Malembo Oyera
2 Nefi 11


Mutu 11

Yakobo aona Muwomboli wake—Lamulo la Mose limaimira Khristu ndipo zimatsimikizira kuti Iye adzabwera. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, Yakobo adayankhula zinthu zambiri kwa anthu anga panthawiyo; komabe zinthu zokhazi ndi zimene ndapangitsa kuti zilembedwe, pakuti zinthu zomwe ndazilemba zikundikwanira.

2 Ndipo tsopano ine, Nefi, ndikulemba mawu ambiri a Yesaya, pakuti moyo wanga ukondwera mu mawu ake. Pakuti ndidzafanizira mawu ake ndi anthu anga, ndipo ndidzawatumiza kwa ana anga onse, pakuti zoonadi iye adaona Muwomboli wanga, monga momwe ine ndamuona iye.

3 Ndipo m’bale wanga, Yakobo, nayenso wamuona iye monga ine ndamuonera; kotero, ndidzatumiza mawu awo kwa ana anga kuti atsimikizire kwa iwo kuti mawu anga ndioona. Kotero, ndi mawu a atatu, watero Mulungu, Ndidzakhazikitsa mawu anga. Komabe, Mulungu amatumiza mboni zochuluka, ndipo amatsimikizira mawu ake onse.

4 Taonani, moyo wanga ukondwera mu kutsimikizira kwa anthu anga za choonandi cha kubwera kwa Khristu; pakuti, pachifukwa ichi, lamulo la Mose lapatsidwa; ndi zinthu zonse zomwe zidaperekedwa za Mulungu kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi, kwa munthu, ziri zoimira iye.

5 Ndipo moyo wanga ukondwera mu mapangano a Ambuye amene adapanga ndi makolo athu; inde, moyo wanga ukondwera mu chisomo chake, ndi mu chilungamo chake, ndi mphamvu, ndi chifundo mu dongosolo lalikulu ndi la muyaya la chiwombolo kuimfa.

6 Ndipo moyo wanga ukondwera mu kutsimikizira kwa anthu anga kuti pokhapokha Khristu adzabwere anthu onse adzawonongeka.

7 Pakuti ngati palibe Khristu palibe Mulungu; ndipo ngati palibe Mulungu, ife palibepo, pakuti sipakadakhala chilengedwe. Koma Mulungu alipo, ndipo iye ndi Khristu, ndipo adzabwera mu chidzalo cha nthawi yake.

8 Ndipo tsopano ndikulemba mawu a Yesaya, kuti aliyense mwa anthu anga akadzaona mawu awa adzakweze mitima yawo ndi kukondwera chifukwa cha anthu onse. Tsopano awa ndiwo mawuwo, ndipo mukhonza kuwafananitsa ndi inu ndi anthu onse.