Malembo Oyera
2 Nefi 16


Mutu 16

Yesaya aona Ambuye—Machimo a Yesaya akhululukidwa—Iye aitanidwa kuti akhale mneneri—Iye anenera za kukana kwa Ayuda kwa ziphunzitso za Khristu—Wotsalira adzabwelera—Fananitsani Yesaya 6. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 M’chaka chimene mfumu Uziya adafa, ndidaonanso Ambuye atakhala pa mpando wachifumu, wautali ndi wotukulidwa, ndipo zovala zawo zidadzadza m’kachisi.

2 Pamwamba pake padaima aserafi; aliyense adali ndi makupe asanu ndi limodzi; awiri adaphimba nkhope yawo, ndipo awiri adaphimba mapazi awo ndipo awiri amaulukira.

3 Ndipo wina adafuula kwa mzake, ndipo adati: Oyera, oyera, oyera, ndi Ambuye wa Makamu; dziko lonse lapansi ladzadza ndi ulemelero wake.

4 Ndipo nsanamira za zitseko zidagwedezeka ndi mawu a wofuulayo, ndipo nyumba idadzadzidwa ndi utsi.

5 Pamenepo ndidati ine: Tsoka kwa ine! pakuti ndathedwa; chifukwa ndine munthu wamilomo yonyansa; ndipo ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; pakuti maso anga aona Mfumu, Ambuye wa Makamu.

6 Pamenepo adauluka m’modzi wa a serafi kwa ine, ali nalo khala lamoto mdzanja lake, limene adalitenga pa m’paniro pa guwa la nsembe.

7 Ndipo iye adakhudza nalo pakamwa panga, nati: Taona, ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa ndipo tchimo lako layeretsedwa.

8 Ndiponso ndidamva mawu a Ambuye, kuti: Kodi ndidzatuma ndani, ndipo ndani adzatipitira ife? Pamenepo ndidati: Ine ndilipano, nditumeni ine.

9 Ndipo iye adati: Pita ndipo uwauze anthu awa—Imvani inu ndithu, koma iwo sadamvetsetse; ndipo onani inu ndithu, koma iwo sadaonetsetse.

10 Nenepetsa mtima wa anthu awa, ndipo lemeletsa makutu awo, ndipo tseka maso awo—kuti angaone ndi maso awo, ndi kumva ndi makutu awo, ndi kumvetsera ndi mitima yawo, ndi kutembenuka ndi kuchilitsidwa.

11 Pomwepo ine ndidati: Ambuye, mpaka liti? Ndipo iye adati: Kufikira mizinda itapasuka yopanda okhalamo, ndipo nyumba zopanda munthu, ndi dziko litakhala bwinja ndithu.

12 Ndipo Ambuye wachotsa anthu kutali, pakuti padzakhala masiyanidwe aakulu pakati pa dziko.

13 Koma padzakhala limodzi mwa ma gawo khumi, ndipo iwo adzabwelera, ndipo adzadyedwa, ngati mtengo wa mkungudza, ndi ngati mtengo wa thundu umene tsinde lake limakhalabe atachotsa masamba ake, chotero, mbewu yopatulika idzakhalabe tsinde lake.