Malembo Oyera
2 Nefi 13


Mutu 13

Yuda ndi Yerusalemu adzalangidwa chifukwa cha kusamvera kwawo—Ambuye achondelera ndi kuweruza anthu awo—Ana aakazi a Ziyoni atembeleredwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha chikunja chawo—Fananitsani Yesaya 3. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo taonani, Ambuye, Ambuye wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu, ndi ku Yuda, mchirikizo ndi ndodo, ndodo yonse ya mkate ndi ndodo yonse ya madzi—

2 Munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo, oweruza, ndi mneneri ndi alauli, ndi akale;

3 Kapitawo wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi mphungu, ndi m’misiri waluso, ndi katswiri polankhula.

4 Ndipo ndidzapereka ana kwa iwo kuti akhale akalonga awo, ndipo makanda adzakhala owalamulira.

5 Ndipo anthu adzapondelezedwa, wina aliyense ndi wina, ndi aliyense ndi mnansi wake; mwana adzadzikuza yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezeka.

6 Pamene munthu adzatenga m’bale wake wa mnyumba ya atate ake, ndipo adzati: Iwe uli ndi zovala, ukhale otilamulira, ndipo kupasuka kumeneku kusabwere pansi pa dzanja lako—

7 Mu tsiku limenelo iye adzalumbira, nati: sindidzakhala mchiritsi; pakuti m’nyumba mwanga mulibe mkate kapena chovala; musandipange ine olamulira wa anthu.

8 Pakuti Yerusalemu wapasuka, ndipo Yuda wagwa, chifukwa cha malilime awo ndi zochita zawo zakhala zotsutsana ndi Ambuye, kuti akwiyitse maso a ulemelero wake.

9 Maonekedwe a nkhope zawo akuchitira umboni motsutsana nawo, ndipo amalengeza uchimo wawo ngati Sodomu, ndipo sangathe kubisa. Tsoka kwa miyoyo yawo, pakuti adadzichitira zoipa paokha.

10 Nenani kwa olungama kuti zilibwino ndi iwo; chifukwa iwo adzadya chipatso cha ntchito zawo.

11 Tsoka kwa oipa, chifukwa adzawonongedwa; pakuti mphotho ya manja awo idzakhala pa iwo.

12 Ndipo anthu anga, ana ndiwo akuwapondereza, ndipo azimayi ndiwo owalamulira iwo. Inu anthu anga, iwo amene akukutsogolerani ndi amene akukulakwitsani ndipo akuwononga njira za mayendedwe anu.

13 Ambuye aimilira kuti adandaule, ndipo ayimilira kuti aweluze anthu.

14 Ambuye adzalowa mu chiweruzo ndi akulu akale a anthu ake, ndi akalonga ake; pakuti inu mwadya munda wampesa ndi zofunkha za aumphawi m’nyumba zanu.

15 Mukutanthauza chiyani inu? Mumaphwanya anthu anga ndi kupera nkhope za osauka, atero Ambuye Mulungu wa makamu.

16 Komanso, Ambuye akuti: chifukwa ana aakazi a Ziyoni akudzikuza, ndi kuyenda atasolora makosi awo ndi maso achipongwe, kuyenda ndi kunyang’ama uko akupita, ndi kuliza zingwinjiri kumapazi awo—

17 N’chifukwa chake Ambuye adzakantha ndi nkhanambo korona wa pamutu pa ana aakazi a Ziyoni, ndipo Ambuye adzaulura magawo awo obisika.

18 Tsiku limeneli Ambuye adzachotsa thamo la zingwinjiri zokometsera zawo ndi zitunga, ndi mphande zozungulira ngati mwezi;

19 Maunyolo, ndi zibangiri, ndi nsalu zophimba kunkhope;

20 Maduku, ndi zokongoletsera za miyendo, ndi malamba akumutu ndi mabotolo a zonunkhira ndi ndolo;

21 Mphete ndi zipini;

22 Ndi zovala zosinthira zapaphwando, ndi zofunda, ndi zimbwi ndi tizipeso;

23 Akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira ndi zophimba nkhope.

24 Ndipo zidzachitika kuti, m’malo mwa fungo lokoma padzakhala fungo lonunkha; ndipo m’malo mwa lamba, chingwe; ndipo m’malo mwa tsitsi labwino, dazi; ndipo m’malo mwa chovala cha papamimba, mpango wachiguduli; zipsera m’malo mwa kukongola.

25 Amuna ako adzagwa ndi lupanga ndipo amphamvu ako mu nkhondo.

26 Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, ndipo adzakhala pansi.