Malembo Oyera
2 Nefi 33


Mutu 33

Mawu a Nefi ndi oona—Akuchitira umboni za Khristu—Iwo amene amakhulupilira mwa Khristu adzakhulupilira mawu a Nefi, amene adzaime monga mboni pamaso pa bwalo la chiweruzo. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano ine, Nefi, sindingalembe zinthu zonse zimene zidaphunzitsidwa pakati pa anthu anga; kapena sindili wamphamvu m’kalembedwe, monga m’kulankhula; pakuti pamene munthu ayankhula ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, mphamvu ya Mzimu Woyera imanyamula mawuwo ku mitima ya ana a anthu.

2 Koma taonani, alipo ambiri amene aumitsa mitima yawo motsutsana ndi Mzimu Woyera, kuti ulibe malo mwa iwo; kotero, amataya zinthu zambiri zimene zidalembedwa ndi kuzitenga kukhala zinthu zopanda pake.

3 Koma ine, Nefi, ndalemba zomwe ndalemba, ndipo ndaziyesa kukhala ngati zamtengo wapatali, ndipo makamaka kwa anthu anga. Pakuti ndimawapemphelera mosalekeza usana, ndipo maso anga anyowetsa mtsamiro wanga mu usiku chifukwa cha iwo; ndipo ndililira kwa Mulungu wanga ndi chikhulupiliro, ndipo ndikudziwa kuti iye adzamva kulira kwanga.

4 Ndipo ndikudziwa kuti Ambuye Mulungu adzapatura mapemphero anga kuti apindulire anthu anga. Ndipo mawu amene ine ndawalemba mu kufooka adzapangidwa amphamvu kwa iwo; pakuti akuwakopa iwo kuchita zabwino; ndipo amawadziwitsa iwo za makolo awo; ndipo amanena za Yesu, ndi kuwakopa iwo kuti akhulupilire mwa iye, ndi kupilira kufikira chimaliziro, ndiwo moyo wamuyaya.

5 Ndipo amayankhula mwaukali motsutsana ndi tchimo, molingana ndi kumveka kwa choonandi; kotero, palibe munthu adzakwiye pa mawu amene ine ndalemba pokhapokha adzakhale wa mzimu wa mdyerekezi.

6 Ndimalemekeza mu zomveka; ndimalemekeza mu choonadi; ndimalemekeza mwa Yesu wanga, chifukwa adawombola moyo wanga ku gahena.

7 Ndili ndi chikondi pa anthu anga, ndi chikhulupiliro chachikulu mwa Khristu kuti ndidzakumana ndi miyoyo yopanda banga pa mpando wake wa chiweruzo.

8 Ndili ndi chikondi pa Myuda—Ndikunena Myuda, chifukwa ndikutanthauza kwa iwo kumene ndidachokera.

9 Ndilinso ndi chikondi pa Amitundu. Koma taonani, pakuti palibe mmodzi wa awa amene ine ndingathe kuyembekezera kupatula iwo adzayanjanitsidwe kwa Khristu, ndi kulowa mu chipata chopapatiza, ndi kuyenda mu njira yolunjika imene imatsogolera ku moyo, ndi kupitiliza mpaka kumapeto kwa tsiku lakuyesedwa.

10 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndiponso Myuda, ndi inu akumalekezelo a dziko lapansi, mvetserani ku mawu awa ndi kukhulupilira mwa Khristu; ndipo ngati simukhulupilira mawu awa, khulupilirani mwa Khristu. Ndipo ngati mungakhulupilire mwa Khristu mudzakhulupilira mawu awa, pakuti ndi mawu a Khristu, ndipo iye waapereka kwa ine; ndipo amaphunzitsa anthu wonse kuti adzichita zabwino.

11 Ndipo ngati sali mawu a Khristu, weruzani inu—pakuti Khristu adzakuonetsa kwa inu, ndi mphamvu ndi ulemelero waukulu, kuti iwo ndi mawu ake, patsiku lomaliza; ndipo inu ndi ine tidzaima maso ndi maso pabwalo lake lamilandu; ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndidalamulidwa ndi iye kuti ndilembe zinthu izi, posatengela za kufooka kwanga.

12 Ndipo ndikupemphera Atate mu dzina la Khristu kuti ambiri a ife, ngati si tonse, tikathe kupulumuka mu ufumu wake pa tsiku lalikulu ndi lomaliza ilo.

13 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, nonse amene muli a nyumba ya Israeli, ndi inu nonse akumapeto kwa dziko lapansi, ine ndikuyankhula ndi inu ngati mawu a m’modzi ofuula kuchokera m’fumbi: Tsalani bwino mpaka tsiku lalikulu ilo lidzafike.

14 Ndipo inu amene simudzatenga nawo ubwino wa Mulungu, ndi kulemekeza mawu a Ayuda, ndiponso mawu anga, ndi mawu amene adzatuluke mkamwa mwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, taonani, ndikukutsanzikani kwa muyaya, chifukwa mawu awa adzakuweruzaniinu patsiku lomaliza.

15 Pakuti chimene ndikusindikiza pa dziko lapansi, chidzabweretsedwa kwa inu kutsutsana nanu pa bwalo lachiweruzo; pakuti motero Ambuye adandilamula ine, ndipo ine ndikuyenera kumvera. Ameni.

Print