Malembo Oyera
2 Nefi 10


Mutu 10

Yakobo afotokoza kuti Ayuda adzampachika Mulungu wawo—Adzamwazikana kufikira atayamba kum’khulupilira iye—Amerika adzakhala dziko la ufulu limene palibe mfumu idzalamulire—Dziyanjanitseni kwa Mulungu ndi kulandira chipulumutso kudzera mu chisomo chake. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, ine, Yakobo, ndikuyankhula kwa inu kachiwiri, abale anga okondedwa, zokhudzana ndi nthambi yolungama imene ndayankhulayi.

2 Pakuti taonani, malonjezano amene ife talandira ndi malonjezano kwa ife molingana ndi thupi; kotero, monga zaonetseredwa kwa ine kuti ambiri mwa ana athu adzaonongedwa mu thupi cifukwa cha kusakhulupilira, komabe, Mulungu adzakhala wa chifundo kwa ambiri; ndipo ana athu adzabwenzeretsedwa, kuti adzabwere ku icho chimene chidzawapatsa iwo chidziwitso choonadi cha Muwomboli wawo.

3 Kotero, monga ndanena kwa inu, kuyenera kukhala koyenera kuti Khristu—pakuti mu usiku wapitawu, mngelo wayankhula nane kuti ili lidzakhala dzina lake—ayenera kubwera pakati pa Ayuda, pakati pa iwo amene ali mbali ya oipa kwambiri ya dziko lapansi; ndipo iwo adzampachika iye—pakuti kuteroko kuli koyenera kwa Mulungu wathu, ndipo palibe mtundu wina pa dziko lapansi umene ungapachike Mulungu wawo.

4 Pakuti ngati zozizwitsa zingachitike pakati pa maiko ena, iwo angalape, ndi kudziwa kuti iye ndi ndi Mulungu wawo.

5 Koma chifukwa cha zaunsembe zolakwika ndi kusaweluzika, iwo aku Yerusalemu adzaumitsa makosi awo kwa iye, kuti apachikidwe.

6 Kotero, chifukwa cha kusaweruzika kwawo, dziwonongeko, njala, mliri, ndi kukhetsa mwazi zidzafika pa iwo; ndipo amene sadzaonongedwa adzamwazikana pakati pa maiko onse.

7 Koma taonani, akutero Ambuye Mulungu: Pamene tsikulo lidzafika limene iwo adzakhulupilira mwa ine, kuti ine ndine Khristu, ndiye ine ndapanga pangano ndi makolo awo kuti iwo adzabwenzeretsedwa mu thupi, pa dziko lapansi, ku maiko a cholowa chawo.

8 Ndipo zidzachitika kuti adzasonkhanitsidwa kuchokera kupa kubalalika kwawo kwanthawi yaitali, kuchokera ku zilumba za nyanja, ndi kuchokera ku zigawo zinayi za dziko lapansi; ndipo maiko a Amitundu adzakhala aakulu pamaso panga, akutero Mulungu, mu kuwatengera iwo kupita ku maiko acholowa chawo.

9 Inde, mafumu a Amitundu adzakhala atate awo owalera, ndipo mfumukazi zawo zidzakhala mayi awo owalera; kotero, malonjezo a Ambuye ndi aakulu kwa Amitundu, pakuti iye wayankhula izi, ndipo ndani angatsutse?

10 Koma taonani, dziko ili, adatelo Mulungu, lidzakhala dziko la cholowa chanu, ndipo Amitundu adzakhala odala padzikolo.

11 Ndipo dziko ili lidzakhla la ufulu kwa Amitundu, ndipo sipadzakhala mafumu pa dzikolo, amene adzaukitsa kwa Amitundu.

12 Ndipo ndidzalimbitsa dziko ili motsutsana ndi maiko ena onse.

13 Ndipo iye amene amenyana ndi Ziyoni adzaonongeka, atero Mulungu.

14 Pakuti iye amene adzadzutsa mfumu motsutsana nane adzaonongedwa, pakuti ine, Ambuye, Mfumu ya kumwamba, ndidzakhala mfumu yawo, ndipo ndidzakhala kuunika kwawo kunthawi zonse, amene amva mawu anga.

15 Kotero, pachifukwa ichi, kuti mapangano anga akwaniritsidwe amene ndidapanga kwa ana a anthu, kuti ndidzawachitira iwo pamene adakali mu thupi, ndikuyenera kuononga ntchito zachinsinsi za mumdima, ndi za akupha ndi za zonyansa.

16 Kotero, iye amene amenyana ndi Ziyoni, onse Ayuda ndi Amitundu, onse akapolo ndi afulu, onse amuna ndi akazi, adzaonongeka; pakuti ndi amene ali achigololo a dziko lapansi, pakuti iwo amene sali kumbali yanga, ali otsutsana nane, atero Mulungu wathu.

17 Pakuti ndidzakwaniritsa malonjezo anga amene ndidapanga kwa ana a anthu, kuti ndidzawachitira iwo pamene adakali mu thupi—

18 Kotero, abale anga okondedwa, atero Mulungu wathu: Ndidzasautsa mbewu yanu ndi dzanja la Amitundu; komabe, ndidzafewetsa mitima ya Amitundu, kuti adzakhale ngati atate kwa iwo; kotero, Amitundu adzadalitsidwa ndi kuwerengedwa pakati pa nyumba ya Israeli.

19 Kotero, ndidzapatula dziko ili kwa mbewu yako, ndi iwo amene adzawerengedwe pamodzi ndi mbewu yako, kunthawi zosatha, kukhala dziko lacholowa chawo; pakuti liri dziko losankhika, atero Mulungu kwa ine, kuposa maiko ena onse, kotero ndidzafuna anthu onse okhala m’menemo kuti adzalambire ine, atero Mulungu.

20 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, poona kuti Mulungu wathu wachifundo watipatsa ife chidziwitso chachikulu chokhudzana ndi zinthu izi, tiyeni timukumbukire iye, ndi kusiya machimo athu, ndipo osagwetsa mitu yathu, pakuti sitili otayidwa; komabe, tathamangitsidwa kuchokera ku dziko la cholowa chathu; koma tatsogozedwa ku dziko labwino, pakuti Ambuye wapanga nyanja njira yathu, ndipo ife tili pa chilumba cha nyanja.

21 Koma aakulu ndiwo malonjezo a Ambuye kwa iwo amene ali pa zilumba za pa nyanja; kotero monga tikunena zilumba, pakuyenera kukhala zambiri kuposa izi, ndipo zimakhalidwanso ndi abale athu.

22 Pakuti taonani, Ambuye Mulungu wapititsa kutali ku nthawi ndi nthawi kuchokera ku nyumba ya Israeli, molingana ndi chifuniro chake komanso kukonda kwake. Ndipo taonani tsopano, Ambuye amakumbukira iwo onse amene adathyoledwa, kotero amatikumbikiranso ife.

23 Pamanepo, kondwelerani mitima yanu, ndipo kumbukirani kuti muli ndi ufulu kudzichitira inu eni—kusankha njira ya imfa yosatha kapena njira ya moyo wamuyaya.

24 Kotero, abale anga okondedwa, dziyanjanitseni nokha ku chifuniro cha Mulungu, ndipo osati ku chifuniro cha mdyerekezi ndi thupi; ndipo kumbukirani, mukayanjanitsidwa ndi Mulungu, kuti ndi kudzera, komanso mwa chisomo cha Mulungu mokha ndimo kuti inu mungapulumutsidwe.

25 Kotero, Mulungu akuutseni inu kwa akufa ndi mphamvu ya chiukitso, ndiponso kuchokera ku imfa yamuyaya ndi mphamvu ya chitetezero, kuti mudzalandilidwe mu ufumu wamuyaya wa Mulungu, kuti mudzamutamande iye kudzera mu chisomo cha umulungu. Ameni.