Malembo Oyera
2 Nefi 23


Mutu 23

Chiwonongeko cha Babulo chikuimilira chiwonongeko pa Kubwera kwachiwiri—Lidzakhala tsiku la mkwiyo ndi kubwenzera—Babulo (dziko lapansi) adzagwa kwa muyaya—Fananitsani Yesaya 13. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Zolemetsa za Babulo, zimene Yesaya mwana wa Amozi adaziona.

2 Kwezani mbendera pa phiri lalitali, kwezani mawu kwa iwo, gwedezani dzanja, kuti alowe m’zipata za akulu.

3 Ine ndalamulira woyeretsedwa anga, ndaitananso a mphamvu anga, pakuti mkwiyo wanga suli pa iwo amene akondwera mu ukulu wanga.

4 Phokoso la unyinji m’mapiri akukhala ngati a mtundu wa anthu waukuru, phokoso loopsya la maufumu a maiko osonkhanitsidwa pamodzi, Ambuye wa Makamu asonkhanitsa makamu a nkhondo.

5 Iwo abwera kuchokera ku dziko lakutari, kuchokera kumalekezero a kumwamba, inde, Ambuye, ndi zida za mkwiyo wake, kuti awononge dziko lonse.

6 Lirani mofuula inu, pakuti tsiku la Ambuye layandikira; lidzafika monga chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvu zonse.

7 N’chifukwa chake manja onse adzalefuka, mtima wa munthu aliyense udzasungunuka;

8 Ndipo adzachita mantha; zowawa ndi masautso zidzawagwira, adzazizwa wina ndi mzake; nkhope zawo zidzakhala ngati malawi a moto.

9 Taonani, tsiku la Ambuye likudza, lankhanza ndi mkwiyo, ndi ukali oopsa, kuti lisandulitse dziko bwinja; ndipo adzawonongamo wochimwa a mmenemo.

10 Pakuti nyenyezi za kumwamba ndi magulu a nyenyezi zake sizidzapereka kuwala kwawo; dzuwa lidzadetsedwa pakutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

11 Ndipo ndidzalanga dziko lapansi chifukwa cha kusaweruzika kwawo, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zawo; ndidzathetsa kudzikweza kwa onyada, ndipo ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsya.

12 Ndipo ndidzapanga munthu wamtengo wapatali kuposa golidi woyengeka, ngakhale anthu woposa golidi wa ku Ofiri.

13 N’chifukwa chake, ndidzagwedeza kumwamba, ndipo dziko lapansi lidzasuntha kuchoka m’malo mwake, mu mkwiyo wa Ambuye wa Makamu, ndipo m’tsiku la mkwiyo wake waukali.

14 Ndipo padzakhala ngati mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa imene palibe munthu oyitola, ndipo adzatembenukira aliyense kwa anthu a mtundu wake, nadzathawira aliyense ku dziko lake.

15 Wonse wodzikweza adzalasidwa; inde, ndipo onse ophatikizana ndi oipa adzagwa ndi lupanga.

16 Ana awo adzatswanyidwa pamaso pawo; nyumba zawo zidzaphwasulidwa ndipo akazi awo adzagwirilidwa.

17 Taonani, ndidzawautsira Amedi kumenyana nawo, amene sadzasamala za siliva ndi golidi, kapena kukondwera naye.

18 Mauta awo adzamphwanya anyamata m’zidutswa; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; maso awo sadzalekelera ana.

19 Ndipo Babulo, ulemelero wa maufumu, kukongola kwa ulemelero wa Akadisi, kudzakhala ngati momwe Mulungu adawononga Sodomu ndi Gomora.

20 Anthu sadzakhalamonso, kapenanso sadzakhalamo m’badwo ndi m’badwo: ngakhale M-arabu sadzamanga hema wake pamenepo; ngakhale abusa sadzamanga khola lawo pamenepo.

21 Koma zilombo za m’chipululu zidzagona pamenepo; ndipo nyumba zawo zidzadzala ndi nyama zonyasa zakukuwa; ndipo akadzidzi adzakhala pamenepo, ndipo atonde adzavina pamenepo.

22 Ndipo mimbulu ya mzisumbu idzalira m’mabwinja a nyumba zawo, ndi ankhandwe m’manyumba awo abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachulukitsidwa. Pakuti ndidzamuwononga msanga; inde, pakuti ndidzachitira anthu anga chifundo, koma oipa adzataika.