Malembo Oyera
2 Nefi 12


Mutu 12

Yesaya aona kachisi wa m’masiku otsiriza, kusonkhanitsa kwa Israeli, ndi chiweruzo cha dzaka chikwi ndi mtendere—Odzikweza ndi oipa adzatsitsidwa pa Kubwera Kwachiwiri—Fananitsani Yesaya 2. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Mawu amene Yesaya, mwana wa Amozi, adaona zokhudzana ndi Yuda ndi Yerusalemu.

2 Ndipo zidzachitika masiku omaliza, pamene phiri la nyumba ya Ambuye lidzakhazikika pa mwamba pa mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda, ndi mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.

3 Ndipo anthu ambiri adzapita ndi kunena, Bwerani inu, tiyeni tipite ku phiri la Ambuye, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa ife mayendedwe ake, ndipo ife tidzayenda m’njira zake; pakuti mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Ambuye kuchokera mu Yerusalemu.

4 Ndipo iye adzaweruza pakati pa maiko, ndipo adzadzudzula anthu ambiri: ndipo adzasula malupanga awo kukhala zolimira, ndi mikondo yawo kukhala mbedza—Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

5 Inu nyumba ya Yokobo, bwerani, tiyeni tiyende mu kuwala kwa Ambuye, inde, bwerani, pakuti inu nonse mwasochera, aliyense mu njira zake zoipa.

6 N’chifukwa chake, Inu Ambuye, mwawasiya anthu anu, a nyumba ya Yakobo, chifukwa adzadzidwa ku m’mawa, ndikumvera alauli ngati Afilisti, ndipo adzikondweretsa okha mwa ana a achilendo.

7 Dziko lawonso ladzadza ndi siliva ndi golide, ndipo palibe mathero pa chuma chawo; dziko lawo ladzadza ndi akavalo, ndipo palibe malire pa magaleta awo.

8 Dziko lawo ladzadzanso ndi mafano, amapembedza ntchito za manja awo, zimene zapangidwa ndi dzala dzawo.

9 Ndipo munthu wamba sagwada pansi, ndipo munthu wamkuru sadzichepetsa, kotero musamukhululukire.

10 Inu oipa inu, lowani thanthwe, ndi kubisala m’fumbi, pakuti kuopa Ambuye ndi ulemelero wachifumu wake zidzakukanthani.

11 Ndipo zidzachitika kuti maonekedwe odzikuza a munthu adzatsitsidwa, ndipo kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi, ndipo Ambuye okha adzakwezedwa mu tsikulo.

12 Pakuti tsiku la Ambuye wa makamu lidzafika posachedwa kwa maiko onse, inde, pa aliyense; inde, pa onyada ndi odzikweza, ndipo pa aliyense amene ali otukulidwa adzatsitsidwa.

13 Inde, ndipo tsiku la Ambuye lidzafika pa mitengo yonse yamkungudza waku Lebanoni, pakuti ndi yaitali ndi yotukulidwa; ndi pa mitengo yathundu yonse ya ku Basana;

14 Ndi pamapiri onse aatali, ndi pa zitunda zonse, ndi pa maiko onse amene ali odzikweza, ndi pa anthu onse.

15 Ndi pansanja zonse zitalizitali, ndi pa makoma onse amipanda.

16 Ndi pa ngalawa zonse za pa nyanja, ndi pa ngalawa zonse za Tarisisi, ndi pa zithunzi zonse zokondweretsa.

17 Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, ndi kudzikuza kwa anthu kudzatsitsidwa; ndipo Ambuye okha adzakwezedwa pa tsiku limenelo.

18 Ndipo mafano adzawathetsa psiti.

19 Ndipo adzalowa m’maenje a m’mathanthwe, ndi m’mapanga a m’dziko lapansi, Pakuti mantha a Ambuye adzagwera iwo ndipo ulemelero wa ukulu wake udzawakantha iwo, akadzadzuka kudzagwedeza koopsa dziko lapansi.

20 Mutsikulo munthu adzataya mafano ake a siliva, ndi mafano ake a golide, amene adadzipangira yekha kuti adzipembedza, kwa minyewa ndi kwa mileme.

21 Kuti akalowe m’mapanga a thanthwe, ndi pamwamba pa miyala yogumuka, pakuti mantha a Ambuye adzawagwera iwo, ndi ukulu wa ulemelero wake udzawakantha iwo, akadzadzuka ndi kuwagwedeza koopsya dziko lapansi.

22 Msiyeni munthu amene mpweya wake uli m’phuno mwake, pakuti kodi ndikuti komwe iye adzawerengedwe?