Malembo Oyera
2 Nefi 17


Mutu 17

Efraimu ndi Siriya amenya nkhondo ndi Yuda—Khristu adzabadwa mwa namwali—Fananitsani Yesaya 7. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika m’masiku a Ahazi mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Siriya, ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli, adapita ku Yerusalemu kukamenyana naye, koma sadathe kupambana.

2 Ndipo adauzidwa a nyumba ya Davide, kuti: Siriya wagwirizana ndi Efraimu. Ndipo mtima wake udasuntha, ndi mtima wa anthu ake, momwe mitengo ya mu nkhalango imagwedezekela ndi mphepo.

3 Pamenepo Ambuye adati kwa Yesaya: Pita tsopano ukakumane ndi Ahazi, iwe ndi Seariyasubu mwana wako, pamamaliziro a ngalande ya thamanda la pa mtunda mu khwalala la wochapa zovala nsalu.

4 Ndipo ukati kwa iye: Chenjera, ndipo khala chete; usaope, kapena mtima wako kulefuka chifukwa cha michira iwiri ya muuni ofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Siriya, ndi wa mwana wa Remaliya.

5 Chifukwa cha Siriya, Efraimu, ndi mwana wa Remaliya, adapangira iwe upo oipa, nati:

6 Tiyeni tipite tikamenyane ndi Yuda ndipo tikamuvutitse, ndipo tiyeni tizigumulire mpata m’menemo, ndi kuika mfumu pakati pake, inde, mwana wamamuna wa Tabeeli.

7 Atero Ambuye Mulungu: Izo sizidzakhazikika, ndipo sizidzachitika.

8 Pakuti mutu wa Siriya ndiwo Damasiko, ndipo mutu wa Damasiko, Rezini; ndipo m’dzaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzamphwanyidwa kuti sadzakhalanso mtundu wa anthu.

9 Ndipo mutu wa Efraimu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wamamuna wa Remaliya. Ngati simudzakhulupilira ndithu zimudzakhazikika.

10 Komanso, Ambuye adayankhulanso kwa Ahazi, nati:

11 Funsa chizindikiro kwa Ambuye Mulungu wako; funsa mozama kapena m’mwambamwamba.

12 Koma Ahazi adati: Sindipempha ngakhale sindidzamuyesa Ambuye.

13 Ndipo iye adati: Mverani tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi chinthu chaching’ono kwa inu kutopetsa anthu, koma mudzatopetsanso Mulungu wanga?

14 N’chifukwa chake, Ambuye mwini adzakupatsani inu chizindikiro—Taonani, namwali adzakhala ndi pakati, ndipo adzabala mwana wamamuna, ndipo adzamutcha dzina lake Imanueli.

15 Mafuta ndi uchi iye adzadya, kuti adziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino.

16 Pakuti mwanayo asadadziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene umadana nalo lidzasiyidwa ndi mafumu ake awiriwo.

17 Ambuye adzabweretsa pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate ako, masiku amene sadabwerepo kuyambira tsiku limene Efraimu adachoka kwa Yuda, mfumu ya Asiriya.

18 Ndipo zidzachitika kuti mu tsiku limenelo Ambuye adzaimbira muluzi ntchentche za ku mbali yothera ya Igupto, ndi njuchi za m’dziko la Asiriya.

19 Ndipo zidzabwera, ndikupumula zonse m’zigwa za mabwinja, ndi m’mapanga a mathanthwe, ndi pa minga zonse ndi pathengo ponse.

20 Mutsiku lomwelo Ambuye adzameta mutu ndi tsitsi lakumapazi ndi lumo lobwereka ndi iwo ali ku tsidya lija la mtsinje, ndi mfumu ya Asiriya, ndipo lidzanyeketsanso ndevu.

21 Ndipo zidzachitika mu tsikulo, munthu adzaweta ng’ombe yaing’ono ndi nkhosa ziwiri;

22 Ndipo zidzachitika, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka omwe zidzapereke iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi aliyense adzadya amene adzatsale m’dzikomo.

23 Ndipo zidzachitika mu tsikulo, paliponse padzakhala, pamene padali mipesa chikwi chimodzi cha mtengo wake wa chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.

24 Ndi mivi ndi mauta, anthu adzafikako kumeneko, chifukwa dziko lonse lidzakhala ndi lunguzi ndi minga.

25 Ndipo mapiri onse amene adzakumbidwa ndi makasu, kumeneko sadzafikako kuopa lunguzi ndi minga; koma padzakhala potumizira ng’ombe, ndi popondaponda ziweto.

Print