Malembo Oyera
2 Nefi 14


Mutu 14

Ziyoni ndi ana ake aakazi adzawomboledwa ndi kuyeretsedwa m’tsiku la dzaka chikwi—Fananitsani Yesaya 4. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo mutsiku limenelo, azimayi asanu ndi awiri, adzagwira mwamuna m’modzi, nati: Tidzadya zakudya zathu, ndi kuvala zovala zathu; koma tiloleni tidzitchedwa dzina lanu lokha ndikuchotsa chotonzo chathu.

2 Mutsiku limenelo nthambi ya ambuye idzakhala yokongola ndi ya ulemelero; chipatso cha mnthaka chabwino ndi chokometsetsa kwa iwo amene adzapulumuka ku Israeli.

3 Ndipo zidzachitika kuti, iwo amene adzasiyidwa mu Ziyoni ndi kukhalabe mu Yerusalemu adzatchedwa oyera, aliyense amene walembedwa mwa amoyo mu Yerusalemu—

4 Pamene Ambuye adzakhala atatsuka zonyansa za ana aakazi a Ziyoni, ndipo adzatsuka mwazi wa Yerusalemu pakati pawo ndi mzimu wa chiweruzo ndi mzimu wakutentha.

5 Ndipo Ambuye adzalenga pamalo onse okhala pa Phiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi mu usana ndi kuwala kwa malawi a moto mu usiku; pakuti pa ulemelero onse a Ziyoni padzakhala choteteza.

6 Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi mu nthawi ya usana wa kutentha, ndi pamalo pothawira, ndi pobisalira ku mphepo ya mkuntho ndi mvula.