Mutu 21
Tsinde la Jese (Khristu) lidzaweruza m’chilungamo—Chidziwitso cha Mulungu chidzakuta dziko lapansi mu dzaka chikwi—Ambuye adzakwezera mbendera ndi kusonkhanitsa Israeli—Fananitsani Yesaya 11. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo padzatulukira ndodo pa tsinde la Jese, ndipo nthambi idzatuluka kuchokera m’mizu yake.
2 Ndipo mzimu wa Ambuye udzakhala pa iye, mzimu wa wanzeru ndi wa kuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wa chidziwitso ndi wakuopa Ambuye.
3 Ndipo iye adzapangidwa ozindikira mwachangu mu kuopa Ambuye; ndipo sadzaweruza mongoona ndi m’maso ake, kapena kudzudzula mwa kungomva ndi makutu ake.
4 Koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzula ofatsa a dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake, ndipo ndi mpweya wa milomo yake adzapha oipa.
5 Ndipo chilungamo chidzakhala lamba wa mchiuno mwake, ndi kukhulupilika lamba wa impsyo zake.
6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzadzitsogolera.
7 Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadyera pamodzi; ndipo ana awo adzagona pansi limodzi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe.
8 Ndipo mwana woyamwa adzasewera pa una wa mavu, ndipo mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’pfunkha la mphiri.
9 Sizidzavulaza kapena kuwononga m’phiri langa lonse loyera, pakuti dziko lapansi lidzadzala ndi chidziwitso cha Ambuye, monga madzi adzadza nyanja.
10 Ndipo pa tsiku limenelo padzakhala muzu wa Jese, umene udzaima ngati mbendera ya anthu; kwa iyo amitundu adzafunafuna; ndipo popuma pake padzakhala ulemelero.
11 Ndipo padzachitika patsiku limenelo kuti Ambuye adzabwezeranso kachiwiri dzanja lake kulanditsa otsalira a anthu ake amene adatsala kuchokera ku Asiriya, ndi ku Igupto, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinala, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za nyanja.
12 Ndipo iye adzaimikira mbendera maiko, ndipo adzasonkhanitsa opirikitsidwa a Israeli, nadzasonkhanitsa obalalika a Yuda kuchokera ku ngodya zinai za dziko lapansi.
13 Nsanje ya Efraimu idzachoka, ndi adani a Yuda adzadulidwa; Efraimu sadzachitira nsanje Yuda, ndipo Yuda sadzazunza Efraimu.
14 Koma iwo adzaulukira pa mapewa a Afilisti kumadzulo; ndipo adzawawononga iwo a kum’mawa limodzi; adzatambasula dzanja lawo kwa Edomu ndi Moabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera iwo.
15 Ndipo Ambuye adzawononga ndithu lilime la nyanja ya Aigupto; ndipo ndi mphepo yake yamphamvu adzagwedeza dzanja lake pa mtsinje, ndipo adzaukantha mu mitsinje isanu ndi iwiri, nadzaolotsa anthu ovala pansi pouma.
16 Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsalira amene adzasiyidwa, wochokera ku Asiriya, monga momwe zidaliri kwa Israeli m’tsiku limene iwo adatuluka m’dziko la Aigupto.