Malembo Oyera
2 Nefi 28


Mutu 28

Mipingo yonama yambiri idzamangidwa m’masiku omaliza—Idzaphunzitsa ziphunzitso zabodza, zopanda pake, ndi zopusa—Mpatuko udzachuluka chifukwa cha aphunzitsi abodza—Mdyerekezi adzakwiya m’mitima ya anthu—Adzaphunzitsa mitundu yonse ya ziphunzitso zabodza. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, taonani, abale anga, ndayankhula kwa inu, molingana ndi momwe Mzimu wandikakamizira ine, kotero, ndikudziwa kuti izi ndithu zikuyera kuchitika.

2 Ndipo zithu zimene zidzalembedwe kuchokera m’bukuli zidzakhala za mtengo wapatali kwa ana a anthu, ndipo makamaka kwa mbewu yathu, imene ndi otsalira a nyumba ya Israeli.

3 Pakuti zidzachitika mu tsiku limenero kuti mipingo imene idzamangidwe, ndipo osati kwa Ambuye, pamene wina adzati kwa mzake: Taona, ine ndi wa Ambuye; ndipo enawo adzati: Ine, ndine wa Ambuye; ndipo motere aliyense adzatero amene wamanga mpingo, koma osati kwa Ambuye—

4 Ndipo adzakangana wina ndi mzake; ndipo ansembe awo adzakangana wina ndi mzake, ndipo iwo adzaphunzitsa mwa kuphunzira kwawo, ndipo adzakana Mzimu Woyera, umene umapereka mawu.

5 Ndipo iwo amakana mphamvu ya Mulungu, Oyera wa Israeli; ndipo adzanena kwa anthu: Mvetserani ife, ndipo mverani langizo lathu; pakuti taonani kulibe Mulungu lero, chifukwa Ambuye ndi Muwomboli wachita ntchito yake, ndipo adapereka mphamvu zake kwa anthu.

6 Taonani, mvetserani inu kwa langizo langa, ngati adzanene kuti pali chozizwitsa chopangidwa ndi dzanja la Ambuye, musakhulupilire, chifukwa pakuti lero iye sali Mulungu wa zozizwitsa; iye wachita ntchito yake.

7 Inde, ndipo adzakhalapo ambiri amene adzati: Idyani, imwani, ndipo sangalalani, chifukwa mawa tidzafa; ndipo zidzakhala bwino ndi ife.

8 Ndipo padzakhalanso ambiri amene adzati: Idyani, imwani ndi kusangalala; komabe opani Mulungu—iye adzatilungamitsa pakuchita tchimo laling’ono; inde, namani pang’ono, pezelani mwayi pa wina chifukwa cha mawu ake, kumbani dzenje kwa mnansi wanu; palibe choipa m’zimenezi; ndipo chitani zonsezi, pakuti mawa tidzafa; ndipo ngati kuli kuti ndife wolakwa, Mulungu adzatimenya ndi dzikwapu dzochepa, ndipo pamapeto pake tidzapulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu.

9 Inde, ndipo padzakhala ambiri amene adzaphunzitse monga motere, ziphunzitso zabodza ndi zopanda pake ndi zopusa, ndipo adzakhala odzikuza m’mitima mwawo, ndipo adzafunafuna mozama kubisira Ambuye uphungu wawo; ndipo ntchito zawo zidzakhala za mu mdima.

10 Ndipo mwazi wa oyera mtima udzafuula kuchokera pansi panthaka motsutsana nawo.

11 Inde, wonse achokamo mu njira; iwo aipitsidwa.

12 Chifukwa cha kunyada, ndi chifukwa cha aphunzitsi abodza, ndi chiphunzitso chabodza, mipingo yawo yaipitsidwa, ndipo mipingo yawo ndiyodzikweza; chifukwa cha kunyada iwo ali odzikuza.

13 Amabera osauka chifukwa cha malo awo opatulika abwino; amabera osauka chifukwa cha zovala zawo zabwino; ndipo amazunza ofatsa ndi osauka mumtima, chifukwa m’kunyada kwawo ali odzikuza.

14 Amavala makosi ouma ndi mitu yokwezedwa; inde ndi chifukwa cha kunyada, ndi kuipa, ndi zonyansa ndi zadama, wonse asochera kupatula ochepa, amene ali otsatira odzichepetsa a Khristu; komabe, akutsogoleredwa, moti nthawi zambiri amalakwitsa chifukwa akuphunzitsidwa ndi malangizo a anthu.

15 Iwo anzeru, ndi ophunzira, ndi olemera, amene ali odzikuza m’kunyada kwa mitima yawo, ndi wonse amene amalalikira ziphunzitso zabodza, ndi wonse amene amachita zadama, ndi kupotoza njira yolondola ya Ambuye, tsoka, tsoka, tsoka kwa iwo, atero Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse, chifukwa adzaponyedwa pansi ku gahena!

16 Tsoka kwa iwo amene atembenuzira wolungama m’chinthu chachabe ndi kunyoza chimene chiri chabwino, ndi kunena kuti chilibe phindu! Pakuti tsiku lirinkudza limene Ambuye Mulungu adzayendera mofulumira anthu wokhala pa dziko lapansi; ndipo mutsiku limene iwo adzakhwima m’kusaweruzika, iwo adzawonongedwa.

17 Koma taonani, ngati anthu okhala pa dziko lapansi adzalapa ku zoipa zawo ndi zonyansa sadzawonongedwa, atero Ambuye wa Makamu.

18 Koma taonani, mpingo waukulu ndi wonyansa uja, wachigololo wa dziko lapansi, ukuyenera kugwa ku dziko lapansi ndipo kwakukulu kuyenera kukhala kugwa kwake.

19 Pakuti ufumu wa mdyerekezi ukuyenera kudzagwedezeka, ndipo wonse amene ali a m’menemo akuyenera kutakasika m’kulapa, apo ayi mdyerekezi adzawagwira iwo ndi maunyolo ake wosatha, ndi kutakasika ku mkwiyo ndi kuwonongeka.

20 Pakuti taonani, patsiku limenero, iye adzakwiya mmitima ya ana a anthu, ndi kuwachangamutsa iwo ku mkwiyo wotsutsana ndi zomwe ziri zabwino.

21 Ndipo ena adzawatonthoza, ndi kuwafikitsa ku chisungiko chathupi, kufikira iwo adzati: Zonse ziri bwino mu Ziyoni; inde Ziyoni akuchita bwino, zonse ziri bwino—ndipo motero mdyerekezi amanamiza moyo wawo, ndipo amawatsogolera iwo mosamalitsa kupita ku gahena.

22 Ndipo taonani, ena amawakopa, ndi kuwauza iwo kuti kulibe gahena, ndipo amati kwa iwo: Ine si mdyerekezi, pakuti palibepo woteroyo—ndipo motere iye amanong’ona m’makutu mwawo, kufikira atawagwira ndi maunyolo ake oipa, kumene kulibe chipulumutso.

23 Inde, iwo amagwidwa ndi imfa, ndi gahena; ndi imfa ndi gahena, ndi mdyerekezi ndi wonse amene agwidwa m’menemo akuyenera kudzaima pamaso pa mpando wa chifumu wa Mulungu, ndi kuweruzidwa monga mwa ntchito zawo, kuchoka pamenepo akuyenera kupita kumalo omwe adakonzeredwa kwa iwo, ngakhale nyanja ya moto ndi sulfure, amene ndi mazunzo osatha.

24 Kotero, tsoka kwa iye amene ali pamtendere mu Ziyoni!

25 Tsoka kwa iye amene afuula: Zonse ziri bwino!

26 Inde, tsoka likhale kwa iye amene amamvera malangizo a anthu, ndi kukana mphamvu ya Mulungu, ndi mphatso ya Mzimu Woyera!

27 Inde, tsoka kwa iye amene amati: Talandira, ndipo sitikusowanso!

28 Ndipo potsiriza, tsoka kwa iwo amene amanjenjemera, ndi kukwiya chifukwa cha choonadi cha Mulungu. Pakuti taonani, iye amene amangidwa pa thanthwe amachilandira ndi chimwemwe; ndipo iye amene wamangidwa pa maziko a mchenga amanjenjemera ndikugwa.

29 Tsoka kwa iye amene adzati: Talandira mawu a Mulungu, ndipo sitikufunanso mawu ena a Mulungu, pakuti tili nawo okwanira!

30 Pakuti taonani, akutero Ambuye Mulungu: Ndidzapereka kwa ana a anthu mzere pa mzere, langizo pa langizo, pano pang’ono ndi apo pang’ono; ndipo wodala ndi iwo amene amvetsera kwa malangizo anga, ndikubwereketsa khutu ku uphungu wanga, pakuti adzaphunzira nzeru; pakuti kwa iye amene alandira ndidzapereka zochuluka; ndipo kwa iwo amene adzati, tili nazo zokwana, kwa iwo chidzalandidwa ngakhale chomwe ali nacho.

31 Otembeleredwa ndi iye amene ayika chikhulupiliro chake mwa munthu, kapena kupanga thupi mkono wake, kapena adzamvera malamulo a anthu, pokhapokha malangizo adzapatsidwe ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

32 Tsoka kwa Amitundu, atero Ambuye Mulungu wa Makamu! Pakuti ngakhale ine ndidzatambasula dzanja langa kwa iwo kuchokera tsiku ndi tsiku, iwo adzandikana; komabe, ndidzawachitira chifundo, atero Ambuye Mulungu, ngati iwo adzalapa ndi kubwera kwa ine; pakuti mkono wanga watalikitsidwa tsiku lonse, atero Ambuye Mulungu wa Makamu.