Malembo Oyera
2 Nefi 20


Mutu 20

Chiwonongeko cha Siriya chikuimilira chiwonongeko cha oipa pa Kubwera Kwachiwiri—Anthu ochepa adzatsala Ambuye akadzabweranso kachiwiri—Otsalira a Yakobo adzabwelera mutsiku limenelo—Fananitsani Yesaya 10. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Tsoka kwa iwo amene akulengeza zolengeza zosalungama, ndi amene amalemba zoipa zimene adazilemba;

2 Kuwabweza aumphawi ku chiweruziro, ndi kuwalanda chilungamo kwa anthu anga aumphawi, kuti akazi amasiye akhale chofunkha chawo, ndi kuwabera ana opanda bambo!

3 Ndipo mudzachita chiyani pa tsiku lakuzonda, ndi chipasuko chochokera kutali? mudzathawira kwa ndani kuti mupeze thandizo? ndipo mudzasiya kuti ulemero wanu?

4 Popanda ine adzagwada pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Pazonsezi mkwiyo wake sudachoke, ndipo dzanja lake liri chitambasulire.

5 Inu Asiriya, ndodo ya mkwiyo wanga, ndi ndondo m’manja mwawo ndi ukali wawo.

6 Ine ndidzamutumiza iye kukamenyana ndi mtundu wachinyengo, ndipo pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamulamulira kuti atenge zolanda, ndipo kuti atenge zofunkha, ndikuzipondereza pansi monga matope a m’makwalala.

7 Koma iye sakufuna kuti zitero ngakhale mtima wake sukuganiza motero; koma mumtima mwake akufuna kuwononga ndi kudula mitundu yosawerengeka.

8 Pakuti anena: Akalonga anga kodi sali wonse mafumu?

9 Kodi Kalino si monga Karimesi? Kodi Hamati si monga Aripadi? Kodi Samariya si monga Damasiko?

10 Monga dzanja langa lidakhazikitsira maufumu a mafano, ndi mafano awo osema adaposa iwo aku Yerusalemu ndi ku Samariya.

11 Kodi ine sindidzachita, monga m’mene ndidachitira kwa Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake?

12 Kotero, zidzachitika kuti pamene Ambuye adzachita ntchito yawo yonse pa Phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, Ndidzalanga zipatso za kudzikuza mtima wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemelero wa maonekedwe ake okwezeka.

13 Pakuti anena: Mwa mphamvu ya dzanja ndi nzeru zanga ndachita zinthu izi; pakuti ine ndiri wanzeru, ndipo ndachotsa malire a anthu awa, ndipo ndalanda chuma chawo, ndipo ndagwetsa iwo wokhalamo monga munthu wolimba mtima.

14 Ndipo dzanja langa lapeza monga chisa chuma cha anthu; ndipo ngati wina asonkhanitsa mazira otsala ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi; ndipo padalibe wina adasuntha phiko, kapena kutsegula kukamwa, kapena kusunzumira.

15 Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha kwa iye amene adula nayo? Kodi macheka adzadzikweza okha kwa iye awagwedeza? Ngati ndodo ingadzigwedeze yokha pa iye amene akuinyamula, kapena ndodo ingadzinyamule yokha ngati iyo siidali nkhuni!

16 N’chifukwa chake Ambuye, Ambuye wa Makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemelero wake adzayatsa kuyaka ngati kuyaka kwa moto.

17 Ndipo kuwala kwa Israeli kudzakhala moto, ndipo Oyera wake adzakhala lawi, ndipo adzayatsa ndi kupsereza minga zake ndi lunguzi zake tsiku limodzi.

18 Ndipo adzanyeketsa ulemelero wa m’nkhalango yake, ndi wa munda wake obala zipatso, zonse moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.

19 Ndipo mitengo yotsala ya m’nkhalango yake idzakhala yowelengeka, kuti mwana ailembe.

20 Ndipo padzachitika pa tsikulo, kuti otsala a Israeli, ndi iwo amene adapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso pa owagwedeza adawakantha, koma adzatsamira pa Ambuye, Oyera wa Israeli, m’choonadi.

21 Otsala adzabwelera, inde, ngakhale otsalira a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.

22 Popeza ngakhale anthu anu Israeli achuluka ngati mchenga wakunyanja, wotsala a iwo adzabwelera; chiwonongeko chidzasefukira ndi chilungamo.

23 Pakuti Ambuye wa Makamu adzachita chiwonongeko chotsimikizirika pakati pa dziko lonselo.

24 Kotero, atero Ambuye Mulungu wa Makamu: Inu anthu anga okhala m’Ziyoni, musachite mantha ndi Asiriya; adzakukanthani inu ndi ndodo, ndipo adzanyamula ndodo yake pa inu, monga mwa machitidwe a Aigupto.

25 Pakuti katsala kamphindi kakang’ono, ndipo ukali udzaleka ndi mkwiyo wanga chiwonongeko chawo.

26 Ndipo Ambuye wa Makamu adzamuutsira nkwapulo monga mwa kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo monga ndodo yake idali pa nyanja, momwemo adzainyamula ngati m’mene adachitira Aigupto.

27 Ndipo padzachitika pa tsikulo katundu wake adzachotsedwa pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako, ndipo goli lidzawonongedwa chifukwa cha kudzodza.

28 Wafika ku Ayati, wadutsa ku Migironi; ku Mikimashi adasunga zotengera zake.

29 Iwo apita adutsa pa mpata, adagona pa Geba; Ramati achita mantha; Gibeya wa Sauli wathawa.

30 Kweza mawu ako, iwe mwana wamkazi wa Galimu; pangitsa kuti zimveke kwa Laisi, iwe Anatoti wosauka.

31 Madimena wachotsedwa; okhala m’Gebimu asonkhana kuti athawe.

32 Adzakhalabe mu Nobu tsiku lomwelo; adzagwedezera dzanja lake pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.

33 Taonani, Ambuye, Ambuye wa Makamu adzadula nthambi moopsya; ndipo zazitali msinkhu zidzadulidwa; ndipo odzikweza adzatsitsidwa.

34 Ndipo adzadula nkhalango za m’nthengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu.