Malembo Oyera
2 Nefi 5


Mutu 5

Anefi adzisiyanitsa okha kwa aLamani, asunga malamulo a Mose, ndi kumanga kachisi—Chifukwa cha kusakhulupilira kwawo, Alamani achotsedwa pamaso pa Ambuye, atembeleredwa, ndipo akhala chikwapu kwa aNefi. Mdzaka dza pafupifupi 588–559 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, zidachitika kuti ine, Nefi, ndidalira kwambiri kwa Ambuye Mulungu wanga, chifukwa cha mkwiyo wa abale anga.

2 Koma taonani, mkwiyo wawo udakulabe motsutsana ndi ine, kufikira kuti adafunitsitsa kuchotsa moyo wanga.

3 Inde, adang’ung’udza motsutsana nane, nati: Mng’ono wathu akuganiza zotilamulira ife; ndipo ife tayesedwa kwambiri chifukwa cha iye; kotero, tsopano tiyeni timuphe, kuti tisazunzikenso chifukwa cha mau ake. Pakuti taonani, sitidzalora kuti iye akhale wolamulira wathu; pakuti kuli kwa ife, amene tiri abale akulu, kulamulira anthu awa.

4 Tsopano sindilemba pa mapale awa mau onse amene iwo adang’ung’udza motsutsana nane. Koma ndichokwanira kwa ine kunena kuti iwo adafuna kuchotsa moyo wanga.

5 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adandichenjeza ine, kuti Ine, Nefi, ndichoke kwa iwo ndikuthawira m’chipululu, ndi onse amene akadapita nane.

6 Pachifukwa ichi, zidachitika kuti, ine, Nefi, ndidatenga banja langa, ndiponso Zoramu ndi banja lake, ndi Samu, mkulu wanga ndi banja lake, ndi Yakobo ndi Yosefe, abale angaaang’ono ndiponso alongo anga, ndi onse amene adafuna kupita nane. Ndipo onse amene adapita nane adali omwe adakhulupilira mu machenjezo ndi mabvumbulutso a Mulungu; kotero, adamvetsera kwa mau anga.

7 Ndipo tidatenga mahema athu ndi zinthu zina zilizonse zomwe tikadatha, ndipo tidayenda m’chipululu kwa nthawi ya masiku ambiri. Ndipo titayenda kwa nthawi ya masiku ambiri, tidakhoma mahema athu.

8 Ndipo anthu anga adafuna kuti titchule dzina la malowo Nefi; kotero, tidawatcha kuti Nefi.

9 Ndipo onse amene adali ndi ine adadzitengera pawokha kudzitcha anthu a Nefi.

10 Ndipo tidatsata kusunga ziweruzo, ndi malemba, ndi malamulo a Ambuye mu zinthu zonse, monga mwa chilamulo cha Mose.

11 Ndipo Ambuye adali nafe; ndipo tidachita bwino kwambiri; pakuti tidafesa mbewu, ndipo tidakololanso zochuluka. Ndipo tidayamba kuweta ziweto ndi nyama zamitundumitundu.

12 Ndipo ine, Nefi, ndidabweretsanso zolemba zomwe zidazokotedwa pa mapale a mkuwa; ndiponso kampira, kapena kampasi, amene adakonzeredwa kwa bambo anga ndi dzanja la Ambuye molingana ndi zomwe zalembedwa.

13 Ndipo zidachitika kuti tidayamba kuchita bwino koposa, ndi kuchulukana mdziko.

14 Ndipo ine, Nefi, ndidatenga lupanga la Labani, ndipo mofanana nalo ndidapanga malupanga ambiri, kuti mwa njira ina iliyonse anthu amene tsopano akutchedwa aLamani angabwere kwa ife ndi kudzationonga; pakuti ndidadziwa za udani wawo pa ine ndi ana anga ndi iwo omwe amatchedwa anthu anga.

15 Ndipo ndidawaphunzitsa anthu anga kumanga zomanga, ndi kugwira ntchito mu mitundu yonse yamatabwa, ndi zitsulo, ndi kopa, ndi mkuwa, ndi golide, ndi siliva, ndi miyala yamtengo wapatali, zimene zidali zochuluka kwambiri.

16 Ndipo ine, Nefi, ndidamanga kachisi; ndipo ndidaimanga mofanana ndi kachisi ya Solomoni koma siidamangidwe ndi zinthu zamtengo wapatali; popeza kuti sizimapezeka mdziko, kotero, siikadamangidwa ngati mmene idalili kachisi ya Solomoni. Koma mamangidwe ake adali ofanana ngati kachisi ya Solomoni; ndi mamangidwe ake adali abwino kwambiri.

17 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidachititsa anthu anga kukhala akhama ndi kugwira ntchito ndi manja awo.

18 Ndipo zidachitika kuti iwo adafuna ine ndikhale mfumu yawo. Koma ine, Nefi ndidafunitsitsa kuti pasakhale mfumu; komabe, ndidawachitira iwo monga izo zidali mu mphamvu zanga.

19 Ndipo taonani, mau a Ambuye adakwaniritsidwa kwa abale anga, amene adanena zokhudza iwo, kuti ndidzakhale owalamulira ndi mphunzitsi wawo. Kotero, ndidakhala mtsogoleri wawo ndi mphunzitsi wawo, malingana ndi malamulo a Ambuye, kufikira nthawi yomwe iwo adafuna kuchotsa moyo wanga.

20 Kotero, mau a Ambuye adakwaniritsidwa omwe iwo adanena kwa ine, nati; Pamene iwo sadzamvera mau ako adzachotsedwa pamaso pa Ambuye. Ndipo taonani, iwo adachotsedwa pamaso pake.

21 Ndipo adachititsa thembelero kufikira kwa iwo, inde, angakhale thembelero lowawa chifukwa cha mphulupulu zawo. Pakuti taonani, iwo adalimbitsa mitima yawo motsutsana naye, kufikira iwo adakhala ngati mwala; kotero, pamene iwo adali oyera ndi okongola kwambiri, ndi okondweretsa, kuti asakope anthu anga, Ambuye Mulungu adachititsa khungu lakuda kubwera pa iwo.

22 Ndipo akutero Ambuye Mulungu: Ndidzapangitsa kuti akhale osaoneka bwino kwa anthu ako kufikira iwo atalapa machimo awo.

23 Ndipo idzakhala yotembeleredwa mbewu ya iye amene asakanizana ndi mbewu zawo; pakuti nawo adzatembeleredwa ndi thembelero lomwelo. Ndipo Ambuye adayankhula izo, ndipo zidachitika.

24 Ndipo chifukwa cha thembelero lomwe lidafika pa iwo adakhala anthu a ulesi, okonda mphulupulu ndi akapsali, ndipo adayamba kusaka zinyama m’chipululu.

25 Ndipo Ambuye Mulungu adati kwa ine: adzakhala chikwapu kwa mbewu yako, chowachangamutsa iwo powakumbutsa za ine, ndipo ngati sadzakumbukira ine, ndi kumvera mau anga, iwo adzakwapula iwo mpaka ku chiwonongeko.

26 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidadzodza Yakobo ndi Yosefe, kuti akhale ansembe ndi aphunzitsi pa dziko la anthu anga.

27 Ndipo zidachitika kuti tidakhala ndi moyo wa chimwemwe.

28 Ndipo zaka makumi atatu zidali zitapita kuchokera pa nthawi imene tidachoka ku Yerusalemu.

29 Ndipo ine, Nefi, ndidasunga zolemba pa mapale anga, omwe ndidapanga, za anthu anga kufikira tsopano lino.

30 Ndipo zidachitika kuti Ambuye Mulungu adati kwa ine, Panga mapale ena; ndipo udzizokota zambiri zomwe zili zabwino pamaso panga, kuti anthu ako apindule nazo.

31 Kotero, ine, Nefi, kuti ndimvere malamulo a Ambuye, ndidapita ndi kupanga mapalewa pamene ndidazokotapo zinthu izi.

32 Ndipo ndidalemba zimene zili zokondweretsa Mulungu. Ndipo ngati anthu anga akondweretsedwa ndi zinthu za Mulungu, iwo adzakondwera ndi zomwe ndazokota pa mapale amenewa.

33 Ndipo ngati anthu anga akufuna kudziwa gawo la mbiri ya anthu anga, akuyenera kufufuza mapale anga ena.

34 Ndipo ndichokwanira kwa ine kunena kuti zaka makumi anayi zidali zitapita, ndipo tidali kale ndi nkhondo ndi mikangano ndi abale athu.