Malembo Oyera
2 Nefi 25


Mutu 25

Nefi alemekeza m’zomveka—Maulosi a Yesaya adzamveka bwino m’masiku otsiriza—Ayuda adzabwelera ku Babulo, adzapachika Mesiya, ndipo adzamwazikana ndi kukwapulidwa—Adzabwenzeretsedwa pamene adzakhulupilira mwa Mesiya—Iye adzabwera koyamba m’dzaka mazana asanu ndi chimodzi Lehi atachoka ku Yerusalemu—Anefi asunga lamulo la Mose ndipo akhulupilira mwa Khristu, amene ali Oyera wa Israeli. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano, ine, Nefi, ndikuyankhula pang’ono zokhudzana ndi mawu amene ine ndalemba, amene adayankhulidwa ndi pakamwa pa Yesaya. Pakuti taonani, Yesaya adayankhula zinthu zambiri zimene zidali zovuta kwa anthu ambiri kuzimvetsa; pakuti iwo sadziwa zokhudzana ndi kunenera kotere pakati pa Ayuda.

2 Pakuti ine, Nefi, sindidawaphunzitse zambiri zokhudzana ndi machitidwe a Ayuda; pakuti ntchito zawo zidali ntchito zamumdima, ndipo zochita zawo zidali zochita zonyansa.

3 Kotero, ndikulemba kwa anthu anga, kwa onse amene adzalandire kuchoka pano zinthu izi zimene ndazilemba, kuti iwo akadziwe ziweruzo za Mulungu, kuti zidzafika pa maiko onse, molingana ndi mawu amene iye adayankhula.

4 Kotero, mvetserani, Inu anthu anga, amene muli a nyumba ya Israeli, ndipo tcherani khutu ku mawu anga; pakuti chifukwa mawu a Yesaya ndi osamveka kwa inu, komabe iwo ndiomveka kwa onse amene adzadzidwa ndi mzimu wa uneneri. Koma ine ndikupereka kwa inu uneneri, molingana ndi mzimu umene uli mwa ine; kotero ndidzanenera molingana ndi kumveka komwe kwakhala mwa ine kuyambira mu nthawi yomwe ine ndidaturuka ku Yerusalemu ndi atate anga; pakuti taonani, moyo wanga ukondwera mu kumvetsa kwa anthu anga, kuti iwo aphunzire.

5 Inde, ndipo moyo wanga ukondwera mu mawu a Yesaya, pakuti ine ndidachokera ku Yerusalemu, ndipo maso anga adaona zinthu za Ayuda, ndipo ndikudziwa kuti Ayuda amamvetsa zinthu za uneneri, ndipo palibe anthu ena amene amamvetsa za zinthu zimene zidayankhulidwa kwa Ayuda ngati iwo, kupatula kuti iwo adaphunzitsidwa motsatira chikhalidwe cha zinthu za Ayuda.

6 Koma taonani, ine, Nefi, sindidaphunzitse ana monga mwa chikhalidwe cha Ayuda; koma taonani, ine, mwa ine mwini, ndidakhalapo m’Yerusalemu, kotero ndikudziwa zokhudzana ndi madera ozungulira; ndipo ndidatchulapo kwa ana anga zokhudzana ndi ziweruzo za Mulungu, zimene zidachitika pakati pa Ayuda, kwa ana anga, molingana ndi zonse zimene Yesaya adayankhula, ndipo ine sindizilemba.

7 Koma taonani, ndikupitiliza ndi uneneri wanga, molingana ndi kumveka kwanga; m’menemo ndikudziwa kuti palibe munthu akhonza kulakwa; komabe, m’masiku amene uneneri wa Yesaya udzakwaniritsidwe anthu adzadziwadi mwa ndithu, pa nthawi zimene izi zidzachitike.

8 Kotero, ndizofunikira kwa ana a anthu, ndipo iye amene ayesa kuti sizili, kwa amenewo ndidzayankhula mwapadera, ndipo ndidzachepetsa mawu kwa anthu anga omwe; pakuti ndikudziwa kuti adzakhala a mtengo wapatali kwa iwo m’masiku otsiriza; pakuti pa tsikulo iwo adzamvetsetsa; kotero, chifukwa cha ubwino wawo ndawalembera.

9 Ndipo monga m’badwo umodzi udawonongedwa pakati pa Ayuda chifukwa cha mphulupulu, ngakhale choncho iwo adawonongedwa kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo malingana ndi mphulupulu zawo; ndipo palibe wina aliyense wa iwo adawonongedwa kupatula kuti zidaneneredwa ndi aneneri a Ambuye.

10 Kotero, iwo adauzidwa zokhudzana ndi chiwonongeko chimene chikuyenera kudzabwera kwa iwo, mosachedwa atangochoka atate anga ku Yerusalemu; komabe, iwo adaumitsa mitima yawo; ndipo molingana ndi uneneri wanga iwo adawonongedwa, kupatula iwo amene adatengedwa ku ukapolo ku Babulo.

11 Ndipo tsopano izi ndikuyankhula chifukwa cha mzimu umene uli mwa ine. Ndipo ngakhale kuti iwo atengedwera kutali, adzabweleranso, ndikutenga dziko la Yerusalemu; kotero, iwo adzabwenzeretsedwanso ku dziko la cholowa chawo.

12 Koma, taonani, adzakhala ndi nkhondo, ndi mphekesera za nkhondo; ndipo tsiku likadzafika kuti Mwana Obadwa yekha wa Atate, inde, ngakhale Atate Akumwamba ndi dziko lapansi, adzadzionetsera yekha kwa iwo mu thupi, taonani, iwo adzamukana, chifukwa cha mphulupulu zawo, ndi kuuma kwa mitima yawo, ndi kuuma kwa makosi awo.

13 Taonani, adzampachika iye; ndipo akadzaikidwa m’manda kwa nthawi ya masiku atatu iye adzauka kwa akufa, ndi machilitso m’mapiko ake; ndipo onse amene adzakhulupilira mu dzina lake adzapulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu. Kotero, moyo wanga umakondwera mu kunenera zokhudzana ndi iye, pakuti ndaliona tsiku lake, ndipo mtima wanga ukweza dzina lake loyera.

14 Ndipo taonani, zidzachitika kuti Mesiya akadzauka kwa akufa, ndi kudzionetsera yekha kwa anthu ake, kwa ochuluka amene adzakhulupilira pa dzina lake, taonani, Yerusalemu adzawonongedwanso; Pakuti tsoka kwa iwo amene amamenyana ndi Mulungu ndi anthu a mpingo wake.

15 Kotero Ayuda adzamwazikana pakati pa maiko onse; inde, ndiponso Babulo adzawonongedwa; kotero, Ayuda adzamwazikanitsidwa ndi maiko ena.

16 Ndipo atatha kumwazikana, ndipo Ambuye Mulungu wawakwapula iwo ndi maiko ena kwa nthawi ya mibadwo yambiri, inde, ngakhale kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo kufikira iwo adzakopeka kuti akhulupilire mwa Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi chitetezero, chimene chiri chopanda malire kwa anthu wonse—ndipo pamene tsikulo likadzafika limene iwo adzakhulupilira mwa Khristu, ndi kulambira Atate mu dzina lake, ndi mitima yoyera komanso manja oyera, ndi kusayang’aniranso kwa Mesiya wina, pamenepo, pa nthawi imeneyo, tsiku lidzafika limene kudzakhala kofunikira kukhala koyenera kuti akhulupilire mu zinthu izi.

17 Ndipo Ambuye adzaika dzanja lake kachiwiri kuti abwenzeretse anthu ake kuchokera ku mkhalidwe wawo wotaika ndi wakugwa. Kotero, iye adzapitiliza kuchita ntchito yabwino ndi yodabwitsa pakati pa ana a anthu.

18 Kotero, iye adzabweretsa mawu ake kwa iwo, mawu amene adzaweruza iwo patsiku lomaliza, pakuti adzaperekedwa kwa iwo ndicholinga chowatsimikizira iwo za Mesiya woona, amene adakanidwa ndi iwo, ndi kuwatsikimizira iwo kuti sakufunikiranso kuyembekezeranso patsogolo kwa Mesiya kuti abwere, pakuti sipadzabweranso wina, kupatula kuti adzakhala Mesiya wabodza amene adzanamize anthu; pakuti alipo Mesiya m’modzi amene adakambidwa ndi aneneri, ndipo Mesiya ameneyo ndi iye amene adzakanidwe ndi Ayuda.

19 Pakuti molingana ndi mawu a aneneri, Mesiya adzabwera m’dzaka mazana asanu ndi limodzi kuchokera pa nthawi yomwe atate anga adachoka ku Yerusalemu; ndipo molingana ndi mawu a aneneri, ndiponso mawu amngelo wa Mulungu, dzina lake adzakhala Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.

20 Ndipo tsopano, abale anga, Ndayankhula momveka kuti musalakwitse. Ndipo monga Ambuye Mulungu ali wamoyo amene adatulutsa Israeli ku dziko la Igupto, ndi kupatsa mphamvu kwa Mose kuti achilitse maiko atalumidwa ndi njoka ya ululu yakupha, ngati adzaponye maso awo pa njoka imene iye adaikweza patsogolo pawo, ndiponso adapereka kwa iye mphamvu yoti akanthe thanthwe ndipo madzi ayenera kutuluka; inde, taonani ndikunena ndi inu, kuti ngati zinthu izi ndi zoona, ndipo monga Ambuye Mulungu ali wamoyo, palibe dzina lina lopatsidwa pansi pathambo kupatula liri dzina la Yesu Khristu, limene ine ndakamba, limene munthu angapulumutsidwire.

21 Kotero, pa chifukwa ichi Ambuye Mulungu walonjeza kwa ine kuti zinthu izi zimene ndikulemba zidzasungidwa ndi kusamalidwa, ndipo zidzaperekedwa kwa mbewu yanga, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo, kuti lonjezo likwaniritsidwe kwa Yosefe, kuti mbewu yake siidzawonongedwa utali umene dziko likuyenera kukhala.

22 Kotero, zinthu izi zidzapita ku m’badwo ndi m’badwo utali monga dziko lapansi lidzaima; ndipo zidzapita molingana ndi chifuniro ndi kukonda kwa Mulungu; ndipo maiko amene adzakhala nazo adzaweruzidwa ndi izo molingana ndi mawu amene alembedwa.

23 Pakuti timagwira ntchito mwakhama kulemba, kuti tiwakakamize ana athu, ndiponso abale athu, kuti akhulupilire mwa Khristu, ndi kuyanjanitsidwa ndi Mulungu; pakuti tikudziwa kuti ndi mwa chisomo kuti ife tapulumutsidwa, pambuyo pa zonse zomwe tingathe kuchita.

24 Koma, ngakhale timakhulupilira mwa Khristu, ife timasunga lamulo la Mose, ndipo tikuyang’ana mokhazikika kwa Khristu, kufikira lamulo la Mose lidzakwaniritsidwe.

25 Pakuti, chifukwa cha mapeto amenewa, lamulo lidaperekedwa; kotero lamulo lakhala lakufa kwa ife, ndipo tapangidwa a moyo mwa Khristu chifukwa cha chikhulupiliro chathu; komabe timasunga lamulo chifukwa cha malamulo.

26 Ndipo timakamba za Khristu, timakondwera mwa Khristu, timalalikira za Khristu, timanenera za Khristu, ndipo timalemba molingana ndi mauneneri athu, kuti ana athu adziwe gwero limene angayang’anire pa chikhululukiro cha machimo awo.

27 Kotero, timayankhula zokhudzana ndi chilamulo kuti ana athu adziwe kufa kwa chilamulo, ndipo iwo, pakudziwa za kufa kwa chilamulo, akhonza kuyan’ganira kwa moyo umene uli mwa Khristu, ndi kudziwa mathero achimene chilamulo chidaperekedwera. Ndipo chilamulo chikadzakwaniritsidwa mwa Khristu, iwo sakuyenera kuumitsa mitima yawo motsutsana naye pamene chilamulo chikuyenera kuchotsedwa.

28 Ndipo tsopano taonani, anthu anga, ndinu anthu osamva; kotero, ndayankhula momveka kwa inu, kuti musamvetse molakwika. Ndipo mawu amene ine ndayankhula adzaima ngati umboni wakutsutsa inu; pakuti ndiokwanira kuphunzitsa munthu wina aliyense njira yoyenera; pakuti njira yoyenera ndi kukhulupilira Khristu ndi kusamukana iye; pakuti pakumukana iye, inu mukukananso aneneri ndi chilamulo.

29 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu kuti njira yolondora ndi kukhulupilira mwa Khristu, ndi kusamukana iye; ndipo Khristu ndi Oyera wa Israeli; kotero inu mukuyenera kugwada pansi pamaso pake, ndi kumulambira iye ndi mphamvu zanu zonse, maganizo, ndi nyonga, ndi moyo wanu onse; ndipo ngati muchita izi, inu simungadzatulutsidwe kunja.

30 Ndipo, motero monga kudzakhala koyenera, mukuyenera kusunga machitidwe ndi miyambo ya Mulungu kufikira chilamulo chidzakwaniritsidwa chimene chidapelekedwa kwa Mose.

Print