Malembo Oyera
Mosiya 29


Mutu 29

Mosiya anena kuti oweruza asankhidwe m’malo mwa mfumu—Mafumu osalungama amatsogolera anthu awo mu uchimo—Alima wamng’ono asankhidwa oweruza wamkulu ndi mawu a anthu—Iyenso ndi mkulu wansembe wa Mpingo—Alima wamkulu ndi Mosiya amwalira. Mdzaka dza pafupifupi 92–91 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano pamene Mosiya adachita izi adatumiza m’dziko lonselo, mwa anthu onse, kufuna kudziwa chifuniro chawo zokhudza amene adzakhale mfumu yawo.

2 Ndipo zidachitika kuti mawu a anthu adabwera, nati: Tikufuna kuti Aroni mwana wanu akhale mfumu yathu ndi wolamulira wathu.

3 Tsopano Aroni adali atapita ku dziko la Nefi, kotero mfumuyo sikadapereka ufumu pa iye; ngakhale Aroni sadadzitengera ufumu pa iye; ngakhale padalibe aliyense wa ana aamuna a Mosiya amene adafuna kutenga pa iwo ufumu.

4 Kotero mfumu Mosiya adatumizanso pakati pa anthu; inde, ngakhale mawu wolembedwa adawatumiza kwa anthu. Ndipo awa ndi mawu amene adalembedwa, kuti:

5 Taonani, O inu anthu anga, kapena abale anga, pakuti ndimakutengani ngati otero, ndikufuna kuti muganizire chifukwa chimene mwaitanidwira kuti muganizire—pakuti mukufunitsitsa kukhala ndi mfumu.

6 Tsopano ndikulengeza kwa inu kuti iye amene ufumu uli omuyenelera waukana, ndipo sadzatenga pa iye ufumuwu.

7 Ndipo tsopano ngati pangakhale wina wosankhidwa m’malo mwake, taonani, ine ndikuopa kuti kungabuke mikangano pakati panu. Ndipo ndani akudziwa, koma kuti mwana wanga, amene ufumu ndi wake, atembenuke mokwiya ndi kukoka gawo la anthu awa pambuyo pake, amene adzayambitsa nkhondo ndi mikangano pakati panu, chimene chidzakhala chifukwa cha kukhetsa mwazi wambiri, ndi kupotoza njira ya Ambuye, inde, ndi kuwononga miyoyo ya anthu ambiri.

8 Tsopano ine ndikunena kwa inu tiyeni tikhale anzeru ndi kulingalira zinthu izi, pakuti ife tiribe ufulu owononga mwana wanga wamwamuna, ngakhale ife sitikuyenera kukhala ndi ufulu uli wonse wa kuwononga wina ngati iye angasankhidwe m’malo mwake.

9 Ndipo ngati mwana wanga angatembenukirenso m’kunyada kwake ndi zinthu zachabechabe iye adzakumbukira zinthu zimene iye adanena, ndi kutenga ulamuliro wake ku ufumu, zimene zingadzachititse iye ndi anthu awa kuchita tchimo lalikulu.

10 Ndipo tsopano tiyeni tikhale anzeru ndi kuyang’aniratu ku zinthu izi, ndi kuchita chimene chidzapangitse mtendere wa anthu awa.

11 Kotero, ndidzakhala mfumu yanu masiku anga otsala; komabe, tiyeni tisankhe oweruza, kuti aweruze anthu awa molingana ndi malamulo athu; ndipo tidzakonza mwatsopano zochitika za anthu awa, pakuti tidzasankha anthu anzeru kuti akhale oweruza, amene adzaweruza anthu awa molingana ndi malamulo a Mulungu.

12 Tsopano nkwabwino kuti munthu aweruzidwe ndi Mulungu kuposa munthu, pakuti ziweruzo za Mulungu ndi zolungama nthawi zonse, koma ziweruzo za munthu sizikhala zolungama nthawi zonse.

13 Kotero, ngati kukadakhala kotheka kuti mungakhale ndi anthu wolungama kuti akhale mafumu anu, amene akadakhazikitsa malamulo a Mulungu, ndi kuweruza anthu awa malinga ndi malamulo ake, inde, ngati mungakhale ndi anthu m’malo mwa mafumu anu amene akadachita ngakhale monga atate anga Benjamini adawachitira anthu awa—ndikunena kwa inu, ngati ichi chingakhale chotere nthawi zonse, pamenepo kungakhale koyenera kuti nthawi zonse mudzikhala ndi mafumu wolamulira pa inu.

14 Ndipo inenso ndagwira ntchito ndi mphamvu zonse ndi maluso amene ndakhala nawo, kukuphunzitsani malamulo a Mulungu, ndi kukhazikitsa mtendere padziko lonse lapansi, kuti pasakhale nkhondo kapena mikangano, kapena kuba, kapena kulandana, kapena kupha, kapena kusaweruzika kwa mtundu uliwonse;

15 Ndipo aliyense amene adachita mphulupulu, ine ndidamulanga mogwirizana ndi mlandu umene iye adachita, mogwirizana ndi lamulo limene lidapatsidwa kwa ife ndi makolo athu.

16 Tsopano ndinena kwa inu, kuti chifukwa si anthu onse wolungama, sikoyenera kuti mukhale ndi mfumu kapena mafumu wolamulira inu.

17 Pakuti, taonani, ndi kusaweruzika kochuluka bwanji kumene mfumu yoipa imachititsa kuti kupangidwe, inde, ndi chiwonongeko chachikulu chotani!

18 Inde, kumbukilani mfumu Nowa, kuipa kwake ndi zonyansa zake, ndiponso kuipa ndi zonyansa za anthu ake. Taonani chiwonongeko chachikulu chotani chomwe chidawabwelera; ndiponso chifukwa cha mphulupulu zawo adabweretsedwa mu ukapolo.

19 Ndipo kupanda kulowelera kwa Mlengi wawo wanzeru zonse, ndipo chifukwa cha kulapa kwawo koona mtima, iwo akadayenera kukhalabe muukapolo wosapeweka kufikira tsopano.

20 Koma taonani, adawawombola chifukwa adadzichepetsa pamaso pake; ndipo chifukwa chakuti adalilira mwamphamvu kwa iye adawawombola iwo kuchokera mu ukapolo; ndipo ndi motero Ambuye amagwira ntchito ndi mphamvu yake muzochitika zonse pakati pa ana a anthu, kutambasula mkono wachifundo kwa iwo amene amamukhulupilira iye.

21 Ndipo taonani, tsopano ndikunena kwa inu, simungathe kuchotsa mfumu yosalungama, koma ndi mikangano yambiri, ndi kukhetsa mwazi wambiri.

22 Pakuti taonani, ali ndi abwenzi ake mu mphulupulu, ndipo amasunga alonda ake mozungulira iye; ndipo amang’amba malamulo a iwo amene adachita ufumu m’chilungamo asadabwere iye; ndipo amapondereza pansi pa mapazi ake malamulo a Mulungu;

23 Ndipo amakhazikitsa malamulo, ndipo amawatumiza iwo pakati pa anthu ake, inde, malamulo motsatira chikhalidwe cha kuipa kwake; ndipo yense wosamvera malamulo ake amamuchititsa kuti awonongedwe; ndipo aliyense amene apandukira iye adzatumiza ankhondo ake kukamenyana nawo kunkhondo, ndipo ngati angathe adzawawononga; ndipo motero mfumu yosalungama imapotoza njira za chilungamo chonse.

24 Ndipo tsopano taonani ine ndikunena kwa inu, sikuli koyenera kuti zonyansa zotere zibwere pa inu.

25 Kotero, sankhani inu ndi mawu a anthu awa, oweruza, kuti muweruzidwe monga mwa malamulo amene makolo athu adakupatsani, amene ali olondola, amene adapatsidwa kwa iwo ndi dzanja la Ambuye.

26 Tsopano sizimachitikachitika kuti mawu a anthu akhumbe chirichonse chotsutsana ndi cholungama; koma zimachitikachitika kwa anthu ochepa kulakalaka zinthu zosayenera; kotero ichi musunge ndi kuchipanga kukhala lamulo lanu—kuchita zochitika zanu ndi mawu a anthu.

27 Ndipo ngati nthawi ifika kuti mawu a anthu asankhe mphulupulu, ndiyo nthawi yomwe ziweruzo za Mulungu zidzafika pa inu; inde, ndiyo nthawi yomwe adzakuyenderani ndi chiwonongeko chachikulu monga momwe adayendera dziko lino mpaka pano.

28 Ndipo tsopano ngati muli nawo oweruza, ndipo sakukuweruzani molingana ndi lamulo limene laperekedwa, mukhonza kuchititsa kuti aweruzidwe ndi oweruza wapamwamba.

29 Ngati oweruza anu apamwamba sakuweruza ziweruzo zolungama, mudzachititsa kuti chiwerengero chochepa cha oweruza anu aang’ono asonkhane pamodzi, ndipo adzaweruza oweruza anu apamwamba, monga mwa mawu a anthu.

30 Ndipo ndikukulamulirani kuchita izi poopa Ambuye; ndipo ndikukulamulirani kuchita izi, ndipo kuti musakhale mfumu; kuti ngati anthu awa achita machimo ndi mphulupulu adzayankhidwa pa mitu yawo.

31 Pakuti taonani ndikunena kwa inu, machimo a anthu ambiri abwera chifukwa cha mphulupulu za mafumu awo; kotero mphulupulu zawo zayankhidwa pamitu ya mafumu awo.

32 Ndipo tsopano ine ndikukhumba kuti kusalingana uku kusakhalenso mu dziko lino, makamaka pakati pa anthu anga awa; koma ndikukhumba kuti dziko lino likhale laufulu, ndipo munthu aliyense athe kusangalala ndi maufulu ndi mwayi wake mofanana, malinga ngati Ambuye akuona kuti n’koyenera kuti tikhale ndi moyo ndi kulandira dzikoli, inde, ngakhale malinga ngati m’badwa zathu zikadalipo pa nkhope ya dzikoli.

33 Ndipo zinthu zina zambiri mfumu Mosiya adalembera kwa iwo, kufutukura kwa iwo mayesero ndi mavuto onse a mfumu yolungama, inde, zowawa zonse za moyo za anthu awo, ndiponso kung’ung’udza kwa anthu kwa mfumu yawo; ndipo adawafotokozera zonse.

34 Ndipo adawauza kuti izi sizikuyenera kuchitika; koma cholemetsa chikhale pa anthu onse, kuti aliyense asenze gawo lake.

35 Ndipo iye adawafutukuliranso iwo kuipa konse komwe adagwira ntchito, pokhala ndi mfumu yosalungama yowalamulira;

36 Inde, mphulupulu zake zonse ndi zonyansa, ndi nkhondo zonse, ndi mikangano, ndi kukhetsa mwazi, ndi kuba, ndi kulandana, ndi kuchita zadama, ndi mitundu yonse ya mphulupulu zomwe sizingawerengedwe—kuwauza kuti zinthu izi sizikuyenera kuchitika, kuti zidasonyeza kunyansidwa komveka ndi malamulo a Mulungu.

37 Ndipo tsopano zidachitika, atamaliza mfumu Mosiya kutumiza zinthu izi pakati pa anthu adakhutitsidwa ndi choonadi cha mawu ake.

38 Kotero iwo adasiya zikhumbo zawo za mfumu, ndipo adakhala odera nkhawa kwambiri kuti munthu aliyense akhale ndi mwayi wofanana m’dziko lonselo; inde, ndipo munthu aliyense adasonyeza kufunitsitsa kuyankha chifukwa cha machimo ake.

39 Kotero, zidachitika kuti iwo adasonkhana pamodzi m’magulu m’dziko lonselo, kuti ayankhule mawu awo zokhudza amene akuyenera kukhala oweruza awo, kuti aweruze iwo monga mwa lamulo limene lidapatsidwa kwa iwo; ndipo adakondwera kwakukulu chifukwa cha ufulu umene udapatsidwa kwa iwo.

40 Ndipo iwo adakhala ndi chikondi chachikulu kwambiri kwa Mosiya; inde, adamulemekeza koposa munthu wina aliyense; pakuti iwo sadayang’ane pa iye monga wolamulira wankhanza amene adali kufunafuna phindu, inde, chifukwa cha phindu limene liipitsa moyo; pakuti sadawalande chuma chawo, ndipo sadakondwere mu kukhetsa mwazi; koma iye adakhazikitsa mtendere m’dzikolo, ndipo adalora kwa anthu ake kuti awomboledwe ku ukapolo wa mtundu uliwonse; kotero iwo adamulemekeza iye, inde, mopitilira muyezo.

41 Ndipo zidachitika kuti iwo adaika oweruza kuti aziwalamulira, kapena kuti aweruze iwo molingana ndi lamulo; ndipo izi adachita m’dziko lonselo.

42 Ndipo zidachitika kuti Alima adasankhidwa kukhala oweruza wamkulu woyamba, iye pokhalanso mkulu wansembe, atate ake atapereka udindo pa iye, ndipo atamupatsa iye udindo wokhudza zochitika zonse za mpingo.

43 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima adayenda m’njira za Ambuye, ndipo adasunga malamulo ake, ndipo adaweruza ziweruzo zolungama; ndipo mudali mtendere wosalekeza m’dzikomo.

44 Ndipo kotero udayamba ulamuliro wa oweruza m’dziko lonse la Zarahemula, pakati pa anthu onse amene ankatchedwa Anefi; ndipo Alima adali oweruza oyamba ndi wamkulu.

45 Ndipo tsopano zidachitika kuti atate ake adamwalira, ali ndi dzaka makumi asanu ndi atatu mphambu ziwiri, atakhala ndi moyo wakukwaniritsa malamulo a Mulungu.

46 Ndipo zidachitika kuti Mosiya adamwaliranso, m’chaka cha makumi atatu ndi mphambu zitatu dza ulamuliro wake, ali ndi dzaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zitatu; kupanga mu zonse, dzaka mazana asanu ndi zisanu ndi zinayi kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu.

47 Ndipo motero adamaliza ulamuliro wa mafumu pa anthu a Nefi; ndipo motero adatha masiku a Alima, yemwe adali woyambitsa mpingo wawo.

Print