Malembo Oyera
2 Nefi 8


Mutu 8

Yakobo apitiliza kuwerenga kuchokera ku Yesaya: M’masiku otsiriza, Ambuye adzatonthoza Ziyoni ndi kusonkhanitsa Israeli—Wowomboledwa adzabwera ku Ziyoni pakati pa chisangalalo chachikulu—Fananizani Yesaya 51 ndi 52:1–2. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Mvetserani ine, inu amene mumatsata chilungamo. Yang’anani ku thanthwe kumene inu munasemedwako, ndipo ku bowo la dzenje kumene inu mwakumbidwa.

2 Yang’anani kwa Abrahamu, kholo lanu, ndi kwa Sarai, amene adakubalani inu; pakuti ndidamuyitana iye yekha, ndi kumudalitsa.

3 Pakuti Ambuye adzatonthoza Ziyoni, adzatothoza mabwinja ake onse; ndipo adzasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi chipululu chake ngati munda wa Ambuye. Chisangalalo ndi kukondwa kudzapezeka m’menemo, mayamiko ndi nyimbo.

4 Mvetserani ine, anthu anga; ndikutchera khutu kwa ine, Iwe pfuko langa; pakuti chilamulo chidzachoka kwa ine ndipo ndidzakhazikitsa chiweruzo changa kukhala kuunika kwa anthu anga.

5 Chilungamo changa chili pafupi; chipulumutso changa chamuka, ndipo nkono wanga udzaweruza anthu. Zilumba zidzandidikira ine, ndipo pa mkono wanga iwo adzakhulupilira.

6 Kwezani maso anu kumwamba, ndi kuyang’ana pansi padziko; pakuti thambo lidzachoka ngati utsi, ndi dziko lapansi lidzatha ngati chovala, ndipo amene akhala m’menemo adzafa chimodzimodzi. Koma chipulumutso changa chidzakhala chosatha ndipo chilungamo changa sichidzathetsedwa.

7 Mvetserani ine, inu amene mumadziwa chilungamo, anthu amene ndalemba chilamulo changa m’mitima mwawo, musaope chitonzo cha anthu, ndipo musaope zonyoza zawo.

8 Pakuti njenjete zidzawadya ngati chovala, ndipo mbozi zidzawadya ngati ubweya. Koma chilungamo changa chidzakhala nthawi zonse, ndi chipulumutso changa ku mibadwo ndi mibadwo.

9 Galamuka, Galamuka! Vala mphamvu, Iwe mkono wa Ambuye: Galamuka ngati m’masiku akale. Kodi sindiwe amene udadula Rehabi, ndi kuvulaza chilombo?

10 Kodi sindiwe amene udaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; amene udasandutsa kuya kwa nyanja yakuya kukhala njira yodutsira wowomboledwa?

11 Kotero, wowomboledwa a Ambuye adzabwelera, ndipo adzafika ndi kuimba ku Ziyoni, ndi chimwemwe chosatha ndipo chiyero chidzakhala pa mitu yawo; ndipo adzakhala ndi chisangalalo ndi kukondwa; chisoni ndi maliro zidzachoka.

12 Ine ndine iye; inde, ndine wakukutonthozani inu. Taonani, ndiwe ndani, kuti udziopa munthu, amene adzafa, ndi mwana wa munthu, amene adzakhala ngati udzu?

13 Ndipo waiwala Ambuye mlengi wako, amene adayala kumwamba, ndi kukhazika maziko a dziko lapansi, nachita mantha masiku onse, chifukwa cha ukali wa opondereza, ngati kuti ali okonzeka kuononga? Ndipo uli kuti ukali wa opondereza?

14 Wam’nsinga otengedwa adzafulumira, kuti amasulidwe, ndipo kuti asadzafe mu dzenje, kapena kuti mkate wake usowa.

15 Koma ine ndine Ambuye Mulungu wako, amene mafunde ake adaomba; Ambuye wamakamu ndiye dzina langa.

16 Ndipo ndaika mawu anga mkamwa mwako, ndipo ndakuphimba iwe ndi chithunzithunzi cha dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndikunena kwa Ziyoni: Taona, inu ndinu anthu anga.

17 Galamuka, galamuka, imilira, Iwe Yerusalemu, amene udamwa pa dzanja la Ambuye chikho cha ukali wake—iwe wamwa zisenga za chikho chonjenjemera chomphwanyika—

18 Ndipo padalibe m’modzi womutsogolera pakati pa ana aamuna onse amene iye adawabala; kapena womgwira pa dzanja, mwa ana onse aamuna amene iye adawabala.

19 Ana aamuna awiri awa abwera kwa iwe, ndani amene adzakumvera iwe chisoni—bwinja lako ndi chiwonongeko, ndi njala, ndi lupanga—ndipo ndi ndani amene ndidzakutonthozela iwe?

20 Ana ako aamuna adakomoka, kupatula awiriwa; agona pamutu pa makwalala onse; monga ng’ombe muukonde, iwo adzadzidwa ndi ukali wa Ambuye, kudzudzula kwa Mulungu wako.

21 Kotero mvera izi tsopano, iwe wasautsidwa ndi kuledzera, ndipo osati ndi vinyo:

22 Akutero Ambuye wako, Ambuye ndi Mulungu wako aweruzira mlandu wa anthu ake; taona, ndachotsa mu dzanja lako chikho chonjenjemera, nsenga ya chikho cha ukali wanga; iwe siudzamwanso kachiwiri.

23 Koma ndichiika mu dzanja la iwo amene asautsa iwe; amene anena ku moyo wako: Welama, kuti ife tidutse—ndipo iwe wagonetsa thupi lako monga pansi ndi monga nsewu kwa iwo amene adadutsa.

24 Galamuka, galamuka, vala mphamvu zako, iwe Ziyoni; vala chovala chako chokongola, iwe Yerusalemu, mzinda oyera; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso mwa iwe osadulidwa ndi wodetsedwa.

25 Dzisatse wekha kufumbi; dzuka, khala pansi, iwe Yerusalemu; udzimasule wekha ku maunyolo apa khosi pako, iwe mwana wamkazi wam’nsinga wa Ziyoni.

Print