Malembo Oyera
2 Nefi 1


Buku Lachiwiri la Nefi

Za nkhani ya imfa ya Lehi. Abale ake a Nefi amuukira iye. Ambuye amuchenjeza Nefi kuti apite m’chipululu. Maulendo ake m’chipululu, ndi zina zotero.

Mutu 1

Lehi alosera za dziko la ufulu—Mbewu yake idzabalalikana ndi kukanthidwa ngati idzakana Oyera wa Israeli—Alimbikitsa ana ake aamuna kuvala chida cha chilungamo. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti ine, Nefi, nditamaliza kuphunzitsa abale anga, atate athu, Lehi, adayankhulanso zinthu zambiri kwa iwo, ndipo adabwereza kwa iwo, zinthu zazikulu zimene Ambuye adawachitira iwo powabweretsa iwo kuchokera m’dziko la Yerusalemu.

2 Ndipo adayankhula kwa iwo zokhudzana ndi kupanduka kwawo pamadzi, ndi zifundo za Mulungu populumutsa miyoyo yawo, kuti iwo sadamezedwe m’nyanja.

3 Ndiponso adayankhula kwa iwo zokhudzana ndi dziko la lonjezano, limene iwo adalandira—m’mene Ambuye adaliri wa chifundo potichenjeza ife kuti tithawe m’dziko la Yerusalemu.

4 Pakuti taonani, iwo adati, ndaona masomphenya, m’mene ndikudziwa kuti Yerusalemu waonongedwa; ndipo tikadakhalabe mu Yerusalemu tikadatha psiti.

5 Koma, adatero iwo, posalabadira za masautso athu, talandira dziko la lonjezano, dziko lomwe liri losankhika kuposa maiko onse; dziko limene Ambuye Mulungu wapangana ndi ine kuti likuyenera kudzakhala dziko la cholowa cha mbewu yanga. Inde, Ambuye walonjeza dziko ili kwa ine, ndi kwa ana anga kwa muyaya, ndiponso onse amene adzatsogozedwa kuchoka m’maiko ena ndi dzanja la Ambuye.

6 Kotero, Ine, Lehi, ndikunenera molingana ndi zintchito za Mzimu umene uli mwa ine, kuti sipadzakhala wina amene adzabwere ku dziko lino pokhapokha atabweretsedwa ndi dzanja la Ambuye.

7 Kotero, dziko ili lapatulidwa kwa iye amene iye adzamubweretse. Ndipo ngati iwo adzamtumikira iye molingana ndi malamulo ake amene iye wapereka, lidzakhala dziko la ufulu kwa iwo; kotero, iwo sadzatengedwa konse ku ukapolo; ngati ndichoncho, zidzakhala chifukwa cha uchimo; pakuti ngati kusaweruzika kudzachuluka, lotembeleredwa lidzakhala dzikolo chifukwa cha iwo, koma kwa olungama lidzadalitsidwa kwa muyaya.

8 Ndipo taonani, Ndi cha nzeru kuti dziko ili lisadziwitsidwe kaye kwa maiko ena; pakuti taonani, maiko ambiri adzakhamukira m’dzikoli, mpaka kuti sipadzakhala malo a cholowa.

9 Kotero, Ine, Lehi, ndalandira lonjezo, kuti pokhapokha ngati iwo amene Ambuye Mulungu adzawatulutsa mu dziko la Yerusalemu adzasunga malamulo ake, iwo adzachita bwino pa nkhope ya dzikoli; ndipo adzabisidwa kwa maiko ena, kuti iwo atenge dzikoli kwa iwo wokha. Ndipo ngati zikhala kuti iwo adzasunga malamulo ake, adzadalitsidwa pa nkhope ya dziko lino, ndipo sipadzakhala wina wakuwazunza iwo, kapena kuwalanda dziko la cholowa chawo; ndipo iwo adzakhalamo motetezeka kwa muyaya.

10 Koma taonani, nthawi ikadzafika yoti iwo adzacheperachepera mukusakhulupilira, atalandira madalitso aakulu kuchokera m’dzanja la Ambuye—pokhala nacho chidziwitso cha chilengedwe cha dziko lapansi, ndi anthu onse, podziwa ntchito zazikulu ndi zodabwitsa za Ambuye kuchokera pa chilengedwe cha dziko lapansi; pokhala ndi mphamvu yopatsidwa kwa iwo yochita zinthu zonse mwa chikhulupiliro; pokhala nawo malamulo onse kuchokera pa chiyambi, ndipo atabweretsedwa ndi ubwino wake opanda malire ku dziko ili la mtengo wapatali la lonjezano—taonani, ndikunena, ngati tsiku lidzafike kuti iwo adzakana Oyera wa Israeli, Mesiya woona, Muwomboli wawo ndi Mulungu wawo, taonani, ziweruzo za iye amene ali wolungama zidzakhala pa iwo.

11 Inde, adzabweretsa maiko ena kwa iwo, ndipo iye adzawapatsa iwo mphamvu, ndipo adzalanda kwa iwo maiko awo, ndipo adzawachititsa iwo kuti abalalike ndi kukanthidwa.

12 Inde, pamene m’badwo umodzi udzapita kwa wina, padzakhala kukhetsa mwazi, ndi kuyenderedwa kwakukulu pakati pawo; kotero, ana anga, ndikufuna kuti mukumbukire; inde, ndikadakonda mudakamvera mawu anga.

13 O kuti mukadadzuka; kudzuka ku tulo tatikulu, inde ngakhale tulo ta ku gahena, ndikugwetsa ma unyolo oyipa amene inu mwamangidwa nawo, amene ali ma unyolo amene amamanga ana a anthu, kuti atengedwere ku ukapolo mpaka ku phompho la muyaya la masautso ndi tsoka.

14 Galamukani! ndi kumuka ku fumbi, ndi kumva mawu akholo lonjenjemera, amene ziwalo zake mukuyenera kugonetsa pansi m’manda ozizira ndi achete, kumene palibe opitako angabwelere; masiku ochepa okha ndipo ine ndikupita njira ya dziko lonse lapansi.

15 Koma taonani, Ambuye awombola moyo wanga ku gahena; ndaona ulemelero wake, ndipo ndazunguliridwa kwa muyaya m’mikono ya chikondi chake.

16 Ndipo ndikukhumbira kuti inu mukumbuke kusunga malamulo ndi ziweruzo za Ambuye; taonani iyi yakhala nkhawa ya moyo wanga kuyambira pa chiyambi.

17 Mtima wanga walemedwa ndi chisoni kuchokera ku nthawi ndi nthawi, pakuti ndidachita mantha, kuti chifukwa cha kuumitsa mitima kwanu Ambuye Mulungu wanu adzabwera ndi chidzalo cha mkwiyo wake pa inu, kuti muchotsedwe ndi kuonongedwa kwa muyaya.

18 Kapena, kuti thembelero lidzabwera kwa inu kwa nthawi ya mibadwo yambiri; ndipo inu mudzayenderedwa ndi lupanga, ndi chilala, ndi kudedwa, ndi kutsogozedwa molingana ndi chifuniro ndi ukapolo wa mdyerekezi.

19 Inu ana anga, kuti zinthu zimenezi zisakugwereni, koma kuti mukhale anthu osankhika ndi okondeledwa a Ambuye. Koma taonani, kufuna kwake kuchitidwe; pakuti njira zake ndi zolungama kwa muyaya.

20 Ndipo iye wanena kuti: Pokhapokha ngati mudzasunga malamulo anga mudzachita bwino m’dziko; koma pokhapokha ngati simudzasunga malamulo anga, mudzadulidwa kuchoka pamaso panga.

21 Ndipo tsopano kuti moyo wanga ukhale ndi chisangalalo mwa inu, ndi kuti mtima wanga uchoke m’dziko lino wokondwa chifukwa cha inu, kuti ndisatsikire ndi kudandaula ndi chisoni kumanda, mukani ku fumbi, ana anga, ndi kukhala anthu, ndipo khalani otsimikizika m’maganizo amodzi ndi mu mtima umodzi, ogwirizana mu zinthu zonse, kuti inu musagwe mu ukapolo.

22 Kuti musatembeleredwe ndi thembelero lowawa; ndiponso, kuti inu musapute mkwiyo wa Mulungu wachilungamo pa inu, mpaka ku chiwonongeko, inde, chiwonongeko cha muyaya cha thupi ndi mzimu.

23 Galamukani, ana anga; valani chida cha chilungamo. Gwetsani maunyolo amene inu mwamangidwa nawo, ndikutuluka mu m’dima, ndi kuuka kufumbi.

24 Musapandukirenso m’bale wanu, amene maganizo ake akhala aulemelero, ndipo amene adasunga malamulo kuchokera ku nthawi yomwe tidachoka ku Yerusalemu; ndipo amene wakhala chida cha m’manja mwa Mulungu, kutibweretsa ife ku dziko la lonjezano; pakuti padakapanda iye, ndibwezi titawonongeka ndi njala m’chipululu; komabe, inu mudafuna kuchotsa moyo wake; inde, ndipo wazunzika m’chisoni chachikulu chifukwa cha inu.

25 Ndipo ndili ndi mantha ndi kunjenjemera kwakukulu chifukwa cha inu, kuti angadzazunzikenso; pakuti taonani, mwamuimba mlandu kuti iye adafuna mphamvu ndi ulamuliro pa inu; koma ndikudziwa kuti iye sadafune mphamvu kapena ulamuliro pa inu, koma iye wafuna ulemelero wa Mulungu; ndi ubwino wanu womwe wamuyaya.

26 Ndipo inu mudang’ung’udza chifukwa iye wanena momveka kwa inu. Mukuti wagwiritsa ntchito kupsa mtima; mukunena kuti iye wakhala okwiya ndi inu; koma taonani, kuthwa kwake kudali kuthwa kwa mphamvu ya mawu a Mulungu, amene adali mwa iye; ndipo umene mukuutcha mkwiyo chidali choonadi, molingana ndi chimene chili mwa Mulungu, chimene iye sakadadziletsa, kukuonetserani inu mopanda mantha zokhudza kusaweruzika kwanu.

27 Ndipo kuyenera kuti mphamvu ya Mulungu ikhale mwa iye, ngakhale kufikira kukulamulani inu kuti mumvere. Koma taonani, sadali iye, koma udali Mzimu wa Ambuye umene udali mwa iye, umene udatsekula pakamwa pake kuti ayankhule mpaka kuti sakadatha kupatseka.

28 Ndipo tsopano mwana wanga, Lamani, ndiponso Lemueli ndi Samu, ndiponso ana anga onse amene muli ana a Ismaeli, taonani, ngati mudzamvera mawu a Nefi simudzawonongeka. Ndipo ngati mumvera kwa iye, ndikukusiyirani inu dalitso, inde ngakhale dalitso langa loyamba.

29 Koma ngati inu simudzamvera kwa iye, ndikutenga mdalitso wanga, inde, ngakhale dalitso langa, ndipo lidzakhala pa iye.

30 Ndipo tsopano, Zoramu, ndikuyankhula ndi iwe: Taona, iwe ndi mdzakazi wa Labani, komabe, iwe wabweretsedwa kuchokera ku dziko la Yerusalemu, ndipo ndikudziwa kuti iwe ndi bwenzi lenileni la mwana wanga, Nefi, kwamuyaya.

31 Kotero, chifukwa wakhala okhulupilika, mbewu yako idzakhala yodalitsidwa ndi mbewu yake, kuti adzakhala akuchita bwino kwa nthawi yayitali pa nkhope ya dziko lino; ndipo palibe, kupatula kusaweruzika pakati pawo, kumene kudzawavulaze kapena kusokoneza kuchita bwino kwawo pa nkhope ya dziko lino kwamuyaya.

32 Kotero, ngati udzasunge malamulo a Ambuye, Ambuye apatula dziko ili kuti likhale chitetezo cha mbewu yako ndi mbewu ya mwana wanga.