Malembo Oyera
Mosiya 12


Mutu 12

Abinadi amangidwa chifukwa chonenera kuwonongedwa kwa anthu ndi imfa ya Mfumu Nowa—Ansembe onyenga atchula malemba ndipo anamizira kusunga chilamulo cha Mose—Abinadi ayamba kuwaphunzitsa Malamulo Khumi. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti patatha dzaka ziwiri zimene Abinadi adabwera pakati pawo modzibisa, kuti iwo sadamudziwe iye, ndipo adayamba kunenera pakati pawo, kuti: Motero Ambuye andilamulira ine, nati—Abinadi, pita ndipo unenere kwa anthu anga awa; pakuti aumitsa mitima yawo motsutsana ndi mawu anga; sadalape zoipa zawo; kotero, ndidzawalanga mu mkwiyo wanga, inde, mu mkwiyo wanga waukali ndidzawalanga chifukwa cha mphulupulu zawo ndi zonyansa zawo.

2 Inde, tsoka kwa m’badwo uwu! Ndipo Ambuye adati kwa ine: Tambasula dzanja lako, ndipo nenera, nati: Akutero Ambuye, kudzachitika kuti m’badwo uwu, chifukwa cha mphulupulu zawo, udzatengedwa mu ukapolo, ndipo udzakanthidwa pa tsaya; inde, ndipo udzathamangitsidwa ndi anthu, ndipo udzaphedwa; ndipo mbalame zamlengalenga, ndi agalu, inde, ndi zilombo, zidzadya nyama yawo.

3 Ndipo zidzachitika kuti moyo wa mfumu Nowa udzayesedwa ngati chovala m’ng’anjo yotentha; pakuti adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye.

4 Ndipo zidzachitika kuti ndidzakantha awa anthu anga ndi masautso owawa, inde, ndi njala ndi mliri; ndipo ndidzawachititsa kuti adzalire tsiku lonse.

5 Inde, ndipo ine ndidzachititsa kuti adzakhala ndi zothodwetsa pamisana yawo; ndipo adzathamangitsidwa patsogolo ngati bulu wosayankhula.

6 Ndipo zidzachitika kuti ndidzatumiza matalala pakati pawo, ndipo adzawakantha; ndipo adzakanthidwa ndi mphepo ya kum’mawa; ndipo tizilombo tidzasakaza dziko lawo, ndi kudya mbewu zawo.

7 Ndipo adzakanthidwa ndi mliri waukulu—ndipo zonsezi ndidzazichita chifukwa cha mphulupulu zawo ndi zonyansa zawo.

8 Ndipo zidzachitika kuti kupatula iwo alape ndidzawawononga iwo kotheratu kuchoka pa nkhope ya dziko lapansi; koma adzasiya zolemba pambuyo pawo, ndipo ndidzawasungira ku mitundu ina yomwe idzalandira dzikolo; inde, ngakhale ichi ndidzachita, kuti ndiulure zonyansa za anthu awa kwa a mitundu ina. Ndipo zinthu zambiri Abinadi adanenera motsutsa anthu awa.

9 Ndipo zidachitika kuti adakwiya naye; ndipo adamugwira, ndipo adamutenga iye ali womangidwa pamaso pa mfumu; nanena kwa mfumu, Taonani, tabwera ndi munthu pamaso panu, amene adanenera zoipa za anthu anu, ndi kuti Mulungu adzawawononga.

10 Ndipo aneneranso zoipa za moyo wanu, ndipo akuti moyo wanu udzakhala ngati chovala m’ng’anjo yamoto.

11 Ndipo kachiwiri, iye akunena kuti inu mudzakhala ngati phesi, ngakhale ngati phesi louma la m’munda, limene limaponderezedwa ndi nyama ndi kuponderezedwa ndi mapazi.

12 Ndiponso, akunena inu mudzakhala ngati maluwa a nthula, amene, pamene acha ndithu, ngati mphepo iwomba, amaulutsidwa pa nkhope ya dziko. Ndipo akunamizira ngati Ambuye anena izi. Ndipo akunena izi zonse zidzafika pa inu pokhapokha inu mulape, ndipo ichi chifukwa cha mphulupulu zanu.

13 Ndipo tsopano, inu mfumu, mwachita choipa chachikulu chotani, kapena machimo akulu ati amene anthu anu achita, kuti ife titsutsidwe ndi Mulungu kapena kuweruzidwa ndi munthu uyu?

14 Tsopano, O mfumu, taonani, ife tili opanda mlandu, ndipo inu, O mfumu, simudachimwe; kotero, munthu uyu wakunamizirani, ndipo wanenera pachabe.

15 Ndipo taonani, ndife olimba, sitidzalowa mu ukapolo, kapena kutengedwa ukapolo ndi adani athu; inde, ndipo mwachita bwino m’dziko, ndipo mudzachitanso bwino.

16 Taonani, munthuyo ndi uyu, timpereka m’manja mwanu; mukhonza kuchita naye mwakufuna kwanu.

17 Ndipo zidachitika kuti mfumu Nowa idapangitsa kuti Abinadi aponyedwe mu ndende; ndipo adalamulira ansembe asonkhane pamodzi, kuti akachite nawo zokambirana za zomwe akuyenera kuchita naye.

18 Ndipo zidachitika kuti adati kwa mfumu, Mubweretseni kuno kuti timufunse; ndipo mfumu idalamulira kuti abwere naye pamaso pawo.

19 Ndipo adayamba kumfunsa iye, kuti akamukole, kuti akakhale nacho chomuzengera mlandu iye; koma iye adawayankha molimba mtima, ndipo adatsutsa mafunso awo onse, inde, kwa kuzizwa kwawo; pakuti adawayankha m’mafunso awo onse, ndikuwasokoneza m’mawu awo onse.

20 Ndipo zidachitika kuti m’modzi wa iwo adati kwa Iye: Mawu olembedwawo amatanthauza chiyani, amene adaphunzitsidwa ndi makolo athu, nati:

21 Ndi pokongola bwanji pamapiri ndi mapazi a iye amene amabwera ndi uthenga wabwino; amene amafalitsa mtendere; amene amabweretsa uthenga wabwino wa zabwino; amene amafalitsa chipulumutso; amene amanena kwa Ziyoni, Mulungu Wako akulamulira;

22 Alonda ako adzakweza mawu; ndi mawu pamodzi adzayimba; pakuti adzaona maso ndi maso pamene Ambuye adzabweretsa kachiwiri Ziyoni;

23 Sangalalani; imbani pamodzi inu mabwinja a Yerusalemu; pakuti Ambuye watonthoza anthu ake, wawombola Yerusalemu;

24 Ambuye waika poyera mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse, ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu?

25 Ndipo tsopano Abinadi adati kwa iwo: Kodi ndinu ansembe, ndi kumanamizira kuphunzitsa anthu awa, ndi kumvetsa mzimu wa kunenera, koma mukufuna kudziwa kwa ine chimene zinthu izi zikutanthauza?

26 Ndikunena kwa inu, tsoka likhala kwa inu chifukwa chopotoza njira za Ambuye! Pakuti ngati mukudziwa izi simudaziphunzitse; kotero, inu mwapotoza njira za Ambuye.

27 Simudaike mitima yanu pakuzindikira; kotero, simudakhale anzeru. Kotero, mumawaphunzitsa chiyani anthu awa?

28 Ndipo adati: Ife timaphunzitsa chilamulo cha Mose.

29 Ndipo adanenanso kwa iwo: Ngati mumaphunzitsa chilamulo cha Mose, bwanji simuchisunga? Chifukwa chiyani mumaika mitima yanu pa chuma? Ndi chifukwa chiyani mukuchita zadama ndikuwononga mphamvu zanu ndi akazi achigololo, inde, ndi kuchititsa anthu awa kuchimwa, kuti Ambuye ali ndi chifukwa chonditumira ine kunenera motsutsa anthu awa, inde, ngakhale choipa chachikulu motsutsa anthu awa?

30 Simukudziwa kuti ndikunena zoona? Inde, mukudziwa kuti ndikunena zoona; ndipo mukuyenera kunjenjemera pamaso pa Mulungu.

31 Ndipo zidzachitika kuti mudzakanthidwa chifukwa cha mphulupulu zanu, pakuti mwanena kuti mumaphunzitsa lamulo la Mose. Ndipo mukudziwa chiyani za lamulo la Mose? Kodi chipulumutso chimabwera mwa lamulo la Mose? Mukuti chani?

32 Ndipo iwo adayankha nati chipulumutso chimabwera mwa lamulo la Mose.

33 Koma tsopano Abinadi adati kwa iwo: Ndikudziwa ngati musunga malamulo a Mulungu mudzapulumutsidwa; inde, ngati mukusunga malamulo amene Ambuye adampatsa Mose m’phiri la Sinai, akuti;

34 Ine ndine Ambuye Mulungu wako, amene ndidakutulutsa m’dziko la Igupto, m’nyumba yaukapolo.

35 Usakhale ndi Mulungu wina koma Ine.

36 Usadzipangire iwe fano losema; kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi.

37 Tsopano Abinadi adati kwa iwo, Kodi inu mwachita zonsezi? Ndikunena kwa inu, Iyayi, simudachite. Ndipo kodi inu mwaphunzitsa anthu awa kuti akuyenera kuchita zinthu zonsezi? Ndikunena kwa inu, Ayi, simudachite.