

24 Ndipo zidachitika kuti mfumu idakhazikitsidwa mtima kwa anthu ake; ndipo idati kwa iwo, tiyeni tipite tikakumane ndi anthu anga, opanda zida; ndipo ndikulumbira kwa inu kuti anthu anga sadzapha anthu anu.

25 Ndipo zidachitika kuti adatsatira mfumuyo; ndipo adapita patsogolo wopanda zida kukakumana ndi Alamani. Ndipo zidachitika kuti iwo adakumana ndi Alamani; ndipo mfumu ya Alamani idagwada pansi pamaso pawo, ndipo idachondelera m’malo mwa anthu a Limuhi.

26 Ndipo pamene Alamani adaona anthu a Limuhi, kuti adali opanda zida, iwo adali ndi chifundo pa iwo ndipo adakhazikitsa mtima pansi kwa iwo, ndipo adabwelera ndi mfumu yawo mu mtendere ku dziko lawo.