Malembo Oyera
2 Nefi 22


Mutu 22

M’masiku a dzaka chikwi anthu wonse adzatamanda Ambuye—Iye adzakhala pakati pawo—Fananitsani Yesaya 12. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo patsiku limenelo udzati: Inu Ambuye, ndidzakuyamikani inu; ngakhale mudandikwiyira ine, mkwiyo wanu wabwelera, ndipo mudanditonthoza.

2 Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupilira, ndipo sindidzaopa; pakuti Ambuye Yehova ndiye mphamvu zanga ndi nyimbo yanga, iyenso wakhala chipulumutso changa.

3 Kotero, ndichisangalalo mudzatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

4 Ndipo patsilu limenelo mudzati: Yamikani Ambuye, itanirani pa dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa anthu, tchulani kuti dzina lake lakwezeka.

5 Imbirani Ambuye; pakuti wachita zinthu zazikulu, izi zadziwika pa dziko lonse lapansi.

6 Lira mokweza ndipo fuula, iwe okhala mu Ziyoni; pakuti Woyera wa Israeli ali wamkulu pakati pako.

Print