Malembo Oyera
Mosiya 21


Mutu 21

Anthu a Limuhi akanthidwa ndi kugonjetsedwa ndi Alamani—Anthu a Limuhi akumana ndi Amoni ndipo atembenuka—Iwo awuza Amoni za mapale makumi awiri ndi anayi a Ayeredi. Mdzaka dza pafupifupi 122–121 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Limuhi ndi anthu ake adabwelera ku mzinda wa Nefi, ndipo adayamba kukhalanso m’dzikolo mu mtendere.

2 Ndipo zidachitika kuti patatha masiku ambiri Alamani adayambanso kuutsidwa mu mkwiyo motsutsana ndi Anefi ndikuyamba kulowa m’malire a dzikolo mozungulira.

3 Tsopano iwo sadayerekeze kuwapha iwo, chifukwa cha lumbiro limene mfumu yawo idapanga kwa Limuhi; koma ankawakantha m’masaya awo, ndipo adaonetsa ulamuliro pa iwo; ndipo adayamba kuwasenzetsa zothodwetsa pa misana yawo, ndi kuwathamangitsa iwo monga amachitira bulu wosayankhula—

4 Inde, zonsezi zidachitika kuti mawu a Ambuye akwaniritsidwe.

5 Ndipo tsopano masautso a Anefi adali aakulu, ndipo padalibe njira yoti akadadzipulumutsira iwo eni kuchokera m’manja mwawo, pakuti Alamani adali atawazungulira iwo mbali zonse.

6 Ndipo zidachitika kuti anthu adayamba kung’ung’udza ndi mfumu chifukwa cha masautso awo; ndipo adayamba kufuna kupita kukamenyana nawo kunkhondo. Ndipo iwo adasautsa mfumu mowawa ndi madandaulo awo; kotero adawapatsa iwo kuti achite monga mwa zokhumba zawo.

7 Ndipo adasonkhananso pamodzi ndi kuvala zida zawo, ndipo adapita kukamenyana ndi Alamani kuti akawathamangitse m’dziko lawo.

8 Ndipo zidachitika kuti Alamani adawamenya iwo, ndipo adawathamangitsira iwo m’mbuyo, ndipo adapha ambiri a iwo.

9 Ndipo tsopano kudali kulira kwakukulu ndi maliro pakati pa anthu a Limuhi, mkazi wamasiye kulilira mamuna wake, mwana wamamuna ndi mwana wamkazi akulilira atate awo, ndi abale chifukwa cha abale awo.

10 Ndipo padali akazi amasiye ambiri m’dzikomo; ndipo iwo adali kulira kwambiri tsiku ndi tsiku, pakuti mantha aakulu a Alamani adadza pa iwo.

11 Ndipo zidachitika kuti kulira kwawo kosalekeza kudautsa otsala a anthu a Limuhi kuti akwiye motsutsana ndi Alamani; ndipo adapitanso kunkhondo, koma adabwenzedwanso m’mbuyo, atavutika ndikutayika kwambiri.

12 Inde, adapitanso ngakhale kachitatu, ndi kukamva zowawa m’chimodzimodzi; ndipo iwo omwe sadaphedwe adabweleranso ku mzinda wa Nefi.

13 Ndipo iwo adadzichepetsa iwo eni mpaka ku fumbi, kugonjera iwo eni ku goli la ukapolo, kudzipereka okha kuti akanthidwe, ndi kuthamangitsidwira uku ndi uko, ndi kulemetsedwa, molingana ndi zikhumbo za adani awo.

14 Ndipo adadzichepetsadi ngakhale mu kuya kwa kudzichepetsa; ndipo adafuula mwamphamvu kwa Mulungu; inde, ngakhale usana wonse adalilira kwa Mulungu wawo kuti awawombole ku masautso awo.

15 Ndipo tsopano Ambuye adachedwa kumva kulira kwawo chifukwa cha mphulupulu zawo; komabe Ambuye adamva kulira kwawo, ndipo adayamba kufewetsa mitima ya Alamani kuti adayamba kuchepetsa zolemetsa zawo; komabe Ambuye sadaone koyenera kuwawombola iwo kutuluka mu ukapolo.

16 Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kuchita bwino pang’onopang’ono m’dzikomo, ndipo adayamba kudzala mbewu mochulukira, ndi nkhosa, ndi ng’ombe, kuti sadavutike ndi njala.

17 Tsopano padali kukula kwa chiwerengero cha akazi kuposa mene adaliri amuna; kotero mfumu Limuhi idalamulira kuti mzibambo aliyense apereke thandizo kwa amasiye ndi ana awo, kuti angathe kufa ndi njala; ndipo izi adachita chifukwa cha kukula kwa chiwerengero chawo cha amene adaphedwa.

18 Tsopano anthu a Limuhi adakhala pamodzi mu gulu monga momwe zidaliri zotheka, ndipo adasunga mbewu zawo ndi ziweto zawo;

19 Ndipo mfumu payokha sidadzidalire yokha kunja kwa makoma a mzindawo; pokhapokha ngati ingatenge alonda ake pamodzi naye, kuopa kuti ingagwere m’manja mwa Alamani.

20 Ndipo idapangitsa kuti anthu ake adziyang’anira dziko mozungulira kuti mwa njira ina angatenge ansembe aja amene adathawira m’chipululu, amene adaba ana aakazi a Alamani, ndipo amene adapangitsa chiwonongeko chachikulu chotero kuti chidze pa iwo.

21 Pakuti adafuna kuwagwira kuti awalange; pakuti adabwera m’dziko la Nefi usiku; ndipo adatenga chimanga chawo ndi zinthu zawo zambiri zamtengo wapatali; kotero adakhala akuwadikilira.

22 Ndipo zidachitika kuti kudalibenso chosokoneza pakati pa Alamani ndi anthu a Limuhi, ngakhale mpaka nthawi yomwe Amoni ndi abale ake adalowa m’dzikolo.

23 Ndipo mfumu pokhala kunja kwa zipata za mzinda ndi alonda ake adapeza Amoni ndi abale ake; ndipo poganiza kuti iwo adali ansembe a Nowa kotero adapangitsa kuti iwo atengedwe, ndi kumangidwa, ndi kuponyedwa mu ndende. Ndipo akadakhala ansembe a Nowa akadawapangitsa kuti aphedwe.

24 Koma pamene adapeza kuti sadali iwowo, koma kuti adali abale ake, ndipo adali atabwera kuchokera m’dziko la Zarahemula, adadzazidwa ndi chisangalalo chachikulu.

25 Tsopano mfumu Limuhi idali itatumiza, pambuyo pa kubwera kwa Amoni, chiwerengero chochepa cha anthu kufunafuna dziko la Zarahemula; koma sadalipeze, ndipo adatayika m’chipululu.

26 Komabe, adapeza dziko lomwe lidali ndi anthu; inde, dziko limene lidakutidwa ndi mafupa owuma; inde, dziko limene lidali ndi anthu ndipo lidawonongedwa; ndipo iwo, poganizira kuti liri m’dziko la Zarahemula, adabwelera ku dziko la Nefi, atafika m’malire a m’dzikomo masiku ochepa pambuyo pa kubwera kwa Amoni.

27 Ndipo iwo adabwera ndi zolemba; ngakhale zolembedwa za anthu amene adawapeza mafupa awo; ndipo zidazokotedwa pa mapale a miyala.

28 Ndipo tsopano Limuhi adadzadzidwanso ndi chisangalalo pophunzira kuchokera mkamwa mwa Amoni kuti mfumu Mosiya adali ndi mphatso yochokera kwa Mulungu; imene ankatha kumasulira zozokota zotere; inde, ndipo Amoni nayenso adakondwera.

29 Komabe Amoni ndi abale ake adadzadzidwa ndi chisoni chifukwa ambiri a abale awo adaphedwa;

30 Komanso kuti mfumu Nowa ndi ansembe ake idapangitsa anthu kuchita machimo ochuluka ndi mphulupulu kwa Mulungu; ndipo iwonso adachita chisoni chifukwa cha imfa ya Abinadi; ndiponso chifukwa cha kuchoka kwa Alima ndi anthu amene adapita naye limodzi, amene adali atapanga mpingo wa Mulungu kudzera mu nyonga ndi mphamvu ya Mulungu, ndi chikhulupiliro pa mawu amene adayankhulidwa ndi Abinadi.

31 Inde, iwo adalira chifukwa cha kuchoka kwawo, pakuti sadadziwe kumene iwo adathawira. Tsopano akadagwirizana nawo mokondwera, chifukwa iwo eniwo adali atachita pangano ndi Mulungu kuti amtumikira ndi kusunga malamulo ake.

32 Ndipo tsopano kuchokera pakubwera kwa Amoni, Mfumu Limuhi adali atalowanso mu pangano ndi Mulungu, ndiponso ambiri a anthu ake, kuti amtumikire ndi kusunga malamulo ake.

33 Ndipo zidachitika kuti mfumu Limuhi ndi ambiri a anthu ake adali akufuna kubatizidwa; koma padalibe m’dzikomo amene adali ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu. Ndipo Amoni adakana kuchita chinthu ichi, pakudziona ngati wantchito wosayenelera.

34 Kotero iwo sadadzipangire okha kukhala mpingo, kuyembekezera pa Mzimu wa Ambuye. Tsopano iwo adali ofunitsitsa kukhala ngakhale ngati Alima ndi abale ake amene adathawira kuchipululu.

35 Adali ofunitsitsa kubatizidwa monga mboni ndi umboni wakuti adali ofunitsitsa kutumikira Mulungu ndi mtima wawo wonse; komabe iwo adatalikitsa nthawi; ndipo nkhani ya ubatizo wawo idzaperekedwa pambuyo pake.

36 Ndipo tsopano kuphunzira konse kwa Amoni ndi anthu ake, ndi mfumu Limuhi ndi anthu ake, kudali koti adziwombole iwo wokha kuchokera m’manja mwa Alamani ndi ku ukapolo.

Print