Malembo Oyera
2 Nefi 19


Mutu 19

Yesaya ayankhula mwaumesiya—Anthu mum’dima adzaona kuwala kwakukulu—Kwa ife mwana watibadwira—Adzakhala Kalonga wa mtendere ndipo adzalamulira pa mpando wa chifumu wa Davide—Fananitsani Yesaya 9. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Komabe, mdimawo sudzakhala woterowo m’kusautsidwa kwake, pamene poyamba adasautsa pang’ono dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, ndipo pamapeto pake adasautsa mowawa kwambiri njira ya Nyanja Yofira kutsidya lija la Yordani mu Galileya wa maiko.

2 Anthu amene adayenda mu mdima aona kuwala kwakukulu; iwo amene akhala mu dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwawala kwa iwo.

3 Inu mwachulukitsa maiko, ndi kuwonjezera chisangalalo—iwo asangalala pamaso panu monga mwachisangalalo mu nthawi yokolola, ndipo monga anthu akondwera pogawana zofunkha.

4 Pakuti inu mwathyola goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake ndi ndodo ya omusautsa ake.

5 Pakuti nkhondo iliyonse ya wankhondo imakhala ndi phokoso losokoneza ndi zovala zovimvinyika m’mwazi; koma izi zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.

6 Pakuti kwa ife watibadwira mwana, kwa ife mwana mamamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake; ndipo adzamutcha dzina lake, Wodabwitsa, Mphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere.

7 Za kuonjezera ulamuliro ndi mtendere sizidzatha, pa mpando wa chifumu wa Davide, ndipo paufumu wake kuulamulira, ndi kuukhazikitsa ndi chiweruzo ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi ku nthawi zonse. Changu cha Ambuye wa Makamu chidzachita zimenezi.

8 Ambuye adatumiza mawu ake kwa Yakobo ndipo adafikira pa Israeli.

9 Ndipo anthu wonse adzadziwa, ngakhale Efraimu ndi anthu okhala mu Samariya, amene amanena monyada ndi mokula mtima:

10 Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yadulidwa, koma ife tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.

11 N’chifukwa chake Ambuye adzakhazikitsa adani a Rezini kutsutsana naye, ndi kuwaphatikiza adani ake pamodzi;

12 Asiriya patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israeli ndi kukamwa koyasama. Pazonsezi mkwiyo wake sudachoke, koma dzanja lake liri chitambasulire.

13 Pakuti anthu sadatembenukire kwa iye amene adawakantha, kapena kufuna Ambuye wa Makamu.

14 N’chifukwa chake Ambuye adzadula mwa Israeli mutu ndi mchira wake, nthambi ndi mlulu tsiku limodzi.

15 Wakale, ndiye mutu; ndi mneneri amene aphunzitsa zonama, ndiye mchira.

16 Pakuti atsogoleri a anthu awa ndiwo amawasokeretsa; ndipo iwo amene akutsogoleredwa ndi iwo awonongeka.

17 N’chifukwa chake Ambuye sadzasangalala ndi anyamata awo, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye awo ndi akazi amasiye; pakuti aliyense wa iwo ali wonyenga ndi ochita zoipa, ndipo mkamwa mwake mumayankhula zopusa. Pazonsezi mkwiyo wake sudachoke, koma dzanja lake liri chitambasulire.

18 Pakuti kuipa kumayaka ngati moto; kudzamaliza lunguzi ndi minga, ndi kuyatsa thengo la m’nkhalango, ndipo zofuka zake zidzakwera ngati kukwera kwa utsi.

19 M’kukwiya kwa Ambuye wa Makamu dziko ladetsedwa, ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni za moto; palibe amene adzachitire chisoni m’bale wake.

20 Ndipo adzakwatula kudzanja la kumanja nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lakumanzere ndipo sadzakhuta; iwo adzadya munthu aliyense nyama ya dzanja lake la iye yekha—

21 Manase, Efraimu; ndi Efraimu, Manase; iwo wonse pamodzi adzamenyana ndi Yuda. Pazonsezi mkwiyo wake sudachoke, koma dzanja lake liri chitambasulire.